CHIKHULUPILIRO CHA MSILAMU
MUTU 1: CHIKHULUPILIRO CHATHU
Chikhulupiliro chathu ndiko kukhulupilira mwa Allah, Angelo ake, Mabuku ake, Atumiki ake, Tsiku la Chiweruzo, komanso Chikonzero cha zabwino ndi zoipa.
KUKHULUPILIRA UMBUYE WA ALLAH, UMODZI NDI MBIRI ZAKE.
Kumeneku ndiko kukhulupilira kuti Iye ndi Mbuye, Mlengi, Wolamulira komanso Woyendetsa zonse.
Timakhulupilira kuti umulungu wa Allah ndi woona ndipo zina zonse zotchedwa Mulungu ndizabodza.
Timakhulupilira kuti Allah ali ndi Maina abwino kwambiri komanso Mbiri zapamwamba zedi.
Timakhulupilira kuti Iye ndi mmodzi ndipo alibe ofanana naye mu umulungu wake, m’maina ake ndi mumbiri zake. Allah akunena mu Qur’an Yolemekezeka: “Mbuye wathambo ndi nthaka ndi zapakati paizo: Choncho mpembedze iye basi. Ndipo pitiriza ndikupilira popembedza iye. Kodi ukumudziwa [wina] yemwe ali wofanana naye [Allah]?” [19:65]
Timakhulupilira kuti iye ndi “Allah, palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo, Wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chilichonse. Kusinza sikum’gwira ngakhale tulo. Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Iye. Kodi ndani angathe kuombola kwa Iye popanda chilolezo chake? Akudziwa zapatsogolo ndi zomwe zili pambuyo pawo ndipo zolengedwazo sizidziwa chilichonse pa zomwe zili m’kudziwa kwake kupatula chimene wafuna. Arsh [Kama Yachifumu Yaikulu] yake yakwanira kumwamba ndi pansi ndipo sizimam’vuta kuzisunga zimenezo. Ndipo Iye [yekha] njemwe ali Wapamwambamwamba, Ngwamkulu kwabasi, [Ngolemekezeka kwambiri].” [2:255]
Timakhulupilira kuti “Iye ndi Allah, amene palibenso wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, wodziwa zam’seri ndi zooneka. Iye Ngwachifundo Chambiri ndiponso Ngwachisoni Chosatha. Iye ndi Allah, amene palibenso wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, Mwini chilichonse, Woyera, mwini mtendere, Wotsimikizira [Aneneri ake mphamvu yochitira zozizwitswa,] Msungi wa chilichonse [yemwe akuona zochita za akapolo ake]; Wamphamvu zopambana, Mgonjetsi wotukuka mu ulemelero; Wamkulukulu.Wapatukana kuzimene akumuphatikiza nazo. Iye ndi Allah; Mlengi [wazinthu, palibe chom’fanizira]; Muwumbi wa chilichonse. Mkonzi wa maonekedwe a zinthu, ake ndi maina abwino, zonse zakumwamba ndipansi zikum’lemekeza Iye ndikum’yeretsa kumakhalidwe osayenerana ndi ulemelero wake. Iye Ngopambana ndiponso Ngwanzeru zakuya”. [59:22-4]
Timakhulupilira kuti “Ufumu wakumwamba ndi padziko lapansi ngwa Allah; amalenga zimene wafuna; amene wam’funa amam’patsa ana achikazi ndiponso amene wam’funa amam’patsa ana achimuna. Kapena kuphatikiza [ana] achimuna ndi achikazi [kupereka kwamunthu mmodzi], ndipo amene wam’funa amam’chita kukhala chumba. Ndithu, Iye Ngodziwa; Wokhoza [chilichonse]” [42:49-50]
Timakhulupilira kuti “Palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona zonse. Makiyi akumwamba ndi pansi ndiake. Amam’chulukitsira rizq amene wam’funa ndipo amam’chepetsera amene wam’funa. Ndithu, Iye Ngodziwa chilichonse [pochiika pamalo oyenerana nacho].” [42:11-12]
Timakhulupilira kuti “Ndipo palibe nyama iliyonse [cholengedwa chilichonse] panthaka koma rizq lake lili kwa Allah; Ndipo [Iye] akudziwa mbuto yake yamuyaya ndi mbuto yake yakungodutsapo [yomwe ndi pano padziko lapansi]. Zonse zili m’buku lofotokoza chilichonse.” [11: 6]
Timakhulupilira kuti “Ndipo Iye [Allah] ali nawo makiyi azobisika palibe akuwadziwa koma Iye basi. Ndipo akudziwa zapamtunda ndi zapanyanja. Ndipo palibe tsamba limene limagwa koma amalidziwa. Ndipo [siigwa] njere mumdima wam’nthaka [koma iye akudziwa]. Ndipo [sichigwa] chachiwisi ngakhale chouma, koma chili m’Buku loonetsa chilichonse.” [6:59]
Timakhulupilira kuti “Ndithu, kudziwa kwa nthawi [yakutha kwa dziko] kuli ndi Allah [yekha]. Iye ndiamene amavumbwitsa mvula [nthawi imene wafuna]; ndipo akudziwa zimene zili m’ziberekero [mwa zolengedwa zake: zachimuna kapena zachikazi]. Ndipo aliyense sadziwa chomwe apeze mawa; [chabwino kapena choipa]; ndiponso sadziwa aliyense kuti ndidziko liti adzafera. Ndithu, Allah Ngodziwa ndiponso Ngodzindikira mmene zinthu zilili.” [31:34]
Timakhulupilira kuti Allah amayankhula zomwe wafuna nthawi iliyonse yomwe wafuna: “ndipo Allah adayankhula ndi Musa mwachindunji.” [4:164]; “Pamene Musa adafika kumalo achipangano chathucho, ndipo Mbuye wake namulankhula” [7:143]; “Ndipo tidamuitana kumbali yakudzanjadzanja la phiri la Turi, ndipo tidamuyandikitsa ndi kuyankhula nafe momunong’oneza.” [19:52]
Timakhulupilira kuti “Ngakhale nyanja ikadakhala inki yolembera mawu a Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha mawu a Mbuye wanga asadathe, ngakhale tikadabweretsa nyanja ina ndikuionjezera pa iyo [nyanjazo zikadatha, Mawu a Allah akalipobe]”. “[18:109]; “Ndipo ndithu, ngakhale mitengo yonse ili mnthaka ikadakhala zolembera, ndipo nyanja [nkukhala inki], ndikuyionjezeranso [madzi ake] ndi nyanja zisanu ndi ziwiri, Mawu a Allah sakadatha. Ndithu, Allah Ngwamphamvu, Ngwanzeru zakuya.” [31:27].
Timakhulupilira kuti Mawu a Allah ndi owona koposa pofalitsa uthenga, ndipo ndiabwino komanso achilungamo; “Ndipo mawu a Mbuye wako akwanira moona ndi mwachilungamo. Palibe amene angathe kusintha mawu ake. Iye Ngwakumva, Ngodziwa.” [6:115]; “Kodi ndi mawu andani angakhale oona kuposa a Allah?” [4:87].
Timakhulupilira kuti Qur’an ndi Mawu a Allah. Anayankhula kwa Mngelo Jibril alaih salaam yemwe anawatumiza kwa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam: “Nena [iwe Muhammad]: “Mzimu woyera [Jibril] waitsitsa [Qur’an Yolemekezeka] kuchokera kwa Mbuye wako mwachoonadi” [16:102]; “Ndipo, ndithu iyi [Qur’an] ndiyo chivumbulutso cha Mbuye wazolengedwa zonse. Mzimu wokhulupilika [Jibril] udaivumbulutsa pamtima wako kuti ukhale mmodzi wa achenjezi, m’chilankhulo cha Chiarabu chomveka bwino.”[26:192-95]
Timakhulupilira kuti Allah ndiwapamwamba pa zolengedwa zonse, chifukwa iye akunena kuti: “Ndipo Iye [Yekha] njemwe ali Wapamwambamwamba, Ngwamkulu kwabasi, [Ngolemekezeka kwambiri]” [2:255]; “Iye ndi Mgonjetsi pa anthu ake [onse]; Iye Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa nkhani zonse.” [6:18]
Timakhulupilira kuti “Ndithu, Mbuye wanu ndi Allah amene adalenga thambo ndi nthaka [ndi zonse zam’menemo] m’masiku asanu ndi limodzi; [masiku omwe palibe yemwe akuwadziwa kutalika kwake koma Iye yekha], kenako adakhazikika pampando wake wachifumu [kukhazikika kwake akukudziwa ndi Iye yekha basi], Amayendetsa zinthu [za zolengedwa zake.]” [10:3].
Timakhulupilira kuti Iye samazisiya zolengedwa zake nthawi zonse pamene ali pampando wake; amadziwa mmene zolengedwa zake ziliri, amamva zoyankhula zawo, amaona zomwe akuchita komanso amayendetsa zinthu zawo. Amapereka kwa aliyense osauka ngakhale olemera. Amapereka komanso amatenga ulemelero kwa yemwe wam’funa; amam’kweza ndipo amamusitsa yemwe wam’funa. Ali ndi zabwino zonse ndipo Iye ndi wamphamvu pa chilichonse. Palibe yemwe angakhale ndi mbiri zimenezi zofanana ndi za Allah “palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona zonse.” [42:11]. Ife sitimakhulupilira monga mmene ena amanenera kuti Allah ali pamodzi ndi zolengedwa zake mthupi padziko lapansi, ndipo aliyense yemwe amakhulupilira zimenezi timamutenga kuti ndi okanira komanso osokera chifukwa wam’panga Allah kukhala wopunguka.
Timakhulupilira zomwe Mtumiki anatiuza kuti Allah amatsika pathambo loyandikira usiku uliwonse ndipo amanena kuti “ndani yemwe akupempha ndimuyankhe? Ndani yemwe akupempha chikhululuko ndimukhululukire?” [Al Bukhari & Muslim].
Timakhulupilira kuti Allah adzabwera Tsiku la Chiweruzo kudzaweruza pakati pa anthu chifukwa anati: “Sichoncho! [Siyani machitidwe amenewa]; nthaka ikadzapondedwapondedwa [ndikuifafaniza], adzabwera Mbuye wako [m’mabweredwe omwe akuwadziwa iye mwini] ndipo Angero ali mmizere yondondozana. Basi tsiku limenelo idzabweretsedwa Jahannam, pa tsiku limenelo munthu adzakumbukira, koma kukumbuka kumeneko kudzam’thandiza chiyani?” [89:21-23]
CHIFUNIRO CHA ALLAH
Timakhulupilira kuti Chifuniro cha Allah chili m’mitundu iwiri:
a] Chifuniro pa chilichonse: Umu ndimmene amachitira zofuna zake zabwino ngakhale zoipa. Chifuniro ichi kutanthauza kuti amapereka chilolezo pazilizonse zomwe zingachitike; zabwino ngakhale zoipa, zokondedwa ngakhale zosakondedwa, monga mmene akunenera: “Ndipo Allah akadafuna, sakadamenyana; koma Allah amachita zimene akufuna.” [2:253] komanso “ngati Allah akufuna kukulekelerani kusokera, Iye ndiye Mbuye wanu. Ndipo kwa Iye mudzabwezedwa” [11:34].
b] Chifuniro cha pa Chipembedzo: Chifuniro ichi ndi cha zomwe akuzikonda, monga momwe akunenera “Ndiponso Allah akufuna kukufewetserani” [4:27].
Timakhulupilira kuti Chifuniro chake pa chinthu chilichonse komanso pa Chipembedzo, ndi mbali ya nzeru zake. Chilichonse chomwe amapanga muzifuniro ziwirizi, zimakhala ndi zifukwa zokwanira malinga ndi nzeru zake ngakhale tifune kapena tisafune. “Kodi Allah si Muweruzi wanzeru kuposa aweruzi onse?” [95:8]; “Kodi ndani ali wabwino polamula koposa Allah? [Izi nzodziwika] kwa anthu otsimikiza [kuti Allah alipo].” [5:50].
Timakhulupilira kuti Allah amakonda akapolo ake osankhika ndipo kuti iwo amamukonda “Nena: [iwe Mtumiki] “Ngati inu mukum’konda Allah, tsatani ine; Allah akukondani” [3:31]; “Ndiye kuti posachedwapa Allah Adzabweretsa anthu omwe awakonda, nawonso amkonda;” [5:54]; “Ndipo Allah amakonda opilira.” [3:146]; “ndipo chitani Chilungamo; ndithu, Allah amakonda ochita chilungamo.” [49:9]; “Ndipo chitani zabwino. Ndipo Allah, amakonda ochita zabwino.” [5:93].
Timakhulupilira kuti Allah amakonda zomwe analamula muntchito komanso zoyankhula zabwino, ndipo amadana ndi zomwe analetsa mu ntchito komanso zoyankhula zoipa “Ngati mukana ndithu, Allah Ngodzikwaniritsa sasaukira kwa inu [Chikhulupiliro chanu ndi kuthokoza kwanu]; koma sakonda kukanira kwa anthu ake. Ngati mum’thokoza [pa mtendere Wake umene uli painu] akuyanja kuthokoza kwanuko.” [39:7]; “koma Allah sadafune kuti iwo apiteko; Choncho adawatsekereza, ndipo kudanenedwa: “Khalani pamodzi ndi otsalira.” [9:46]
Timakhulupilira kuti Allah amakonda okhulupilira mwaiye komanso akuchita zabwino “Allah adzalandira ntchito zawo nawonso adzayamika zabwino zake ndi kukondweretsedwa nazo [zomwe adzawapatse]; zimenezo ndi zayemwe awope Mbuye wake [Allah].” [98:8]
Timakhulupilira kuti Allah amakwiyira omwe akuyenera kuwakwiyira mwa anthu okanira ndi ena: “achimuna ndi achikazi oganizira Allah maganizo achabe. Kutembenuka koipa kuli kwaiwo ndipo Allah wawakwiyira.” [48:6]; “koma amene akutsekulira mtima wake kusakhulupilira, mkwiyo wa Allah uli paiwo [ndipo anthu otere] adzapata chilango chachikulu.” [16:106].
MBIRI ZINA ZA ALLAH
Timakhulupilira kuti Allah ali ndi Nkhope Yolemekezeka [maonekedwe ake akuwadziwa ndi Iye mwini, palibe chofanana naye] “Ndipo idzatsala nkhope ya Mbuye wako Mwini ulemelero ndi mtendere;” [55:27]
Timakhulupilira kuti Allah ali ndi Manja awiri opatsa: “Koma manja ake [a Allah] Ngotambasuka. Amapatsa mmene wafunira.” [5:64]; “Koma sadam’lemekeze Allah, kulemekeza koyenerana naye, pomwe patsiku la Qiyaamah nthaka yonse [idzakhala], chofumbata chake mmanja; ndipo thambo lidzakulungidwa ndi dzanja lake lamanja. Walemekezeka Allah. Ndipo watukuka kuzimene akumphatikiza nazozi.” [39:67]
Timakhulupilira kuti Allah ali ndi maso awiri, [maonekedwe ake akuwadziwa ndi Iye mwini, palibe chofanana naye] chifukwa anati: “Ndipo khoma chombo moyang’aniridwa ndi Ife, ndi ulangizi wathu [saatha kukuchitira choipa]” [11:37]. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Chotchinga chake ndikuwala; ndipo atati achichotse, kuwala kwankhope yake yolemekezeka kungawotche chilichonse chomwe chingafikire maso ake” [Muslim & Ibn Maajah]. Anthu otsata chiphunzitso cha Mtumiki (Ahlu Sunnah) anagwirizana zoti Allah ali ndi maso awiri, kuchokera pa mawu a Mtumiki salla Allah alaih wasallama pamene amalongosola za Dajjal “Dajjal ali ndi diso limodzi koma Mbuye wanu si wadiso limodzi” [Al Bukhari & Muslim].
Timakhulupilira kuti “Maso samufika [kuti nkumuona]; koma Iye amawafika maso [amawaona pamodzi ndi eni masowo]. Iye Ngodziwa zobisika kwambiri ndi zoonekera.” [6:103].
Timakhulupilira kuti okhulupilira adzamuona Mbuye wawo Tsiku Lowukitsidwa: “Nkhope zina tsiku limenelo zidzawala kwambiri [ndi Mtendere], zili kumuyang’ana Mbuye wawo” [75:22-3].
Timakhulupilira kuti Allah alibe ofanana naye chifukwa Mbiri zake ndizokwanira “palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona Zonse.” [42:11]
Timakhulupilira kuti “Kusinza sikum’gwira ngakhale tulo” [2:255] chifukwa Moyo wake ndiwokwanira komanso wosatha.
Timakhulupilira kuti Iye samam’mana aliyense chilungamo chake chifukwa chilungamo chake ndichokwanira pa aliyense.
Timakhulupilira kuti Iye amadziwa ntchito za akapolo ake, chifukwa kuyang’anira kwake ndikokwanira komanso ngodziwa kalikonse.
Timakhulupilira kuti Iye ndi ngwakutha kuchita chilichonse kumwamba ndi pansi, chifukwa cha kukwanira kwa nzeru ndi mphamvu zake: “Ndithu, machitidwe ake akafuna kuti chinthu chichitike, amangonena kwa icho: “Chitika!” Ndipo chimachitika [nthawi yomweyo].” [36:82]
Timakhulupilira kuti Iye satopa ngakhale kufooka, chifukwa cha Mphamvu zake zosatha: “Ndithu, tidalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo sikudatikhuze kutopa kulikonse” [50:38]
KUMULONGOSOLA ALLAH KUDZERA
MU CHIVUMBULUTSO CHAKE
Timakhulupilira zonse zomwe anadzitchulira iye mwini, komanso zomwe Mtumiki wake anafotokoza, monga Maina ndi Mbiri zake. Koma timakana mfundo ziwiri:
1) Kunena kapena kukhulupulira kuti mbiri za Allah ndi chimodzimodzi za zolengedwa zake.
2) Kunena kapena kukhulupilira kuti mbiri za Allah zili ngati zakutizakuti.
Timatsutsa zonse zomwe anazitsutsa mwini wake pa Iye, komanso zomwe Mtumiki wake anazitsutsa pa Iye.
Timakhulupilira kuti kutsutsa mbiri zoipa ndiko kutsimikiza kwathunthu pazinthu zabwino. Sitimalongosola zomwe Iye kapena Mtumiki wake sadanene zokhunza Iye Allah.
Timakhulupilira kuti kutsatira izi ndikoyenera, chifukwa zimene Allah adatsimikizira kapena kuzitsutsa mumbiri zake, ndizochokera mmawu ake. Iye amazidziwa bwino yekha, mawu ake ali olungama ndi odalirika ndipo anthu sangathe kudziwa chilichonse cha Iye. Zomwe Mtumiki wa Allah adatsimikiza kapena kutsutsa zokhudza Allah, ndizomwe iye adayankhula. Kuwonjezera pakudziwa kuti Allah ndi Wopambana kuposa wina aliyense, Iye ndiwoona kuposa aliyense, komanso woyankhula zoona kwa anthu. Choncho, zomwe Allah ndi Mtumiki wake adanena zokhudza Maina ake ndi Mbiri zake, ndizoonadi; anatidziwitsa ndi kutifotokozera. Choncho ife tilibe kuwiringula kulikonse pa zimenezi.
***
MUTU 2: QUR’AN NDI SUNNAH:
(momwe mbiri zake zikuchokera)
Zonse zomwe tanena pa mbiri za Allah kaya mwachidule kapena mwatsatanetsatane, zimachokera m’Buku la Mbuye wathu komanso m’Sunnah za Mtumiki wake. Zikugwirizananso ndi chikhalidwe cha mibadwo ya Asilamu olungama omwe anapita komanso omwe adadza pambuyo pawo.
Timakana chizolowezi cha iwo omwe adapotoza tanthauzo la malembawa ndikuwamvetsa mwanjira ina.
Timakaniranso chizolowezi cha iwo amene adawapanga malembawa kukhala opanda tanthauzo monga mmene adatumiziridwa ndi Allah ndi Mtumiki wake. Potsiriza, timakana za awo omwe adawonjezera ndikupereka matanthauzo womchita Allah kukhala wofanana ndi zina mwa zolengedwa zake.
MAWU AKE NDI OPANDA KUTSUTSANA
Ife tikudziwa motsimikiza kuti zomwe zavumbulutsidwa mu Buku la Allah ndi Sunnah za Mtumiki wake ndizoonadi. Mulibemo kutsutsana kulikonse: “Kodi bwanji sakuiganizira Qur’an? Ndipo ikadakhala kuti siikuchokera kwa Allah, ndithudi, mmenemo akadapeza kusiyana kwambiri, [mukadapezeka mawu otsutsana; koma Qur’an siili choncho].” [4:82]
Kutsutsana muzoyankhula kumapangitsa kuti zikhale zonama. Choncho ndizosatheka kuti muzoyankhula zomwe zinavumbulutsidwa ndi Allah komanso Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam mupezekemo kutsutsana. Aliyense yemwe amakhulupilira zoti mu Qur’an komanso mu Sunnah za Mtumiki muli zotsutsana, ali ndi zolinga zoipa komanso ndi wosokera. Woteroyo afunika kulapa ndikusiya tchimo lakelo. Ngati wina wake angakhulupilire zimenezi, ndiye kuti kuzindikira kwake ndikochepa, ndipo akuyenera kufunafuna maphunziro kuti azindikire choonadi. Ndipo ngati sakukwanitsabe kuzindikira choona, azisiye mmanja mwa Allah yemwe ndi Wodziwa zonse ndipo asiye kuganizira koipa koma azichita zomwe ozindikira akuchita.
Ife timakhulupilira zonse zomwe zachokera kwa Mbuye wathu: “Iye ndi Yemwe wakuvumbulutsira Buku [ili la Qur’an], lomwe mkati mwake muli ndime zomveka zomwe ndimaziko a Bukuli. Ndipo zilipo zina zokuluwika. Koma amene m’mitima mwawo muli kusokera, akutsata zomwe zili zokuluwika ndicholinga chofuna kusokoneza anthu, ndi kufuna kudziwa tanthauzo lake lenileni, palibe amene akudziwa tanthauzo lake lenileni koma Allah basi. Koma amene azama pamaphunziro, amanena: “Tawakhulupilira [ma aya amenewa]. Onse ngochokera kwa Mbuye wathu,” Ndipo palibe angakumbukire koma eni nzeru basi. “[3:7]. Akuyenera kudziwa kuti mu Qur’an ndi Sunnah, komanso pakati pa zinthu ziwirizi palibe kutsutsana.
***
MUTU 3: KUKHULUPILIRA ANGELO
Timakhulupilira kupezeka kwa Angelo a Allah omwe ndi zolengedwa zake zolemekezeka: “sadzalankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi Wachifundo Chambiri [kulankhula] ndipo adzanena zolondola. “ [78:38]. Allah ndiyemwe anawalenga ndipo amamupembedza ndikumumvera: “Onse akumwamba ndi pansi, ngake [Allah]; ndipo amene ali kwa Iye [Angelo], sadzitukumula pakumulambira, ndiponso satopa [ndi mapemphero]” [21:19]. Angelo ndi obisika kwaife ndipo sitingawaone, koma Allah amamuonetsa yemwe wam’funa mwa akapolo ake ena. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anamuona Mngelo Jibril m’maonekedwe ake enieni; anali ndi mapiko 600 omwe anakwanira mbali zonse [Al-Bukhari ndi Muslim]. Jibril alaih salaam anatenga maonekedwe amunthu pamene anamuwonekera Mariam alaiha salaam. Komanso anamudzera panthawi imene anali ndi ma Swahaba, mmaonekedwe a munthu wosadziwika yemwe amaoneka ngati anali pa ulendo, atavala zoyera kwambiri ndipo anali ndi tsitsi lakuda kwambiri. Anakhala moyang’anizana ndi Mtumiki ndipo anaika manja ake pa maondo a Mtumiki ndikuyamba kumuyankhula. Kenako Mtumiki anawauza ma Swahaba ake kuti munthu ameneyo anali Jibril [Al-Bukhari ndi Muslim].
TCHITO ZA ANGELO
Timakhulupilira kuti Angelo anapatsidwa ntchito zosiyanasiyana. Ena mwa Angelowo ndi Jibril yemwe anapatsidwa ntchito yovumbulutsa mau kuchokera kwa Allah. Iye amapititsa mau kwayemwe Allah wam’funa mwa Atumiki ndi Aneneri ake.
Komanso wina mwa Angelowo ndi Mikail, yemwe amagwira ntchito yogwetsa mvula komanso kumeretsa mmera.
Israfil ndiyemwe adzaimbe lipenga lakumwalira ndi kuuka.
Wina mwa Angelo ndiyemwe amayang’anira mapiri; komanso pali Mngelo wina dzina lake Malik, yemwe amayang’anira Moto.
Angelo ena amayang’anira mimba komanso ana ofunika kubadwa. Ena amagwira ntchito yoteteza anthu ndipo ena amalembera ntchito za anthu. Munthu aliyense ali ndi Angelo awiri: “Palibe chilichonse chimene amayankhula koma pafupi ndi iye pali mlonda amene wakonzekera [kulemba]” [58:18]. Angelo ena ntchito yawo ndi kufunsa munthu yemwe wamwalira, pambuyo pa kuikidwa mmanda. Angelo awiri amabwera kwa iye kudzamufunsa za Mbuye wake, Chipembedzo chake ndi Mtumiki wake. “Allah amawalimbikitsa amene akhulupilira ndimawu olimba m’moyo wadziko lapansi, ndi moyo wapambuyo pa imfa; ndipo Allah amawalekelera kusokera omwe akudzichitira okha zoipa; ndipo Allah amachita zimene wafuna.” [14:27]. Angelo ena amalondera anthu a ku Jannah: “[Uku akunena] “Salaamun Alayikam [Mtendere uli painu] chifukwa chakupilira kwanu [pochita zabwino ndi kusiya zoipa ndi kukhala mwaubwino ndi anzanu]! Taona kukhala bwino kwazotsatira za nyumba ya tsiku la chimaliziro.” [13:24]. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anatiuza kuti: “Angelo 70 thousand amalowa tsiku lirilonse mu mzikiti wolemekezeka wakumwamba nkumapemphera, [ndipo omwe alowa tsiku limenelo sadzatuluka mpaka tsiku la Qiyaamah], chimodzimodzi omwe adzalowe mawa lake.” [Al-Bukhari ndi Muslim]
***
MUTU 4: KUKHULUPILIRA MABUKU A ALLAH
Timakhulupilira kuti Allah Ta’aala anatsitsa mabuku kwa Atumiki ake kudzakhala umboni komanso chiwongoko kwa anthu. Iwo anayeretsa chikhulupiliro chawo ndikuphunzitsa kuchokera m’mabuku amenewa.
“Ndithu, tidatuma Aneneri athu pamodzi ndi zozizwitsa. Ndipo Tidavumbulutsa pamodzi ndi iwo mabuku ndi muyeso wa choonadi kuti anthu achite chilungamo.” [57:25]
MABUKU ODZIWIKA NDI AWA:
1) Taurat [Torah]: Limene linatumizidwa kwa Musa Mtendere ukhale pa iye. Limeneli ndi buku lalikulu kwa ana a Israel: “Ndithudi, tidaivumbulutsa Taurat yokhala ndi chiongoko ndi kuwunika; Aneneri [a Allah] omwe adagonjera Allah, adali kulamulira nayo Ayuda, ndiponso Arabbaniyuna [aphunzitsi amalamulo] ndi Ahabaru [ansembe] omwe adapemphedwa kusunga Buku la Allah ndipo iwo adali mboni pa ilo, choncho [inu Asilamu] musaope anthu, koma opani Ine.”5:44
2) Injeel: Limeneli linatumizidwa kwa Yesu Mtendere ukhale pa iye. Injeel ndi chikwaniritso cha Tauraat komanso chitsimikizo chake: “Ndipo tidatsatiza pamapazi a Aneneriwo, Isa [Yesu] mwana wa Mariam kudzatsimikizira zomwe zidali patsogolo pake m’Buku la Taurat. Ndipo tidampatsa Injeel yomwe mkati mwake muli chiwongoko ndi kuwunika; ndikutsimikizira zomwe zidali patsogolo pake za m’Buku la Taurat. Ndipo ndi chiwongoko ndi ulaliki wabwino kwa oopa [Allah].” [5:46]; “Ndipo ndadza kuti ndikulolezeni zina mwa zomwe zidaletsedwa kwa inu” [3:50].
3) Zauri [Masalimo]: Limeneli ndi buku lomwe Allah anatumiza kwa Davide Mtendere ukhale pa iye.
4) Mabuku a Ibrahim ndi Musa Mtendere ukhale pa iwo.
5) Qur’an Yolemekezeka: Limeneli ndi Buku lomwe linatumizidwa kwa Mtumiki womaliza Muhammad Mtendere ndi Madalitso zipite kwa iye. Limeneli ndi “chiwongoko kwa anthu ndi zizindikiro zoonekera poyera zachiongoko. Ndikutinso ikhale cholekanitsa [pakati pa choonadi ndi chabodza]” [2:185]. Qur’an ndiyotetezedwa ku kusintha kulikonse. Qur’an ikutsimikiza zamabuku onse omwe anadza m’mbuyo mwake ndipo ndi mlowammalo wa mabuku onsewo. Izi zikutanthauza kuti Allah anachotsa mabuku onse omwe anadza m’badwo uno usanadze, ndikuika Qur’an kukhala yokwanira mmalo mwa mabuku onsewo. Allah watsimikiza kuti adzaiteteza Qur’an kuzoipa zonse komanso kuzosokoneza zilizonse: “Ndithu, Ife ndife omwe tavumbulutsa Qur’an, ndipo ndithudi, tiisunga.” [15:9], Ichi nchifukwa Qur’an ndi umboni wa munthu mpaka tsiku la Chiweruziro.
MABUKU AKALE ANASINTHIDWA
Mabuku akale omwe anadza Qur’an isanadze, anali akanthawi kochepa, ntchito yawo inatha pambuyo pa kutsika Qur’an yomwe inadza ndikuwonetsa poyera kusokonezeka kwawo [komwe anthu anawasokoneza]. N’chifukwa chake Qur’an ili yotetezedwa ku chinyengo chilichonse. Mabuku enawo anawonjezeredwa, kupungulidwa ndikusokonezedwa: “Mwa Ayuda alipo omwe amasintha mawu kuwachotsa m’malo mwake.” [4:46]
“Chilango chaukali chidzatsimikizika pa amene akulemba buku ndimanja awo, kenako nanena: “Ili lachokera kwa Allah,” [akunena bodzalo] kuti apeze zinthu zamtengo wochepa [za m’dziko lapansi]: Kuonongeka kuli paiwo chifukwa chazomwe manja awo alemba, ndipo kuonongeka n’kwawo chifukwa chazomwe adapeza.” [2:79]
“Nena: “Kodi ndani adavumbulutsa Buku lomwe lidadza ndi Musa? Lomwe lidali kuwunika ndi chiwongoko kwa anthu, lomwe mwalichita kukhala zigawozigawo; zimene mwafuna kuwonetsa kwa anthu mukuziwonetsa, koma zambiri mukubisa [zomwe
sizigwirizana ndi zofuna zanu].” [6:91]
“Ndipo ndithu mwaiwo muli gulu lomwe likukhotetsa malirime awo [powerenga] buku kuti muwaganizire [mawu awowo] kuti ndi a m’Buku la Allah]; pomwe si a m’ Buku [la Allah]. Ndipo akunena: “Izi zachokera kwa Allah,” Pomwe zimenezo sizinachokere kwa Allah; Ndipo akum’namizira Allah uku akudziwa. Sikoyenera kwa munthu yemwe Allah wam’patsa Buku ndi chiweruzo ndi uneneri, kenako nanena kwa anthu: “Khalani opembedza ine, mmalo mwa Allah.” [3:78-79].
“E inu anthu a Buku! Ndithudi wakufikani Mtumiki wathu yemwe akukufotokozerani poyera zambiri zomwe munkabisa za m’buku. Koma akusiya zambiri [posazilongosola]. Ndithudi kwakudzerani kuwunika kochokera kwa Allah ndi Buku lomwe likufotokoza mwatchutchutchu [chinthu chilichonse]. Ndibukulo Allah akuwatsogolera kunjira zamtendere amene akutsata chiyanjano chake ndikuwatulutsa mumdima ndikuwaika mukuwunika mwalamulo lake, ndi kuwatsogolera kunjira yoongoka.” [5:15-16]
MUTU 5: KUKHULUPILIRA MWA ATUMIKI
Timakhulupilira kuti Allah anatumiza Atumiki kwa anthu ake, omwe: “adauza nkhani zabwino [kwa anthu abwino] ndikuwachenjeza [oipa] kuti anthu asadzakhale ndi mtsutso pa Allah pambuyo pa [kudza kwa] aneneriwa. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.” [4:165]
WOYAMBA NDI WOMALIZA MWA ATUMIKI
Timakhulupilira kuti Woyamba mwa Atumiki anali Nuh ndipo Womaliza anali Muhammad, Mtendere ukhale pa iwo onse: “Ndithudi, takuvumbulutsira [chivumbulutso] monga momwe tidamuvumbulutsira Nuhu [Nowa] ndi aneneri amene anadza pambuyo pake.” [4:163], Ndipo “Muhammad salla Allah alaih wasallam sali tate wa aliyense mwa amuna anu, koma iye ndi Mtumiki wa Allah, ndiponso wotsiriza mwa Aneneri.” [33:40]
ATUMIKI ANYOTA ZA PAMWAMBA
Timakhulupilira kuti mwa Atumiki onse, Muhammad ndi yemwe ali ndi nyota za pamwamba kwambiri, kenako Ibrahim, Musa, Nuh ndi Isa mwana wa Mariam. Ayaah yotsatirayi ikufotokoza za atumiki amenewa: “Ndipo [akumbutse] pamene tidalandira kuchokera kwa Aneneri onse pangano lawo. Ndi kwa iwe, ndi kwa Nuh, Ibrahim, Musa, ndi Isa mwana wa Mariam. Ndipo tidatenga kwa iwo pangano la mphamvu (kuti adzafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu ndi kuitanira anthu ku chipembedzo cha Allah).” [33:7].
Timakhulupilira kuti uthenga wa Muhammad salla Allah alaih wasallam ndi womwewonso anali kupereka Atumiki onse am’mbuyo mwake, monga akunenera Allah kuti: “Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo chonga chomwe adam’langiza Nuh. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Musa, ndi Isa kuti: Mulimbikitse Chipembedzo [potsatira malamulo] ndikuti musalekane pa Chipembedzo.” [42:13]
ATUMIKI NDI ANTHU
Timakhulupilira kuti Atumiki onse ndi anthu olengedwa, omwe alibe mbiri zonga za Allah yemwe anawalenga. Allah akunena kuti: “Ndipo ine sindikukuuzani kuti ndili ndi nkhokwe zachuma cha Allah kapena kuti ine ndikudziwa zinthu zamseri, ndiponso sindinena kuti ndine Mngelo.” [11:31], ndipo anamulangiza Muhammad swalla Llahu alaihi wasallam yemwe ndi omaliza wa iwo, kuti anene: “Ine sindikukuuzani kuti ndili nazo nkhokwe [za zabwino za Allah kotero kuti nkukupatsani chimene mwafuna]. Ndipo [sindikukuuzani] kuti ndikudziwa zamseri, [za Allah kotero kuti nkukufotokozerani zomwe zingakufikeni pamalonda anu monga momwe mwafunira kuti ndikuuzeni]. Ndiponso sindikukuuzani kuti ine ndine Mngelo [nkumandifunsa kuti, “bwanji ukudya pomwe uli Mngelo?]” [6:50]; komanso: “Nena: “Ine ndekha ndilibe mphamvu yodzibweretsera chabwino kapena kudzichotsera choipa, koma chimene Allah wafuna.” [7:188], komanso: Nena “Ine ndilibe udindo wokupatsani mavuto kapena chilungamo [ndi zabwino]. Nena: “Ine palibe anganditeteze kuchilango cha Allah [ngati nditamnyoza] sindingapeze malo [othawira kuchilango chake] kupatula kwa Iye.” [72:21-22].
Timakhulupilira kuti Atumiki ndi akapolo a Allah. Iye anawadalitsa iwo ndi uthenga komanso anawatchula kuti ndi akapolo ake powayamikira. Allah akunena zokhudza Nuh, Mtumiki oyambilira mwa onsewo: “Ndiponso adawauza kuti, E, inu eni mbumba ya amene tidawasenza pamodzi ndi Nuh! [Khalani othokoza monga tate wanu.] Ndithu, iye adali kapolo wothokoza kwambiri.” [17:3]. Allah adanenanso za omaliza mwa iwo, Muhammad salla Allah alaih wasallam: “Watukuka Mwini kupereka madalitso, yemwe wavumbulutsa Qur’an kwa kapolo wake kuti ikhale mchenjezi kwa zolengedwa zonse.” [25:1]
Ndipo pa Atumiki ena onsewo, Allah anati: “Kumbukira, [iwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam akapolo athu Ibrahima, Ishaq ndi Ya’qub, eni mphamvu [pa ntchito yachipembedzo] ndi kuyang’ana kozindikira.” [38:45]; “Pilira [iwe Mtumiki] ku zimene akunenazo [kwa iwe], ndipo kumbuka kapolo wathu Daud, wamphamvu [pa Chipembedzo ndi zamdziko lapansi].” [38:17]; “Ndipo Daud tidampatsa [dalitso lobereka] Sulaiman, amene adali munthu wabwino” [38:30]; “Iye sadali kanthu koma ndi kapolo amene tidampatsa mtendere; Ndipo tidamchita kukhala chitsanzo [chodabwitsa] cha ana a Israeli.” [43:59].
Timakhulupilira kuti Allah anamalizira mauthenga ake kwa anthu pa Muhammad salla Allah alaih wasallam, chifukwa akunena kuti: “Nena: “E inu anthu! Ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu nonse. [Allah] yemwe ali nawo ufumu wa kumwamba ndipansi. Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Amapatsa moyo ndi imfa. Choncho, khulupilirani mwa Allah ndi Mtumiki wake yemwe ndi Mneneri wosadziwa kulemba ndi kuwerenga, yemwe akukhulupilira Allah ndi mawu ake. Ndipo mtsatireni kuti muongoke.” [7:158].
CHISILAMU NDI UTHENGA WOMALIZA KU DZIKO LONSE
Timakhulupilira kuti njira ya Mneneri Muhammad salla Allah alaih wasallam ndicho Chisilamu, chomwe Allah anawasankhira akapolo ake. Iye sadzalandira chipembedzo chilichonse kuchokera kwa munthu, poti anati: “Ndithudi, chipembedzo [choona] kwa Allah ndi Chisilamu.” [3:19]; “Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu ndipo ndakwaniritsa pa inu chisomo changa. Ndakusankhirani Chisilamu kukhala chipembedzo chanu.” [5:3] komanso “Ndipo amene angatsate chipembedzo chosakhala Chisilamu, sichidzalandiridwa kwa iye. Ndipo iye tsiku lomaliza adzakhala mmodzi mwa [anthu] otaika.” [3:85].
Timakhulupilira kuti yense yemwe anganene kuti chipembedzo china chosakhala Chisilamu ndi cholandiridwa kwa Allah, monga Chiyuda, Chikhristu ndi zina zonse, ameneyo ndi kaafiri, osakhulupilira ndipo akuyenera kulapa.
Timakhulupilira kuti yense yemwe angakane uthenga wa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam, ndiye kuti wakana mauthenga a Atumiki onse ngakhale atanena kuti iye ndi okhulupilira ndipo. Allah Ta’aala akunena kuti: “Anthu a Nuh adatsutsa Atumiki” [26:105]. Choncho, Allah akuwapanga iwo kuti anakanira uthenga wonse ngakhale kuti kunalibe Mtumiki wina Nuh alaih salaam asanabwere. Zimenezitu zikumvekanso mma aayah awa: “Ndithudi amene sakhulupilira Allah ndi Atumiki ake, ndikufuna kumulekanitsa Allah ndi atumiki ake, ponena kuti: ‘Ena tikuwakhulupilira, koma ena tikuwakana’, ndipo akufuna kugwira njira yapakati pa izi [osati ya Chisilamu chenicheni kapenanso ya anthu osakhulupilira]. Iwo ndiosakhulupilira enieni. Ndipo osakhulupilira tawakonzera chilango choyalutsa.” [4:150-151].
Timakhulupilira kuti palibe Mneneri wina pambuyo pa Mtumiki wa Allah, Muhammad, salla Allah alaih wasallam. Aliyense yemwe angadzitche kuti ndi Mneneri panthawi ino, kapena kukhulupilira aliyense yemwe akudzitcha kuti ndi Mneneri, wakanira Allah ndi Mtumiki wake komanso wakana zomwe amakhulupilira Asilamu onse.
ATSOGOLERI OLUNGAMA [AL-KHULAFAAU AL-RASHIDUN]
Timakhulupilira kuti Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam anali ndi alowammalo [ma Khalifa] omwe anapitiriza njira zake [Sunnah] poitanira ku Chisilamu ndikukonza umoyo wa anthu. Timakhulupilira kuti Khalifa yemwe anali wabwino kwa onse komanso oyambilira anali Abu Bakr Al-Siddiq, kenako Umar bun Al-Khattab, kenako Uthmaan bun Affaan, kenako Ali bun Abi Talib Allah asangalale nawo onse. Ulowammalo wawo unali kulingana ndi maubwino awo. Allah Ta’ala yemwe ndi Mwini nzeru zonse, sangapereke utsogoleri kwa munthu kupatula yemwe ali wabwino pakati pa munthu komanso ali ndi mbiri za utsogoleri.
Timakhulupilira kuti yemwe anali wapansi mwa ma Swahaba, akhoza kukhala wapamwamba kudzera mu mbiri zake zina kwa omwe anali abwino kuposa iye, koma zimenezo sizikutanthauza kuti iye ndi wapamwamba koposa, chifukwa kukhala wapamwamba kwa onse kuli ndi mfundo zake.
Timakhulupilira kuti Ummah wa Chisilamu ndi Ummah wolemekezeka pakati pa onse, ndipo Allah Ta’ala anaudalitsa ponena kuti: “Inu [Asilamu] ndinu mpingo wabwino umene wasankhidwa kuti uchite zokomera anthu [onse]. Mukulamula [kuchita] zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupilira mwa Allah.” [3:110].
MA SWAHABA A MTUMIKI
Timakhulupilira kuti wabwino kwambiri mu ummah uno ndi ma Swahaba a Mtumiki salla Allah alaih wasallam, kenako omwe anadza pambuyo pawo [ma Taabieen], kenako omwe anadza pambuyo pa ma Taabieen [ma Taabie Taabieen].
Timakhulupiliranso kuti gulu limeneli silidzapeza mavuto kuchokera kwa opereka mavuto mpaka Tsiku Lachiweruziro.
Timakhulupilira kuti kusemphana kumene kunkachitika ndi ma Swahaba a Mtumiki kunkachitika chifukwa cha kufunafuna chilungamo pakulongosola zinthu zomwe aliyense anali kufuna kuti zilongosoke. Yemwe anali olondola mwa iwo, adzalipidwa pawiri ndipo yemwe analakwitsa adzalipidwa kamodzi, koma kulakwitsa kwawoko kudzakhululukidwa.
Timakhulupilira kuti ndibwino kusiya kuyankhula zolakwika zawo ndikumatchula zomwe akuyenera kuyamikiridwa nazo. Tikuyenera kuyeretsa mitima yathu ndikuchotsamo udani womwe ungadze pa ma Swahaba, chifukwa Allah akunena kuti: “Sali ofanana mwa inu amene adapereka chuma [panjira ya Allah] pamodzi ndi kumenya nkhondo usadagonjetsedwe mzinda wa Makka, iwowo ndi omwe ali ndi ulemelero waukulu kuposa amene apereka chuma chawo ndi kumenya nkhondo pambuyo. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino [ngakhale ali osiyana ulemelero wawo];” [57:10]. Ndipo akunena za ife kuti: “Ndipo [okhulupilira] amene adadza pambuyo [pa Amuhajirina ndi Ansari] Akunena kuti: “Mbuye wathu tikhululukireni ndi anzathu amene adatitsogolera pa chikhulupiriro, ndipo musaike mmitima mwathu njiru ndi chidani kwa amene adakhulupilira. O, Mbuye wathu! Inu ndinu Wodekha Wachisoni.” [59:10].
***
Timakhulupilira tsiku lomaliza, lomwe ndi tsiku la chiweruziro pamene anthu adzaukitsidwa kukhala amoyo kuti akhale ku Mtendere kapena ku Chilango choopsa.
KUWUKITSIDWA
Timakhulupilira kuuka kwa akufa. Allah adzabwezeretsa moyo kwa onse omwe anamwalira pamene Israfil adzalize lipenga kachiwiri “Ndipo [pamene] lipenga lidzaimbidwa, onse a kumwamba ndi pansi adzakomoka kupatula amene Allah wamfuna. Kenako lidzaimbidwa lachiwiri; pamenepo [onse] adzauka; adzakhala akuyang’ana [modabwa: ‘n’chiyani chachitika!’]” [39:68]. Anthu adzauka kuchokera mmanda, kuyankha kuitana kwa Mbuye wa zolengedwa zonse. Iwo adzakhala opanda nsapato, amaliseche ndipo osadulidwa: “Monga tidayamba kulenga zolengedwa poyamba, tidzabwerezanso [kuzilenga kachiwiri. Ndipo aliyense adzalipidwa pazomwe adali kuchita] ili ndilonjezo lomwe lili pa Ife. Ndithu, ife ndiochita [zomwe tikunena.]” [21:104].
MABUKU A NTCHITO NDI KUYEZA KULEMERA KWA NTCHITO
Timakhulupilira mabuku a ntchito omwe adzapatsidwa kwa anthu kudzera kumanja kwawo kapena kumbuyo: “Tsono amene adzapatsidwe kaundula wazochita zake kudzanja la manja, basi iye, adzawerengedwa, kuwerengedwa kopepuka, ndipo adzabwelera kwa anthu ake [okhulupilira] ali wokondwa. Koma yemwe adzapatsidwe kaundula wazochita zake chakumanzere kudzera kumbuyo kwa msana wake [chifukwa chomunyoza], basi, iye adzaitana imfa [kuti imufikire; kuti afe apumule, koma siidzamufikira]; ndipo adzalowa ku moto woyaka.” [84:7-12]; “Ndipo munthu aliyense tam’mangilira m’khosi zochita zake; ndipo tsiku la Qiyaamah tidzam’tulutsira kaundula [momwe muli zochita zake]; adzam’peza wovundukulidwa. [Kudzanenedwa kwa iye]: “Werenga kaundula wako [kupyolera m’mphamvu za Allah ngakhale padziko lapansi siunkatha kuwerenga]; mzimu wako ukwanira lero kudziwerengera.” [17:13-14].
Timakhulupilira kuti zoyezera ntchito zidzakhazikitsidwa tsiku lachiweruziro ndipo palibe munthu amene adzalakwitsidwe: “Choncho, amene angachite chabwino Cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake. Ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake. [Allah sachitira chinyengo aliyense]” [99:7-8]; “Tsono omwe mlingo [wa zochita zawo zabwino] udzalemere, iwowo ndiwo opambana, ndipo omwe miyeso yawo [yazochita zabwino] idzatsike, iwowo ndi omwe adadziluzitsa okha; adzakhala ku Jahannam muyaya. Moto ukawawula nkhope zawo, ndipo adzakhala mmenemo uku akukukuta [mano]” [23:102-104] komanso: “Amene wachita chabwino alipidwa zabwino khumi zofanana ndi icho. Ndipo amene wachita choipa sadzalipidwa koma chonga icho [popanda kuonjezera]. Ndipo iwo sadzaponderezedwa.” [6:160].
SHAFA’AH YA MTUMIKI [KUWADANDAULIRACHIPULUMUTSO ANTHU OKHULUPILIRA]
Timakhulupilira kuti kupezeka kwa shafa’ah ya Mtumiki salla Allah alaih wasalam ndiko kupempha kwa Mtumiki komwe adzaloledwe ndi Allah, kuti apemphe mmalo mwa anthu ake, pamene adzakumane ndi zovuta zomwe sadzakwanitsa kupilira.
Anthu adzapita kwa Nuh alaih salaam, kenako kwa Ibrahim, kenako kwa Musa, kenako kwa Isa, koma onsewo adzakana kuti sangakwanitse, ndipo kenako adzapita kwa Muhammad salla Allah alaih wasallam.
Timakhulupilira kuti Shafa’ah idzachitika kwa anthu okhulupilira omwe adzayenera kupita kumoto, kuti asapititsidwe. Choncho Mtumiki salla Allah alaih wasallam adzaloledwa kuima pakati pa akapolo amenewo, komanso aneneri ena, okhulupilira ndi Angelo ena adzaloledwa kuchita shafaah.
Timakhulupiliranso kuti Allah adzawapulumutsa okhulupilira ena popanda shafa’ah ya aliyense, koma kudzera mu Chifundo chake basi.
DZIWE LA MTUMIKI
Timakhulupilira za dziwe la Mtumiki salla Allah alaih wasallam, lomwe madzi ake ndi oyera kuposa mkaka ndipo kukoma kwake ndikoposa uchi komanso kununkhira kwake ndikoposa musk. Mtunda wa mulitali ndi mulifupi mwake ndi kuyenda kwa mtunda wa mwezi watunthu. Kukongola komanso chiwelengero cha zikho zake ndi konga kwa nyenyezi. Okhulupilira mwa otsatira Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam akadzangomwa madzi amenewa sadzamvanso ludzu.
ULALO WOONGOKA [SIRAT]
Timakhulupilira za ulalo woongoka, womwe ndi Siraat womwe udzaikidwa pamwamba pa Jahannam ndipo anthu azidzawoloka malinga ndi ntchito zawo. Oyamba mwa iwo adzadutsa mofulumira ngati mphenzi, kenako otsatira pa iwo adzadutsa mofulumira ngati mphepo, kenako ngati mbalame, kenako ngati munthu yemwe akuthamanga. Mtumiki adzakhala ataima pa ulalo ndikumanena kuti: “Ambuye, pulumutsani, pulumutsani!” poti anthu ena ntchito zawo zidzakhala zopelewera. Ena mwa iwo adzadutsa chokwawa. Ndipo kumayambiliro ndikumapeto kwa ulalowo kudzakhala mbedza zomwe zizidzatenga anthu omwe Allah adzafuna kuwatenga; ena adzapulumutsidwa pomwe ena adzavulazidwa; ndipo ena adzaponyedwa mu Jahannam. [Al-Bukhari ndi Muslim].
Timakhulupilira zonse zomwe zatchulidwa mu Qur’an kapena mu Sunnah za Mtumiki, zoopsa zokhudza tsiku limeneli, Allah atiteteze.
Timakhulupilira shafa’ah ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam kwa anthu kuti akalowe ku Jannah. Shafa’ah imeneyi ndi yopatulika kwa Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam basi.
JANNAH NDI JAHANNAM
Timakhulupilira kuti kuli Jannah ndi Jahannam. Jannah ndi malo a mtendere ndi chisangalalo, omwe Allah Ta’ala awakonzera anthu ochita zabwino. Maso sanaonepo, makutu sanamvepo ndipo palibe yemwe anaganizirapo madalitso omwe anthu aku Jannah akawapeze: “Mzimu uliwonse sudziwa zimene awubisira zotonthoza diso [zosangalatsa moyo ku munda wamtendere] monga mphoto pazimene unkachita.” [32:17].
Jahannam ndi malo achilango omwe Allah wawakonzera anthu osakhulupilira komanso ochita zoipa. Mavuto akumeneko palibe yemwe angawaganizire kuti ndiotani: “Ndithu, achinyengo tawakonzera moto, womwe mipanda yake ikawazinga. Ndipo akapempha chithandizo [chifukwa cha ludzu loopsa lomwe likawapeza], akathandizidwa popatsidwa madzi [otentha kwambiri] monga ntofu, omwe udzasupula nkhope zawo. Taona kuipa chakumwa! ndi kuipa malo wotsamira!” [18:29].
Jannah ndi Jahannam zilipo pakalipano ndipo sizidzaonongeka mpaka muyaya: “Ndipo amene akhulupilira Allah ndi kumachita zabwino, adzamlowetsa m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake; akakhala mmenemo muyaya. Ndithu Allah wamkonzera rizq labwino [Jannah].” [65:11]; “Ndithu, Allah wawatembelera osakhulupilira ndi kuwakonzera moto woyaka kwambiri; Adzakhala mmenemo muyaya. Sadzapeza bwenzi ngakhale mthandizi” [33:64-66].
Sitimatsimikiza za yemwe angakalowe ku Jannah kupatula yekhayo yemwe Allah ndi Mtumiki wake anatsimikiza mu Qur’an kapena Sunnah. Mwa omwe analonjezedwa Jannah pakutchulidwa maina awo, ndi Abu Bakr, Umar, Uthman ndi onse omwe anatchulidwa ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam [AlBukhari ndi Muslim]. Mwa omwe timatsimikiza kuti akalowa ku Jannah chifukwa cha kukwanira kukhala a ku Jannah, ndi omwe ali okhulupirika komanso ochita zabwino.
Chimodzimodzinso sitimatsimikiza zayemwe angakalowe ku Jahannam kupatula yekhayo yemwe Allah ndi Mtumiki wake anatsimikiza mu Qur’an ndi Sunnah, pomutchula dzina kapena mbiri zake; mwa omwe anatchulidwa ndi maina awo kuti akalowa ku Jahannam ndi Abu Lahab, Amr Ibn Luhai Al-Khuza’i ndi ena, [Al-Bukhari ndi Muslim]. Kutsimikizika kwa kulowa ku Jahannam komwe kwatchulidwa mbiri zake ndi monga ma kafir [osakhulupilira], mushrik (opembedza mafano), kapena mpondakuwiri.
ZOMWE ZIMACHITIKA MMANDA
Timakhulupilira za mayesero a mmanda omwe ndi kufunsidwa kwa omwalira za Mbuye wake, Chipembedzo chake ndi Mneneri wake. Pamenepo, “Allah amawalimbikitsa amene akhulupilira ndi mawu olimba m’moyo wadziko lapansi, ndi moyo wapambuyo pa imfa” [14:27]. Okhulupilira adzayankha: “Allah ndi Mbuye wanga, Chisilamu ndi Chipembedzo changa, Muhammad ndi Mneneri wanga.” Pomwe okanira ndi ampondakuwiri adzanena: “Sindikudziwa, ndinangomva anthu akunena zina zake ndipo ine ndimanena.”
Timakhulupilira za kukhazikitsidwa mtima kwa okhulupilira mmanda mwawo: “Amene miyoyo yawo Angelo amaitenga iwo ali abwino, [Angelo] akunena kuti: “Mtendere uli pa inu, lowani kumunda wa Mtendere chifukwa cha [zabwino] zija zomwe mudali kuzichita.” [16:32].
Timakhulupilira za chilango cha mmanda kwa opyola malire komanso okanira “Ukadawaona anthu ochita zoipa akuthatha ndi imfa, nawo Angelo atawatambasula manja awo [ndikuwauza]: “Tulutsani moyo wanu; lero mulipidwa chilango chonyozeka chifukwa cha zomwe mudali kunenera Allah popanda choonadi, ndi kudzitukumula kwanu pa zizindikiro zake” [6:93]. Pa mfundo imeneyi, zoyankhula za Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi zodziwika ndithu. Msilamu akuyenera kukhulupilira zonse zomwe zinakambidwa mu Qur’an ndi mma Hadith zokhudza zinthu zosaoneka ndi maso, asasokoneze ndi za dziko, chifukwa zochitika za tsiku lomaliza sangazifananitse ndi zochitika za mmoyo uno. Kusiyana kwake ndi kwakukulu zedi, Allah ndiye Mwini kuthandiza.
MUTU 7: KUKHULUPILIRA CHIKONZERO CHA ALLAH
NDI CHILAMULO CHAKE
Timakhulupilira chikonzero cha Allah, chabwino ngakhale choipa chomwe iye wakonzera zolengedwa zake malinga ndi nzeru zake zakuya.
Mitundu ya Chikhulupiliro chimenechi: ilipo inayi:
1) Kudziwa: Timakhulupilira kuti Allah Ta’ala amadziwa chilichonse. Iye amadziwa zomwe zinachitika, zomwe zikuchitika, zomwe zidzachitike komanso mmene zidzachitikire. Kudziwa kwake nkosatha, ndipo samasaukira kudziwa kwina kwatsopano komanso saiwala zomwe akudziwa.
2) Kaundula: Timakhulupilira kuti Allah Ta’ala analemba pa Lawh Mahfuz, chilichonse chomwe chikuchitika kufikira tsiku lachiweruziro: “Kodi sudziwa kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zapansi? Ndithu, zonsezo zili mkaundula [wake], ndithu, [kudziwika kwa] zimenezo kwa Allah nkosavuta” [22:70].
3) Chifuniro: Timakhulupilira kuti Allah Ta’la anakonza chilichonse mu chifuniro chake. Palibe chomwe chingachitike popanda chifuniro cha Allah. Chilichonse chomwe wafuna chimachitika, ndipo chomwe sanafune sichichitika.
4) Kulenga: Timakhulupilira kuti: “Allah ndiye Mlengi wa chilichonse, Ndipo Iye ndi Muyang’aniri wa Chilichonse. Makiyi a kumwamba ndi pansi ali kwa Iye.” [39:62-3]. Mumtundu uwu muli zonse zomwe Allah mwiniwake amachita, komanso zonse zomwe zolengedwa zake zimachita, zonsezo ndi zochokera kwa Iye. Choncho, choyankhula, chochita kapena chomwe munthu sanachite, chimadziwika ndi Allah yemwe analemba zimenezo, komanso ndi yemwe anafuna kuti chichitike kapena chisachitike, poti iye ndi amene analenga zonsezo. “Kwa yemwe mwa inu akufuna kuyenda munjira yoongoka; koma simungafune chinthu mwa inu nokha pokhapokha atafuna Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.” [81:28-29]; “Ndipo Allah akadafuna, sakadamenyana; koma Allah amachita zimene akufuna.” [2:253]; “Ndipo ngati Allah akadafuna, sakadachita zimenezo. Choncho asiye ndi izo zomwe akupeka.” [6:137]; “Chikhalirecho Allah ndiye adakulengani ndi zimene mukuchita!” [37:96].
CHIFUNIRO CHA MUNTHU
Ngakhale kuti timakhulupiliranso kuti Allah Ta’la analenga munthu ndikumpatsa mphamvu ndi ufulu wodzisankhira kuchita zomwe wafuna, koma kuti zonsezo zili ndi malire ake omwe sakuyenera kupyola, monga:
1) Allah akunena kuti: “Choncho idzereni minda yanu mmene mungafunire;” [2:223]; komanso “Akadafunadi kuti atuluke [kupita ku nkhondo] akadakonzekera zokonzekera za kunkhondo;” [9:46]. Ma aayah amenewa, Allah watsimikizira munthu kuti “akanafuna kupita kunkhondo” komanso “kukonzekera” akanachita mukufuna kwawo.
2) Kumuuza munthu zoyenera kuchita ndi zoyasenera kuchita: Akanakhala kuti munthu alibe ufulu pakusankha, malangizo amenewa ndiye kuti akanatanthauza kuti Allah akumuza munthu kuchita zomwe sangakwanitse. Zimenezo zakanidwa
ndi Allah mukuyankhula kwake: “Allah sakakamiza mzimu uliwonse koma chimene chili cholingana ndi kukhoza kwake” [2:286].
3) Kumuyamikira yemwe wachita zabwino ndikumulipira zabwino, komanso kumudzudzula yemwe wachita zoipa ndikumupatsa chilango pa zochita zake: Ngati zochitazo sizidachitike mwakufuna kwa munthu, kumuyamikira kukhala masewera komanso kumulanga yemwe walakwa kukhala kumupondereza. Koma Allah ndithu sapondereza komanso sasewera.
4) Allah anatumiza Atumiki ake “[Iwo ndi] aneneri omwe adauza nkhani zabwino [kwa anthu abwino] ndi kuwachenjeza [oipa] kuti anthu asadzakhale ndi mtsutso pa Allah pambuyo pa [kudza kwa] Aneneriwa.” [4:165]. Ngati zochita zamunthu sizinachitike mwakusankha kwake, kutsutsa kwake sikugwira ntchito pakutumizidwa kwa Atumiki. Munthu aliyense akamachita chinthu amaona kuti akuchita kapena sakuchita mokakamizidwa. Koma amatha kuimilira, kukhala, kulowa, kutuluka, kuyenda ulendo kapena kusanyamuka mwakufuna kwake popanda kukakamizidwa ndi wina wake. Iye amatha kusiyanitsa pakati pa kuchita chinthu mwakufuna kwake ndi mokakamizidwa. Chimodzimodzinso Chisilamu chimasiyanitsa pakati pa zinthu ziwirizi; sichimalanga yemwe wachita chinthu cholakwika mokakamizidwa.
KUCHIMWA SIKOLOLEDWA
Timakhulupilira kuti ochimwa sanaloledwe kuti azichita machimo mu chikonzero cha Allah, Allah salola munthu kuchita tchimo; iye amachita kusankha kuti achite tchimolo ndipo sikuti amakhala akudziwa kuti zimenezo ndizomwe Allah anamukonzera, poti palibe yemwe amadziwa chomwe Allah anamukonzera mpaka chitachitika “Ndipo aliyense sadziwa chomwe apeze mawa;” [31:34]. Allah Ta’la salola kupereka chifukwa pa zoipa zomwe munthu akuchita, “Amene akuphatikiza [Allah ndi mafano] anena: “Ngati Allah akadafuna, sitikadamphatikiza, ife ngakhale makolo athu. Ndipo sitikadaletsa chilichonse. [Choncho, izi zomwe tikuchita, Allah akuziyanja]. Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo kufikira adalawa chilango chathu. Nena: “Kodi muli nako kudziwa [kokutsimikizirani zimenezi]? Koti mungatitulutsire [umboni wake wotsimikizira kuti Allah adakulamulani zimenezi]? Inu simutsatira china, koma zongoganizira basi. Ndipo simukunena china koma zabodza basi.” [6:148]. Choncho kwa omwe akugwiritsa ntchito qadar [chikonzero] pa kuchimwa, ponena kuti ‘zimenezi ndizomwe anatilembera’; n’chifukwa chani nanga simunagwire ntchito yabwino ngati munali kudziwa kuti Allah anakulemberani, poti simukudziwa kusiyana kwa zabwino ndi zoipa? N’chifukwa chaketu Mtumiki salla Allah alaih wasallam atawauza ma Swahaba ake kuti “aliyense malo ake anakonzedwa kale ku Jannah kapena ku Jahannam” anati: ‘tsopano pamenepo bwanji tingosiya kugwira ntchito zabwino?’ iye anati: “Ayi, gwirani ntchito zabwino, aliyense adzalondoledwa ku zomwe analengedwera”. [Al-Bukhari ndi Muslim].
Kwa ochimwa yemwe akuyesetsa kupeza pothawira mu qadar ya Allah: “tiyerekeze kuti mukufuna kupita ku Makkah, ndipo pali njira ziwiri zoti mukafikire kumeneko. Ndiye mwauzidwa ndi munthu okhulupirika kuti imodzi mwa njira ziwirizi ndi yoopsa komanso yovuta, pomwe inayo ndiyosavuta komanso yotetezeka; nzachidziwikire inu musankha yachiwiriyo. Simungatenge yoyambayo nkumanena kuti ndichikonzero cha Allah pa inu. Ndipo ngati mungatero, anthu akuonani kuti ndinu wamisala.”
Tikhoza kumuuzanso kuti: “tiyerekeze kuti mwapatsidwa mwayi wosankha pakati pa ntchito ziwiri, inayo ndi ya malipiro apamwamba; nzachidziwikire inu musankha yamalipiro apamwamba. Mukudzisankhira padziko pano zomwe zili zamtengo wochepa ku aakhira nkumagwiritsa ntchito zifukwa zoti ndi chikonzero chanu? Musankha bwanji zoipa ponena kuti ndizomwe wakukhonzerani Allah pomwe mukutha kusiyanitsa nokha chabwino ndi choipa?”
Tikhozanso kumuuza kuti: “timakuonani mukadwala, mumanka mukufunafuna machiritso mwa madokotala osiyanasiyana, ndipo mukamalandira machiritso mumakhala opilira ndi ululu wake, n’chifukwa chani simmangosiya ndikulolera kuti chimenecho ndi chikonzero cha Allah pa inu?”
ZOIPA ZOMWE SIZICHOKERA KWA ALLAH
Timakhulupilira kuti zoipa siziyenera kuikidwa kuti ndi za Allah, chifukwa cha Chifundo chake ndi Nzeru zake. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Ndipo zoipa sizikuchokera kwa inu.” [Muslim] Motero, chikonzero cha Allah pachokha sichimabwera ndi choipa chilichonse, chifukwa chikonzero chake ndi chifundo kwa ife kuchokera mu nzeru zake zakuya.
Zoipa zikhoza kupezeka kuchokera mu zotsatira za chikonzero chake, koma osati kuchokera mu chikonzerocho. Mtumiki salla Allah alaih wasallam adanena pa pemphero la Qunut yomwe adamuphunzitsa Hasan (Allah asangalale naye): “Ndipo titetezeni ku zoyipa zazomwe mwatikonzera” [Tirmidhi ndi ena]. Apa, Mtumiki anaika choipa kukhala chochokera mu zomwe Allah wakonza, osati kuti zomwe wakonzazo ndi zoipa. Choncho apa tikuona kuti zoipa zomwe zimapezeka mu qadar [chikonzero] sizimakhala kuti ndi chikonzerocho. Zimenezo zimakhala zoipa pambali imodzi komanso zabwino mbali ina, kapenanso zimakhala zoipa nthawi ina, komanso zabwino nthawi ina. Kotero, zowawa zomwe zimachitika mdziko chifukwa cha chilala, matenda, umphawi ndi mantha, ndi zoipa ndithu, koma ndi zabwino mbali zina, monga mmene Allah akunenera: “Chisokonezo chaonekera pamtunda ndi panyanja chifukwa cha zimene manja a anthu achita, kuti awalawitse [chilango cha] zina zomwe adachita; kuti iwo atembenukire [kwa Allah].” [30:41]. Kudula dzanja la wakuba kapena kumugenda wachigololo ndi zinthu zowawa kwa wakuba ndi wachigololo, koma ndi zabwino kwa iwo mbali ina, chifukwa ndi kuyeretsedwa kwa iwo kuti chilango cha moyo uno ndi cha tsiku la chiweruzo chisaphatikizike pa iwo. Zilango zimenezi ndi zabwino mbali ina: zimateteza anthu, chuma, ulemelero ndi ubale.
***
MUTU 8:PHINDU LA CHIKHULUPILIRO
Chikhulupiriro chafotokozedwachi chomwe chili ndi mfundo zikuluzikulu, chili ndi phindu lalikulu kwa aliyense yemwe amakhulupilira.
PHINDU LOKHULUPILIRA ALLAH
Kukhulupilira mwa Allah, maina ake, ndi mbiri zake zimachititsa munthu kukhala ndi chikondi ndi ulemelero wa Allah, zomwenso zimampangitsa kuti achite zomwe Allah walamula, ndikupewa zomwe waletsa. Izi ndi njira zopezera chisangalalo chambiri mmoyo uno ndi wa tsiku lomaliza kwa munthu aliyense. “Amene akuchita zabwino, wamwamuna kapena wamkazi uku ali Msilamu timkhazika ndi moyo wabwino [pano padziko, ndipo tsiku la Qiyaamah] tidzawalipira malipiro awo mochuluka kwambiri chifukwa cha zabwino zomwe ankachita.”[16:97].
PHINDU LOKHULUPILIRA ANGELO
Kumeneku ndi kuyamika pa ulemu womwe ukupezeka chifukwa cha kukhulupilira Allah, Mphamvu zake, ndi ulamuliro Wake; Kuyamikidwa ndi kwa Allah chifukwa amachititsa Angelo ena kukhala oyang’anira ena mwa akapolo ake, kulembera zochita zawo ndi zinthu zina zomwe zimawathandiza. Tiwakonde Angelo chifukwa cha zomwe akuchita, monga kupembedza Allah mwanjira yabwino kwambiri komanso kupemphelera okhulupilira.
PHINDU LOKUKHULUPILIRA MABUKU
Kuyamika chifundo ndi chisamaliro cha Allah kwa anthu ake, kotero kuti adapatsa Buku kugulu lirilonse kuti liwatsogolere.
Kuyamikira nzeru za Allah, pakuti adavumbulutsa mmabuku amenewa zomwe zimakwanira mtundu uliwonse. Qur’an yolemekezeka ndi Buku lomaliza ndipo ndiloyenera kwa anthu onse nthawi zonse mpaka tsiku lachiweruzo.
PHINDU LOKHULUPILIRA ATUMIKI
Kuyamika chifundo ndi chisamaliro cha Allah kwa anthu ake pakuwatumizira Atumiki olemekezeka kuti awatsogolere ku njira yolungama. Tithokoze Allah chifukwa cha chisomo chimenechi.
Kukonda ndi kulemekeza Aneneri ndi kuwatamanda momwe akuyenelera, chifukwa ndi Atumiki a Allah omwe anawasankha pakati pa anthu ake. Iwo adapembedza Allah molingana ndi kuthekera kwawo, anapereka uthenga wake kwa anthu, anapereka uphungu woona kwa anthu, ndipo anapilira moleza mtima pa chilichonse chomwe adalandira.
PHINDU LOKHULUPILIRA TSIKU LA CHIWERUZO
Kumvera Allah kuti mudzalandire mphotho tsiku lomaliza, ndikupewa kusamvera kulikonse poopa chilango chake.
Chilimbikitso kwa wokhulupilira pa chilichonse chimene akusowa nacho chisangalalo cha dziko lapansi; chifukwa cha kuyembekeza kuti adzalandire madalitso ndi mphoto ya tsiku lomaliza.
PHINDU LOKHULUPILIRA CHIKONZERO CHA ALLAH
Kuyezamira mwa Allah pamene mukuchita chilichonse; chifukwa gwero komanso zotsatira za zochitazo, zimachokera mu zotsatira za chikonzero cha Allah.
Kukhazikika kwamalingaliro ndi chitonthozo; chifukwa pamene munthu adziwa kuti chilichonse chiri muchikonzero cha Allah ndipo zovuta zikhoza kuchitika nthawi iriyonse, moyo wake umakhala womasuka ndipo mtima wake umakhutira ndi chikhonzero cha Allah. Palibe amene ali ndi moyo wosangalatsa, moyo wopanda nkhawa ndi chidaliro champhamvu, koma yemwe amakhulupilira chikonzero cha Allah.
Kukhala wosadzikuza pamene cholinga chikukwaniritsidwa; chifukwa limenelo ndi dalitso lochokera kwa Allah kudzera muzomwe adakonza kuti zikhale chifukwa cha zabwino ndi kupambana. Munthu ayenera kuyamika Allah chifukwa cha izi, ndikupewa kudzikudza.
Kukhala osadandaula pamene mukulephera; chifukwa chimenecho ndi chikonzero cha Allah, yemwe ali nazo zakumwamba ndi dziko lapansi. Koma popeza kuti zimenezo zichitikabe, munthu ayenera kukhala woleza mtima ndi kuyembekezera mphotho yochokera kwa Allah pakupilira kwake. Allah akunena zamakhalidwe awiri abwino mu ndime iyi: “Silipezeka tsoka lililonse panthaka [monga chilala] ngakhale pamatupi anu koma lidalembedwa kale m’Buku [la Allah] tisadalilenge ndi kulipereka. Ndithu zimenezo kwa Allah n’zofeŵa. [Takudziwitsani zimenezi] kuti musadandaule ndi chimene chakudutsani, ndikutinso musakondwere monyada ndi chimene wakupatsani. Allah sakonda aliyense wodzitama, wonyada,”[57: 22-3].
Timapemphera kwa Allah Ta’ala kuti atipatse ife chikhulupiliro chimenechi, atizindikiritse zipatso zake, atiwonjezere madalitso ake, atichite kukhala munjira yolunjika kumene Iye watitsogolera, ndi kutipatsa madalitso ochokera kwa Iye, ndithu Iye ndi wopereka.
Kuyamika konse kukhale kwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse, mtendere ndi madalitso zikhale pa Mtumiki Muhammad,
banja lake, ma Swahaba ake ndi omwe akuwatsatira moyenera. Ameen
***