Categories

معلومات المواد باللغة العربية

Calling to Allah's Religion

Number of Items: 5

  • chiCheŵa

    LINK

    QUR’AN YOLEMEKEZEKA yotanthauzidwa m’Chichewa ndi

  • chiCheŵa

    PDF

    Chifukwa chakufunika kwa uthengawu kuti ufike kwa anthu onse, a Bungwe la Africa Muslim Agency adandipempha kuti ndimasulire Qur’an m’chichewa, ndicholinga chakuti amene sangathe kumvetsa uthenga wake m’chiarabu, aumve m’chilankhulo chawo cha Chichewa. Choncho ntchitoyi idagwirikadi kotero kuti munthu akawerenga bwinobwino akhoza kumva uthenga wa Mulungu m’Qur’an. Ndayetsetsa m’kutanthauzira kwanga mawu oyerawa kuti musakhale zolakwika zambiri, koma ntchito yogwira Munthu siilephera kupezeka zolakwika kupatula zochita za Chauta. Munthu ndi Munthu basi. Choncho ndikupempha aliyense amene angapeze zolakwika pakatanthauzidwe ka Qur’an kapena kasankhidwe kamawu oyerawa, kuti anditumizire ndi cholinga choti pomazatuluka bukuli kachiwiri muzakhale mopanda zolakwika zimenezo. Pamene ndimagwira ntchitoyi, panali mabuku amene ndimathandizika nawo pakasankhidwe ka kutanthauzira koyenera kwa Qur’an, komanso anthu amene amandithandiza pakasankhidwe ka mawu oyenera m’chichewa. Mabukuwa ndi awa Tafsiri ya Jalalain, Tafsiri ya ibn Kathiri, Al Muntakhab ndi Swafuat Tafaasiri. Ndipo Ntchito yotanthauzira inatha m’chaka cha 1987 pambuyo poigwira mzaka zitatu. Ndipo kuyambira nthawiyo kufikana m’chaka cha 1999 yakhala ikuunikidwa ndi ma Sheikh akuluakulu m’dziko muno. Ine M’bale Wanu -Sheikh Khalid Ibrahim

  • chiCheŵa

    PDF

    Buku ili lasonkhanitsa kakhalidwe kwa amayi m’zipembedzo zitatu: Chiyuda, Chikristu ndi Chisilamu. Bukuli lalongosola mfundo zofunikira zochokera mu Chiyuda, komwe mzimayi sanangomutchula kuti ndi wochimwa, koma anatinso ndiyemwe anamuchimwitsa mwamuna. Koma Qur’an ili ndi kuwona kosiyana ndi mabuku ena onse, poti imamuona mzimai kuti ndi wofunikira kwambiri pa chitukuko cha munthu. Kumbali ya kuchimwa kapena kulungama, mzimai ali ndi kakhalidwe kofanana ndi mwamuna mchipembedzo; iye sichiyambi ya machismo onse. Bukuli lalongosola zokhudza Hijaab, ufulu wa kuphunzir kwa mkazi, ufulu wa kukhala ndi chuma chake pambuyo pa kukwatira, kulowa mmalo pambuyo pa kumwalira m’bale wake, mitala ndi nkhani zina. Awerengi a bukuli azindikira kusiyana komwe kulipo pakati pa Chisilamu ndi zipembedzo zina.

  • chiCheŵa

    PDF

    Cholinga cha bukhuli ndi kuwaunikira anthu omwe amafuna kudziwa zoona zokhazokha, pa zauthenga weniweni womwe Yesu (mtendere ukhale pa iye) ankaphunzitsa. Bukhuli likukamba za machitidwe ena omwe analetsedwa kapena kuvomerezedwa m’Baibulo. Pali chikhulupiliro chakuti anthu akawerenga bukhuli adzipezera okha gulu lenileni la anthu lomwe limatsatira chiphunzitso cha Yesu (mtendere ukhale pa iye). Umboni wochokera m’Baibulo ugwiritsidwa ntchito pofuna kuwaunikira awerengi athu chipembedzo chenicheni cha Yesu (mtendere ukhale pa iye) lero lino. Anthuwa ayenera kudziwa otsatira enieni a chiphunzitso cha Baibulo.

  • chiCheŵa

    PDF

    CHISILAMU NDI CHIPEMBEDZO CHA MBUYE WA ZOLENGEDWA ZONSE