Categories

معلومات المواد باللغة العربية

Issues That Muslims Need to Know

Number of Items: 6

  • chiCheŵa

    PDF

    MALAMULO OFUNIKIRA KWA MSILAMU

  • chiCheŵa

    PDF

    Mu buku ili muli makomo awa: Kufunika kwa Swalaat, lamulo lake komanso zoyenereza kuti swalaat itheke. Machitidwe a wudhu kudzera m’zithunzi zolongosola bwino, kenako Sunnah za wudhu komanso zomwe zimaononga wudhu. Mu bukuli mulinso mapangidwe a Adhaan ndi Iqaamah, mapangidwe a swalaat kudzera m’zithunzi zolongosola bwino, komanso muli khomo la swalaat zisanu ndi swalaat zina za Sunnah. Komanso mukupezeka khomo la Twahara. Bukuli ndilofunikira kwambiri kwa omwe angolowa kumene Chisilamu, komanso Asilamu ena ongoyamba kumene kuphunzira.

  • chiCheŵa

    PDF

    Buku ili likukamba nsanamira zisanu ndi chimodzi za chikhulupiliro cha Msilamu. Layamba ndi kukamba mwachidule zomwe Msilamu amakhulupilira nthawi zonse, kenako lakamba zakomwe chikhulupilirochi chikuchokera (Qur’an ndi Sunnah). Nsanamira zimenezi ndimonga: Kukhulupilira Allah Yekha, kukhulupilira Angelo, kukhulupilira Mabuku a Allah, kukhulupilira Atumiki a Allah, kukhulupilira Tsiku Lachiweruzi ndinso kukhulupilira Chikhonzero cha Allah – komwe zabwino ndi zoipa zimachokera. Choncho buku ili ndi chiwongoko kwa okhulupilira komanso kwaomwe akufuna kukhulupilira.

  • chiCheŵa

    LINK

    QUR’AN YOLEMEKEZEKA yotanthauzidwa m’Chichewa ndi

  • chiCheŵa

    DOC

  • chiCheŵa

    PDF

    Chifukwa chakufunika kwa uthengawu kuti ufike kwa anthu onse, a Bungwe la Africa Muslim Agency adandipempha kuti ndimasulire Qur’an m’chichewa, ndicholinga chakuti amene sangathe kumvetsa uthenga wake m’chiarabu, aumve m’chilankhulo chawo cha Chichewa. Choncho ntchitoyi idagwirikadi kotero kuti munthu akawerenga bwinobwino akhoza kumva uthenga wa Mulungu m’Qur’an. Ndayetsetsa m’kutanthauzira kwanga mawu oyerawa kuti musakhale zolakwika zambiri, koma ntchito yogwira Munthu siilephera kupezeka zolakwika kupatula zochita za Chauta. Munthu ndi Munthu basi. Choncho ndikupempha aliyense amene angapeze zolakwika pakatanthauzidwe ka Qur’an kapena kasankhidwe kamawu oyerawa, kuti anditumizire ndi cholinga choti pomazatuluka bukuli kachiwiri muzakhale mopanda zolakwika zimenezo. Pamene ndimagwira ntchitoyi, panali mabuku amene ndimathandizika nawo pakasankhidwe ka kutanthauzira koyenera kwa Qur’an, komanso anthu amene amandithandiza pakasankhidwe ka mawu oyenera m’chichewa. Mabukuwa ndi awa Tafsiri ya Jalalain, Tafsiri ya ibn Kathiri, Al Muntakhab ndi Swafuat Tafaasiri. Ndipo Ntchito yotanthauzira inatha m’chaka cha 1987 pambuyo poigwira mzaka zitatu. Ndipo kuyambira nthawiyo kufikana m’chaka cha 1999 yakhala ikuunikidwa ndi ma Sheikh akuluakulu m’dziko muno. Ine M’bale Wanu -Sheikh Khalid Ibrahim