P |
afupifupi anthu onse amakhulupilira kuti kunali munthu wotchedwa Yesu (mtendere ukhale pa iye), koma iwo amasiyana momwe amamvera ndikutsatira uthenga womwe iye ankaphunzitsa. Kuchuluka kwa mipingo ya Chikhrisitu ndi mitundu ya Baibulo masiku ano ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti anthu amamva ndi kutsatira uthenga wa Yesu (mtendere ukhale pa iye) mosiyana. Funso nkumati: Kodi uthenga weniweni wachoonadi wa Yesu (mtendere ukhale pa iye) uli kuti?
Nanga ndi anthu ati omwe amatsatira uthenga weniweni wa Yesu lero lino? Cholinga cha bukhuli ndi kuwaunikira anthu, omwe amafuna kudziwa zoona zokhazokha, pa zauthenga weniweni womwe Yesu (mtendere ukhale pa iye) ankaphunzitsa. Bukhuli likukamba za machitidwe ena omwe analetsedwa kapena kuvomerezedwa m’Baibulo. Pali chikhulupiliro chakuti anthu akawerenga bukhuli adzipezera okha gulu lenileni la anthu lomwe limatsatira chiphunzitso cha Yesu (mtendere ukhale pa iye). Umboni wochokera m’Baibulo ugwiritsidwa ntchito pofuna kuwaunikira awerengi athu chipembedzo chenicheni cha Yesu (mtendere ukhale pa iye) lero lino. Anthuwa ayenera kudziwa otsatira enieni a chiphunzitso cha Baibulo.
Akhrisitu lero lino samalabadira machitidwe a Yesu (mtendere ukhale pa iye) omwe ali m’Baibulo ngakhale machitidwewa ndi omwe ayenera kutenga gawo lalikulu pa chikhulupiliro chawo cha Chikhrisitu.
***
M’baibulo, dzina loti Mulungu limayimira Mlengi mmodzi yekha yemwe analenga zinthu zonse. Mulungu mmodzi yekhayu ndi yemwe ayenera kupembedzedwa.
Chipangano Chatsopano chikunena kuti:
Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo lye yekha yekha udzamlambira.” [Mateyu 4:10]
“Yesu anayankhula kuti: …mvera Israyeli, Ambuy eMulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi. [Mariko 12:29]
Chipangano Chakale chikunena kuti:
“…Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu” [Yesaya 44:6]
“Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine. Yang’anani kwa Ine, mupulumutsidwa... mabondo onse adzandigwadira ine...” [Yesaya 45:21-23]
Ndemanga
Ndime za m’Baibulozi zikufotokoza momveka bwino za chithunzithunzi choona chenicheni cha Mulungu. Ichi ndichithunzithunzi chomwe atumiki a Mulungu onse monga Yesu ndi Mose (mtendere ukhale pa iwo) anali nacho, ndipo atumiki onsewa ankawaitanira anthu kuchiphunzitso chimenechi. Ngakhale izi zili chonchi, chithunzithunzi cha Mulungu chomveka bwinochi sichikupanga gawo la chikhulupiliro cha Akhrisitu lero lino. Chikhulupiliro chawo mwa Mulungu Atate, Mulungu Mwana, ndi Mulungu Mzimu Woyera chikutsutsana kwambiri ndi chiphunzitso chomveka bwino choti Mulungu ndi mmodzi yekha.
Ndime za m’baibulo zomwe zasanthulidwazi zatiwunikira kuti Mulungu ndi mmodzi. Choncho, sikoyenera kutchula chinthu china chomwe chili kumwamba kapena padziko lapansi kuti Mulungu chifukwa Mulungu ndi mmodzi yekha.
Pali ndime imodzi yokha ya m’Baibulo yomwe imayikira umboni kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana, ndi Mulungu Mzimu Woyera. Koma ndime imeneyi simapezeka m’maBaibulo a New International Version (NIV) komanso m’maBaibulo a Revised Standard Version (RSV) chifukwa ndimeyi inachotsedwa. Pa zakuchotsedwa kwa ndimeyi, ma Baibulowa amati ndimeyi inachotsedwa chifukwa choti sinkapezeka m’maBaibulo omwe ankalembedwa kalekale m’zaka za m’ma 1600. Ndime yomwe inachotsedwayi ili motere:
“Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu, ndi Madzi, ndi Mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.” [1 Yohane (Buku Loyamba) 5:8]
Mafunso ambiri; Mayankho ochepa
• Ngati Mulungu ali mmodzi wa ‘Utatu’, ndi chifukwa chiyani lye sanakambe za izi m’Chipangano Chakale?
• Kodi Yesu (mtendere ukhale pa iye) ananenapo zoti Iye ndi mmodzi wa ‘Utatu wa Mulungu’? Nanga Mzimu Woyera’ nawonso unakambapo za izi?
• Ngati Utatu wa Mulungu’ ali maziko a chikhulupiliro cha chipembedzo, ndichifukwa chiyani m’Baibulo palibe malo ena pomwe pali mawu oti: Utatu wa Mulungu?
• Ngatidi ‘Utatu wa Mulungu’ ndi chikhulupiliro chopambana kwambiri ngati momwe amachitchukitsira, ndichifukwa chiyani chikhulupilirochi sichimatchuka Yesu (mtendere ukhale pa iye) asanabadwe?
• Ngati Yesu (mtendere ukhale pa iye) anafera machismo a anthu, ndindani yemwe anafera machimo anthu omwe anamwalira iye ‘asanawafere anthu machimo’?
Mwana wa Mulungu?
Mawu oti ‘Mwana wa Mulungu’ m’Baibulo samatanthauza mwana weniweni wodziberekera yekha Mulungu. Ngati Yesu (mtendere ukhale pa iye) alidi mwana weniweni wa Mulungu, ngati momwe Baibulo likunenera, ndiye kuti Adamu, Davide, Efraimu (mtendere ukhale pa iwo) ndi ena otero ayeneranso kumatchedwa ana enieni a Mulungu chifukwa malingana ndi Baibulo nawonso ndi ana a Mulungu.
“..ndipo Efraimu ali mwana wanga woyamba” [Yeremiya 31:9]
“..mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu mwana wa Mulungu” [Luka 3:38]
“Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.” [Aroma 8:14]
“.Yehova ananena ndi ine (Davide), Iwe ndiwe mwana wanga; Ine (Mulungu) lero ndakubala.” [Masalimo 2:7]
Ndemanga
Zikuonetsa kuti mawu oti ‘mwana wa Mulungu’ sanatanthauziridwe moyenerera kuchokera kuchiyankhulo cha Chigiriki. N’kutheka kuti otanthauzira Baibuloli mu ziyankhulo zina ankafuna kutanthauza kuti ‘kapolo wokondedwa wa Mulungu’, osati ‘mwana wodziberekera yekha Mulungu ngati momwe anthu amaganizira lero lino. Anthu akamakamba za ‘mwana wa Mulungu’ n’kumatanthauza kuti ndi mwana weniweni wodziberekera yekha Mulungu, ndiye kuti Davide (mtendere ukhale pa iye) nayenso ayenera kumatchedwa mwana weniweni wa Mulungu. Iyenso ayenera kumatchuka pakati pa anthu onse kuti ndi mwana Mulungu.
M’Baibulo, anthu ambiri kuonjezerapo Yohane akunenapo za ‘ana a Mulungu: (19) “Tidziwa kuti tili ife (ndi ana) ochokera mwa Mulungu.... (20) Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso kuti tizindikire...” [1 Yohane 5:19-20]
M’Baibulo, Yesu (mtendere ukhale pa iye) akamamutchula Mulungu kuti Atate’ akunena mokuluwika. Iye akugwiritsira ntchito liwuli ndi cholinga chopereka ulemu kwa Mulungu. Potero, Iye amakhalanso akusonyeza kuti iye ndiwokondeka wa Mulungu. Ichi ndi chifukwa chakenso pemphero lija la ana kwa Mulungu limayamba motere: “Atate athu mul im’mwamba...”
Ndemanga yomaliza pa za umodzi wa Mulungu
M’Baibulo, palibe malo ngakhale amodzi omwe Yesu ananena kuti: “Ine ndine Mulungu” kapena “Ndilambireni”. Kukanakhala kuti ichi chinali chiphunzitso chofunikiradi kwambiri mu Chikhrisitu, bukhu la Baibulo likanakamba za izi motsindika ndi momveka bwino.
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi chikhulupiliro chomveka bwino chakuti Mulungu ndi mmodzi chili kuti lero lino?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena samatsatira chikhulupilirochi?
• Nanga lero lino, ndianthu ati omwe amakhulupilirabe mu umodzi wa Mulungu?
***
Baibulo limakamba zoti Yesu (mtendere ukhale pa iye) amapemphera pogwetsa nkhope yake pansi, ngati momwe Mose, Abrahamu, Davide (mtendere ukhale pa iye) komanso atumiki ena a Mulungu amachitira akamamupembedza Mulungu. Nawu umboni wochokera m’Baibulo:
1. Yesu (mtendere ukhale pa iye) anagwetsa nkhope yake pansi pochita mapemphero.
“Ndipo anamuka patsogolo pang’ono nagwa nkhope yache pansi, napemphera, nati, ‘Atate, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna ine koma Inu.” [Mateyu 26:39]
2. Abramu (mtendere ukhale pa iye) anagwetsa nkhope yake pansi pochita mapemphero. “Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi... [Genesis 17:3]
3. Mose ndi Aaroni (mtendere ukhale pa iye) anagwetsa nkhope zawo pansi pochita mapemphero.
“Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kumka ku khomo la chihema chokomanako, nagwa nkhope zawo pansi...” [Numeri 20:6]
4. Eliya (mtendere ukhale pa iye) anagwetsa nkhope yake pansi pochita mapemphero.
“…koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimeli; nagwadira pansi, naika nkhope yache pakati pa maondo ache.” [1 Mafumu 18:42]
5. Yoswa (mtendere ukhale pa iye) anagwetsa nkhope yake pochita mapemphero.
“Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yache pansi, napembedza, nati...” [Yoswa 5:19-20]
Ndemanga:
Mawu oti ‘napembedza’ mu ndime ili mumtundayi akuonetsa kuti Yoswa (mtendere ukhale pa iye) anagwa pansi osati ndi chifukwa china ayi, koma chomupembedza Mulungu mmodzi yekha basi.
6. Davide (mtendere ukhale pa iye) anagwetsa nkhope yake pansi popemphera. “…Davide anauka chakumwera, nagwa nkhope yache pansi, nawerama katatu...” [1 Samueli 20:41]
Ndime zina za m’Baibulo zomwe zikuchitira umboni pankhaniyi ndi izi: “Pamene Mose anamva ichi anagwa nkhope yache pansi..” [Numeri 16:4]
“Ndipo (Mose ndi Aroni) anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu...” [Numeri 16:22]
“Ndipo Yoswa anang’amba zobvala zake, nagwa nkhope yake pansi, kulikasa la Yehova...” [Yoswa 7:6]
“Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m’kamwa mwanga m’chilungamo, ndipo sadzabwera, kuti maondo onse adzandigwadira ine...” [Yesaya 45:23]
Ndemanga:
Popemphera, atumiki ndi aneneri onse a Mulungu amagwada pansi nayika nkhope zawo pakati pa maondo awo, ngati momwe chikuonekera chithunzi chili pamwambapa.
Popemphera, Akhrisitu ambir imasiku ano amagwada, kuomba m’manja ndikuchita zinthu zina zosiyaniranatu ndi zomweYesu (mtendere ukhale pa iye) ankachita. Popemphera, Yesu (mtendere ukhale pa iye) ankachita zomwe atumiki onse a Mulungu ankachita. Iye ankagwetsa nkhope yake pansi.
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa kugwetsa nkhope pansi popemphera unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena satsatira mtchitidwewu?
• Nanga lero lino, ndi anthu ati omwe amalemekezabe ndi kutsatira mchitidwewu?
***
Kupereka chaulere kwa anthu osowa ndi lamulo la m’Baibulo. Choperekachi sichiyenera kukhala msonkho kapena mtuka wa pachaka wopereka ku mpingo ayi, koma chiyenera kukhala chopereka chaulere chopita kwa anthu okhawo omwe ali aumphawi ndi osowa.
1. Mose (mtendere ukhale pa iye) alamulidwa kupereka chaulere kwa osowa
“..chifukwa chake ndikuuzani ndikuti, dzanja lanu mulitansire ndithu m’bale wanu, ndi ozunzika anu ndi aumphawi anu, a m’dziko mwanu.” [Deuteronomo 15:11]
“Muzipereka ndithu limodzi la mbeu zanu, zofuma ku munda, chaka ndi chaka...” [Deuteronomo 14:22]
“Mtuka wapachaka ku mpingo’ ndi gawo la chikhumi la zokolola zones lomwe linakhazikitsidwa kuti liperekedwe kwa anthu osauka chaka ndi chaka.” [Oxford Dictionary]
2. Yesu apempha anthu kupereka chaulere kwa osowa
“Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja; kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zam’seri; ndipo Atate wako wakuona m’seri adzakubwezera iwe.” [Mateyu 6:3-4]
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wakupereka chaulere kwa anthu osowa unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena satsatira mtchitidwewu?
Nanga lero lino, ndi anthu ati omwe amalemekezabe ndi kutsatira mchitidwewu?
***
Tikasanthula Chipangano Chatsopano m’Baibulo, tipeza kuti Yesu (mtendere ukhale pa iye) ankasala. Atumiki onse a Mulungu omwe analipo Yesu (mtendere ukhale pa iye) asanabwere ankasalanso.
“Ndipo pamene iye (Yesu) analibe kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.” [Mateyu 4:2]
“Koma mzimu wamtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera ndi kusala zakudya mpamene mungautulutse.” [Mateyu (BukuLoyera) 17:21]
“Ndipo anaunjikana ku Mizipa natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija...” [1 Samueli 7:6]
“Ndipo pakutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya... Pamenepo, m’mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.” [Machitidwe 13:2-3]
“Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadya mkate kapena kumwa madzi.” [Eksodo 34:28]
“Ndipo pamene ponse musala kudya musakhale ndi nkhope yachisoni ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao kuti aonekere kwa anthu kuti ali mkusala kudya. Inde ndinena kwainu, iwo alandiriratu mphoto zao. Koma iwe, posala kudya dzola mutu wako, ndikusamba nkhope yako; kuti usaonekere kwa anthu kuti uli kusala kudya, koma kwa Atate wako ali m’seri: ndipo Atate wako wakuona m’seri adzakubwezera iwe.” [Mateyu 6:16-18]
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa kusala unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena satsatira mchitidwewu?
• Nanga lero lino, kodi ndi anthu ati omwe amalemekezabe ndi kutsatira mchitidwewu?
***
Chipangano Chakale, ngakhalenso Chatsopano, chimalongosola za kufunika koyeretsa thupi munthu asanachite mapemphero. Izi ndi zomwe Yesu (mtendere ukhale pa iye), ngakhalenso atumiki a Mulungu omwe analipo Yesu (mtendere ukhale pa iye) asanabwere, ankachita. Munthu asanapemphere ayenera kuyeretsa ziwalo zina za thupi lake monga manja, nkhope, mapaz indi zina zotero.
1. Mose ndi Aroni (mtendere ukhale pa iwo) adziyeretsa potsuka manja ndi mapazi awo asanapemphere: “Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba. Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ache amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m’menemo... monga Yehova adamuuza Mose.” [Eksodo 40:30-31]
Mose ndi Aroni (mtendere ukhale pa iwo) sanasambitse manja ndi mapazi awo mwakufuna kwawo ayi. Iwo anachita iz ichifukwa Mulungu adamuuza Mose kuti iwo azitero.
2. Davidi (mtendere ukhale pa iye) asamba asanapemphere: “Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zobvala; nafika ku nyumba ya Yehova, napembedza...” [2 Samueli 12:20]
3. Paulo adziyeretsa asanalowe m’Kachisi “Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m’mawa mwache m’mene anadziyeretsa nao pamodzi analowa m’Kachisi...” [Machitidwe 21:26]
Nayenso Paulo, yemwe ali wotsatira wa Yesu (mtendere ukhale pa iye), ankadziyeretsa asanapemphere. Apa ndizachionekere kuti Paulo sankadziyeretsa ndi cholinga china ayi, koma chokachita mapemphero. Yesu (mtendere ukhale pa iye) nayenso ankadziyeretsa asanapemphere. Iye ankachita izi potsatira mchitidwe wa atumiki a Mulungu omwe analipo iye asanabwere, ngati momwe akunenera m’Baibulo:
“Musaganize kuti ndinadza ine kudzapasula chilamulo kapena (machitidwe) a aneneri; sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa”
[Mateyu 5:17]
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa kusambitsa ziwalo (thupi) mapemphero asanachitike unanka kuti?
• Nchifukwa chiyani lero lino anthu ena satsatira mchitidwewu?
• Nanga lero lino, ndi anthu ati omwe amalemekezabe ndi kutsatira mchitidwewu?
***
MUTU 6 Mdulidwe m’Baibulo
Yesu (mtendere ukhale pa iye), ngakhalenso aneneri ndi atumiki a Mulungu omwe analipo iye asanabwere kuyambira pa Abrahamu (mtendere ukhale pa iye), analandira mdulidwe. Baibulo limati mchitidwewu uyenera kutsatiridwa mpaka kalekale.
“Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula iye, anamutcha dzina lache Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe iye m’mimba.” [Luka 2:21]
“Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, koma iwe uzikumbukira pangano langa, iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako m’mibadwo yawo.” [Genesis 17:9]
Izi zikuonetsa kuti mchitidwe wa mdulidwewu unakhazikitsidwa kuti uzichitika mpaka muyaya.
“Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.” [Genesis 17:10]
Malingana ndi ndimeyi, ana eni eni ochokera mwa Abraham (mtendere ukhale pa iye) ndi omwe amalemekeza ndi kutsatira mchitidwe wa mdulidwewu.
“Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu.” [Genesis 17:11]
Maganizo a Paulo (omwe titawakambirane nthawi ina) pa za mdulidwe akutsutsana kwambiri ndi lamulo loti amuna azilandira mdulidwe.
“(ana) A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu...” [Genesis 17:12]
Zoti amuna azidulidwa si mawu okuluwika ayi. Mawuwa ndi omveka bwino ndipo akutanthauza zomwe akunena. Pofuna kukwaniritsa pangano lamuyaya la pakati pa Mulungu ndi Abrahamu (mtendere ukhale pa iye), Yesu (mtendere ukhale pa iye) analandira mdulidwewu ali ndi masiku asanu ndi atatu, ngati momwe malamulo m’Baibulo akunenera. Choncho, chizindikiro cha mdulidwe chikhoza kutidziwitsa otsatira enieni a Yesu komanso a Abrahamu (mtendere ukhale pa iye).
Nanga, kodi ndindani yemwe anathetsa lamulo la mdulidwe pakati pa Akhrisitu?
Lero lino, Akhrisitu samalabadira za mdulidwe chifukwa cha momwe Paulo anatanthauzira lamulo la mdulidwe m’Baibulo. Iye anatanthauzira lamuloli molakwika ponena kuti mdulidwe womwe umanenedwawu si mdulidwe wa khungu ayi, koma wa mtima, chikhalirecho Yesu (mtendere ukhale pa iye) mwini wake analandira mdulidwe wa khungu.
Nawu umboni wochokera m’Baibulo wa zomwe Paulo akukamba pa za mdulidwe:
M’kalata yake kwa Aroma, Paulo akuti:
“…koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mu mzimu, sim’malembo a...” [Aroma 2:29]
M’kalata yake kwa Agalatia, Paulo akuti:
“Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khrisitu simudzapindula naye kanthu.” [Agalatiya 5:2]
Yesu sanalandire mdulidwe wa mumtima. Kuonjezera apo, iye sanayankhulepo za mdulidwe wa mumtima. Yesu anasunga pangano lomwe lili la muyaya polandila mdulidwe wa khungu. Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa mdulidwe unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena satsatira mchitidwewu?
• Nanga lero lino, kodi ndi anthu ati omwe amalemekezabe ndi kutsatira mchitidwewu?
***
Nkhumba ndi nyama yodetsedwa m’Baibulo potsatira zomwe zikupezeka mu ndime izi:
“...ndinkhumba, popeza igawanika chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa. Nyama yache musamaidya, mitembo yake musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.” [Levitiko 11:7-8]
“...ndi nkhumba, popeza igawanika ziboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.” [Deuteronomo 14:8]
Zikuoneka kuti Yesu (mtendere ukhale pa iye) sankadya nyama ya nkhumba chifukwa Baibulo limanena kuti iye anabwera kudzalemekeza ndi kudzatsatira malamulo a Mose (mtendere ukhale pa iye). Yesu (mtendere ukhale pa iye) akunena m’Baibulo kuti:
“Musaganize kuti ndinadza Ine (Yesu) kudzapasula chilamulo kapena (machitidwe) aaneneri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.” [Mateyu 5:17]
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa kusadya nyama ya nkhumba unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena amadyabe nyama ya nkhumba?
• Nanga lero lino, kodi ndi anthu ati omwe sadya nyama ya nkhumba?
***
Mowa ndi woletsedwa m’Chipangano Chakale komanso m’Chipangano Chatsopano.
Chipangano Chakale “Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova; azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa...” [Numeri 6:1-4]
“Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.” [Miyambo 20:1]
“Kuli kwabwino kusadya nyanma, kapena kusamwa vinyo...” [Aroma 14:21]
ChipanganoChatsopano “Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu...” [Luka 1:15]
Zipangano zones ziwiri zikulongosola momveka bwino kuti mowa ndi woletsedwa. Ngakhale izi zili chonchi, mabuku ena m’Baibulo lomweli amaloleza kumwa mowa. Koma kuti munthu amvetse ndi kudziwa zoona zokhazokha, ayenera kuunika ndime zomwe zimaletsa komanso zomwe zimaloleza mchitidwe womwa mowa zomwe zili m’musizi:
Kodi mowa m’Baibulo, ndiwoletsedwa kapena wololedwa?
Unikani ndikusankha nokha!
Siyanitsani A ndi B
A Wololedwa m’Chipangano Chatsopano | B Woletsedwa m’Chipangano Chatsopano |
I Timoteo 5:23 | Luka 1:15 |
“Usakhalensowakumwa madzi wokha, komatu uchite naye vinyo pang’ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako...” | “Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu...” |
Sizotheka kuti mowa ungakhale wololedwa komanso woletsedwa nthawi imodzi! Apa tikhoza kunena motsindika kuti Baibulo limadzitsutsa lokha. N’zokhumudwitsa kuti kudzitsutsa kwa Baibuloku, kunadza chifukwa cha kusamvetsa bwino malemba a Baibulo kwa alembi, makamaka pa nthawi yomwe amatanthauzira Baibulo kuchokera ku Chigiriki n’kupita muziyankhulo zina. Nazi zitsanzo zina za kutsutsana kwa ndime zina m’Chipangano Chakale komanso Chatsopano. Nthawi ino, mulinso ndi ufulu owunika ndime zotsutsana za m’Baibulo zomwe zikutsatirazi ndi kudzisankhira nokha mbali imodzi:
Siyanitsani A ndi B
Zaka zisanu ndi zitatu kapena khumi mphambu zisanu ndi zitatu?
Chipangano Chakale
A 2 Mbiri 36:5 | B 2 Mafumu 24:8 |
Yehoyakini anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wache.. | Yoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wache.. |
Chipangano Chatsopano
Ndi ndodo kapena opanda ndodo?
A Mateyu 10:9-10 | B Marko 6:8 |
Musadzitengere… kapena thumba la kamba la kunjira kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo… | ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena tumba kapena ndalama m’lamba lao |
Ndime zina zotsutsana m’Baibulo ndi izi:
2 Samueli 24:13 imatsutsana ndi
1 Mbiri 21:11-12
2 Samueli 24:13 | 1 Mbiri 21:11-12 |
Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza , nanena naye, kodi zikugwereni m’dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala ? kapena muthawe adani anu akukuoitikitsani miyezi itatu ?.. | Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko; 12. Kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako |
Numeri 4:3 imatsutsanandi Numeri 8:24
Numeri 4:3 | Numeri 8:24 |
Kuyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako. | Kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu ntchito ya chihema chokomanako. |
Marko 16:2 imatsutsana ndi Yohane 20:1
Marko 16:2 | Yohane 20:1 |
Ndipo anadzamamawa tsiku loyamba la Sabata, litaturuka dzuwa. | Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Mariya wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda. |
Luka 23:26 imatsutsana ndi Yohane 19:16
Luka 23:26 | Yohane 19:16 |
Ndipo popita naye anagwira munthu Simon wa ku Kerene ali kuchokera ku minda namseza iye mtanda aunyamule pambuyo pache pa Yesu | Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Pamenepo anatenga Yesu; ndipo anasenza mtanda yekha.. |
Ndipovuta munthu kudziwa ngati Yehoyakini anali ndi zaka zakubadwa zitatu kapena khumi mphambu zisanu ndi zitatu pamene ankayamba kulamulira. Kulephera kusiyanitsa pakati pa manambala awiriwa, 8 ndi 18, kwachititsanso kuti imodzi mwa ndime zotsutsana ziwirizi ikhale ndi umboni wolakwika. Kusiyanitsa kwa kalembedwe ka liwu kukhozanso kubweretsa kusiyana kwa tanthauzo la liwulo. Mwachitsanzo, kuonjezera sa ku mneni kukhozanso kubweretsa kusiyana m’matanthauzo m’Baibulo, ngati momwe zilili ndi nkhani ija ya mowa komanso nkhani ya ndodo.
Ndiye funso n’kumati: ‘Kodi malembo awiri okha n’kubweretsa mavuto anji ku Baibulo? Ndipo ine ndikuti, akhoza kusintha tanthauzo la lamulo la Mulungu. Mwachitsanzo, lamulo la kuti ‘Usabe’ likhoza kukhala ‘Ube’.
Tsopano tikhoza kunena mosapeneka kuti mowa, womwe umaledzeretsa, suyenera kumwedwa. N’zokhumudwitsa kuti malemba a Chikhrisitu anasinthidwa kotero kuti m’Baibulo muli mawu ambiri otsutsana. Kodi ndani yemwe angaleke kumwa mowa ngati malemba akunena kuti Yesu anasintha madzi kukhala vinyo ndicholinga choti omutsatira ake amwe ndi kusangalala?
Kuloledwa kwa Mowa
Mafunso ambiri; mayankho ochepa!
Nthano yosintha madzi kukhala mowa imapezeka mu Uthenga Wabwino wa Yohane wokha, womwe nthawi zambiri umatsutsana ndi Uthenga Wabwino wina (wa Mateyu, Mariko ndi Luka). Poyamba Mpingo unkadana ndi Uthenga Wabwino wa Yohane, kotero kuti unautcha uthengawu kuti ndi ‘wa m’maluwa. Ndipo chifukwa choti Uthenga Wabwino winawo umafotokoza mofanana momwe moyo wa Yesu unalili, anautcha kuti ndi uthenga ‘weniweni’ [The New Encyclopaedia Britannica Vol 5 pg 379]
• Ngati zili zona kuti Yesu (mtendere ukhale pa iye) anasinthadi madzi kukhala vinyo, nanga ndichifukwa chiyani Luka (Luka 1:15) ndi Paulo (Aroma 14:21), omwe amatchedwa otsatira a Yesu (mtendere ukhale pa iye) analetsa kumwa mowa?
• Uthenga Wabwino wa Yohane sungakhale wolondola ndi wopambana kwambiri kuposa mabuku a Luka ndi Aroma chifukwa uthengawu, malingana ndi anthu ophunzira bwino za Chikhrisitu, unalembedwa mochedwa, mu chaka cha 85 A.D, pamene bukhu la Luka linalembedwa mu 70 A.D, ndipo buku la Aroma linalembedwa mu 56 A.D. Mabuku a Luka ndi Aroma analembedwa moyambirira patatsala zaka za pakati pa 20 ndi 30 kuti buku la Yohane lilembedwe.
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wakusamwa mowa unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena amamwabe mowa?
• Nanga lero lino, ndi anthu ati omwe amatsatirabe lamulo la kuletsa mowa?
***
Azimayi once omwe ankakhala pafupi ndi Yesu (mtendere ukhale pa iye) amabisa tsitsi lawo ndi mpango. Uwu unalinso mchitidwe wa azimayi omwe ankakhala limodzi ndi atumiki oyambirira. Azimayi ankavala zovala zosathina ndi zobisa thupi lonse, kuphatikizapo tsitsi, ndipo nthawi zina, nkhope. Iwo ankachita izi podzisungira ulemu komanso powachitira manyazi anthu achilendo.
“Ndipo Rebeka anatukula maso ache, ndipo pamene anaona Isake anatsika pangamila. Ndipo anati kwa mnyamata, ‘Munthuyo ndani amene ayenda m’munda kukomana ndiife?’ Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.” [Genesis 24:64-65]
Rabeka anafunditsa mutu wake pamaso pa mwamuna osamudziwa chifukwa cha manyazi ndi kufuna kudzisungira ulemu wake. Ngakhale lero lino, azimayi ofuna kudzisungira okha ulemu amachitabe ngati momwe Baibulo likunenera.
“Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.” [1 Akorinto 11:5]
“Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi apfunde.” [1 Akorinto 11:6]
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa azimayi wobitsa thupi lawo podzisungira ulemu unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino azimayi samalemekeza ndi kutsatira mchitidwewu?
• Nanga lero lino, kodi ndi azimayi ati omwe amatsatirabe mchitidwewu?
***
Yesu (mtendere ukhale pa iye), kuphatikizapo anthu omwe ankakhala naye pafupi amalonjerana pofunirana mtendere m’moyo wawo.
“...Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nawo, Mtendere ukhale ndi inu.” [Yohane 20:19]
“Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo: mumuke kwa Nabala ndi kundilankhulira iye; ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu…” [1 Samueli 25:5-6]
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa kulonjerana pofunirana mtendere unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena samalemekeza mchitidwewu?
• Nanga lero lino, ndi anthu ati omwe amatsatirabe mchitidwewu?
***
Katapira ndi ndalama zoonjezera zomwe munthu amapereka pobweza ngongole. Malinga ndi Chipangano Chakale, mchitidwe wa katapira ndi wosavomerezeka.
“Musamakongoletsa m’bale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kali konse kokongoletsa.” [Deuteronomo 23:19]
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa kusachita katapira unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena amachitabe katapira?
• Nanga lero lino, ndi anthu ati omwe sachita mchitidwewu?
***
Mwamuna amakhala pa mitala akakhala pa banja ndi akazi osachepera mmodzi. Atumiki ambiri ankachitanso mitala.
“Ndipo Sarai mkazi wache wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wache wa ku Aigupto, Abramu atakhala m’dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wache, kuti akhale mkazi wache…” [Genesis 16:3]
“Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ache, munthu yense ndi a pabanja pache, inde Davide ndi akazi ache awiri.
[1 Samueli 27:3]
Ndime zina za m’Baibulo zomwe zikuchitira umboni pa nkhani ya mitalayi ndi izi:
“Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri...” [1 Mafumu 11:3]
“Ndipo Rehabiamu anaconda Maaka mwana wa mkazi wa Abisalomu kuposa akazi ache onse, ndi akazi ache ang’ono (pakuti adatenga akazi khumi asanu ndi atatu, ndi akazi ang’ono makumi asanu ndi limodzi...” [2 Mbiri 11:21]
“Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye wina wodana naye, nakam’balira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wa mwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye; pamenepo kudzali, tsiku la kugawira ana ache amuna chuma chake, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, Wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu” [Deuteronomo 21:15-16]
Palibe umboni wina uliwonse womwe umanena kuti Yesu (mtendere ukhale pa iye) analetsa mitala. Yesu (mtendere ukhale pa iye) akanaletsa mchitidwe wa mitala, akadaonetsa ngati akudana ndi zomwe ankachita atumiki omwe analipo iye asanabwere.
Ophunzira bwino za Baibulo avomereza mitala
Bambo Eugene Hillman, m’bukhu lake lotchedwa, ‘Polygamy Reconsidered akulongosola kuti:
“Palibe ngakhale ndime imodzi mu Chipangano Chatsopano momwe muli lamulo lonena kuti mwamuna azikwatira mkazi mmodzi yekha basi.” [Polygamy Reconsidered]
Iye ponena akuti Mpingo (wa Chikhrisitu) ku Rome unathetsa mchitidwe wa mitala ndicholinga chofuna kuti anthu asamachite zosemphana ndi chikhalidwe cha ku Greece ndi Rome chomwe chimalola mwamuna kukwatira mkazi mmodzi yekha basi ngakhale chikhalidwechi sichimaletsa mchitidwe wonyansa wachiwerewere.
Tsopano, munthu aliyense ayenera kulingalira izi:
• Kodi mchitidwe wa kuchita mitala unanka kuti?
• Kodi n’chifukwa chiyani lero lino anthu ena sachita mitala?
• Nanga lero lino, kodi ndi anthu ati omwe amalemekezabe ndi kutsatira mchitidwewu?
Tsopano, tiyenera tifufuze anthu omwe lero lino amalemekeza ndi kutsatira chiphunzitso cha Baibulo. Chipembedzo chomwe chimalemekeza ndi kutsatira chiphunzitso cha Baibulo ndi Chisilamu
CHISILAMU!
Asilamu amanena kuti iwo amatsatira chiphunzitso cha Mtumiki Yesu (mtendere ukhale pa iye) komanso ziphunzitso za atumiki ena a Mulungu omwe analipo Yesu (mtendere ukhale pa iye) asanabwere. Tsopano, tiyeni tione ngatidi izi zili zoona. Takambirana kale za machitidwe a Yesu (mtendere ukhale pa iye), ndipo tsopano tiyenera kusiyanitsa machitidwewa ndi machitidwe a Asilamu.
Bukhu la Qur’an likugwirizana kwatunthu ndi ziphunzitso za m’Baibulo zomwe takambirana kale zija motere:
1. Umodzi wa Mulungu m’Qur’an
Mulungu akuti: “…palibe wina wompembedza mwachoonadi, koma Ine; choncho ndilambireni.” [Qur’an 21:25]
2. Kugwetsa nkhope pansi popemphera m’Qur’an
Mulungu akuti: “Uwaona akugwira m’maondo ndi kugwetsa nkhope zawo pansi ncholinga chofuna zabwino za Mulungu ndi chikondi (chake). Zizindikiro zawo zili pa nkhope zawo zosonyeza kulambira kwawo. [Qur’an 481:291
3. Lamulo lopereka chaulere kwa anthu osowa m’Qur’an
Mulungu akuti: “Akufunsa kuti apereke chiyani? Nena: Chuma chilichonse chimene mungachipereke, (chiperekeni) kwa makolo awiri, achibale, kwa ana amasiye, kwa osauka, ndi kwa apaulendo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, ndithudi, Allah akuchidziwa.” [Qur’an 2:215]
4. Kusala m’Qur’an
Mulungu akuti: “Ee inu amene mwakhulupilira! Kwalamulidwa kwa inu kusala (Ramadhan) monga momwe kudalamulidwira kwa anthu akale inu musadabwere kuti muope Allah (popewa zoletsedwa).” [Qur’an 2:183]
Asilamu alamulidwa kusala kwa masiku makumi atatu (30) m’mwezi wolemekezeka wa Ramadhan. M’mweziwu, iwo saadya, samwa, ndipo sakhalira limodzi mamuna ndi mkazi kuyambira m’bandakucha kufikira kulowa kwa dzuwa.
5. Kuyeretsa ziwalo (mapemphero asanachitike) m’Qur’an
Mulungu akuti: “Ee inu amene mwakhulupilira! Pamene mwaimilira kuti mukaswali, sambitsani nkhope zanu, ndi manja anu mpaka mmagongono; ndipo pakani madzi pamitu panu ndi kusambitsa mapazi anu mpaka mu akakolo.” [Qur’an 5:6]
6. Mdulidwe m’Hadeeth
Mtumiki Muhammad (mtendere ukhale pa iye) akunena kuti:
“Pali zinthu zitatu zomwe ndi machitidwe a atumiki: kulandila mdulidwe, kumeta tsitsi la kumalo obisika, ku khwapa, kuwenga zikhadabo ndi kupungula ndevu za pamphuno. [Al-Bukhari]
Msilamu aliyense wachimuna mpaka lero lino amalandirabe mdulidwe. Iye ayenera kudulidwa pakatha masiku asanu ndi atatu akubadwa kwake, ngati momwe analamulira Mtumiki Muhammad (mtendere ukhale pa iye), yemwe tonse tikudziwa kuti anabwera pambuyo pa Yesu (mtendere ukhale pa iye).
7. Nkhumba, nyama yoletsedwa m’Qur’an
Mulungu akuti: “Kwaletsedwa kwa inu (kudya) chakufa chokha, ndi liwende ndi nyama ya nkhumba, ndi chomwe chazingidwa m’dzina osati la Allah...” [Qur’an 5:3]
8. Mowa, chakumwa choletsedwa m’Qur’an
Mulungu akuti: “Ee, inu amene mwakhulupilira! Ndithudi, mowa (kutchova) njuga, kupembedza mafano ndi kuombeza maula (zonsezi) ndiuve, mwa ntchito za Satana. Choncho, zipeweni kuti mupambane.” [Qur’an 5:90]
9. Kuvala mpango m’mutu kwa azimayi podzilemekeza m’Qur’an
Mulungu akuti: “Ndipo auze Asilamu achikazi kuti adzolitse maso awo ndi kusunga umaliseche wawo. Ndipo asaonetse (poyera zomwe amadzikongoletsa nazo kupatula zimene zaonekera poyera (popanda cholinga chotero). Ndipo afunde kumutu mipango yawo mpaka m’zifuwa zawo...” [Qur’an 24:31]
Chifukwa chomwe Mulungu walamulira azimayi kuti azibisa matupi awo chomwenso chikupezeka m’Quran ndi choti mchitidwewu umasiyanitsa azimayi osakhulupilira ndi okhulupilira, omwe amadzipatsa ulemu povala zovala zosathina ndi zazitali. Mchitidwewu umawateteza azimayi okhulupilirawa kumnyozo wa anthu.
10. Kulonjerana pofunirana mtendere m’Qur’an
Mulungu akuti: “Ee, inu amene mwakhulupilira! Musalowe m’nyumba zomwe sinyumba zanu kufikira mutapempha chilolezo poodira ndi kupereka salaamu kwa eni nyumbazo.” [Qur’an 24:27]
Asilamu amalonjerana pofunirana mtendere wina ndi mzake. Pamene iwo akumana, mmodzi amanena mawu a m’chiArabu oti: ‘As-Salaam alaikum’ kutanthauza kuti ‘Mtendere ukhale ndi inu’. Ndipo mnzakeyo ali okakamizidwa kuyankha kuti: ‘Wa-alay-kumus -salaam (Mtendere ukhalenso ndi inu nomwe)’. Izi ndi zomwenso Yesu (mtendere ukhale pa iye) ankachita.
11. Katapira, mchitidwe woletsedwa m’Qur’an
Mulungu akuti: “Ee! Inu amene mwakhulipilira! Opani Allah, ndipo siyani zimene zatsalira m’katapira, ngati inu mulidi okhulupilira.” [Qur’an 2:278]
12. Mitala, mchitidwe wovomerezeka m’Qur’an
Mulungu akuti: “Ngati mwaopa kuti simungachite chilungamo pa amasiye (opaninso kusawachitira chilungamo akazi pamitala), choncho kwatirani amene mukuwafuna mwa akazi; awiri, kapena atatu, kapena anayi (basi). Koma ngati mukuopa kuti simungathe kuchita chilungamo, (kwatirani) mmodzi basi...” [Qur’an 4:3]
***
Asilamu amanena kuti iwo amalemekeza ndi kutsatira machitidwe a Yesu (mtendere ukhale pa iye), ngati momwe kabukhuka kakulongosolera. Kodi kwa iwowa, Yesu (mtendere ukhale pa iye) ndindani?
Yesu (mtendere ukhale pa iye) ndi mmodzi wa atumiki odziwika bwino a Mulungu. Iye anabadwa mozizwitsa popanda bambo. Iye si mwana wa Mulungu ndipo iye si mmodzi wa ‘utatu wa Mulungu’. Ngakhale iye mwini ananena kuti iye anali mtumiki wa Mulungu, osati mwana Wake. Iye sanafere machimo a munthu wina aliyense. Iye sanapachikidwe pa mtanda, kuphedwa kapena kuukitsidwa kwa akufa, koma anatengedwa ndi Mulungu kupita kumwamba.
Kodi Yesu ankapembedza bwanji?
Momwe Yesu (mtendere ukhale pa iye) ankapembedzera Mulungu zanenedwa kale. Yesu (mtendere ukhale pa iye) ankapembedza Mulungu ngati momwe Asilamu amachitira. Choncho, tikhoza kunena kuti Asilamu amapembedza mofanana ndi momwe anthu amachitira nthawi ya Yesu (mtendere ukhale pa iye). Ichi ndi chifukwa chake Asilamu amanena kuti iwo, osati Akhrisitu alero lino, ndi omwe amatsatira mwachoonadi chipembedzo cha Yesu (mtendere ukhale pa iye). Tikhoza kunenanso kuti omwe ankatsatira Yesu (mtendere ukhale pa iye) mwachoonadi pa chiyambi ndi Asilamu. Akhrisitu alero amamutsatira Yesu (mtendere ukhale pa iye) mu dzina lokha osati m’chipembedzo ngati momwe Asilamu amachitira.
Asilamu amanena kuti iwo ndi otsatira enieni a Yesu (mtendere ukhale pa iye). Nanga chinachitika n’chiyani kuti Chikhrisitu chikhale chosokera?
Yesu (mtendere ukhale pa iye) atachoka pa dziko lapansi, panali anthu ena odalitsika omwe ankatsatira chiphunzitso chenicheni cha Yesu (mtendere ukhale pa iye). Ndipo Muhammad (mtendere ukhale pa iye) atabwera, anthuwa anauzindikira uthenga wake ndipo anaulandira ndi manja awiri. Zofanana zomwe Yesu (mtendere ukhale pa iye) ndi Muhammad (mtendere ukhale pa iye) anali nazo zinawachititsa anthu kuika chikhulupiliro chawo pa Muhammad (mtendere ukhale pa iye). Iwo ankamukhulupilira Muhammad (mtendere ukhale pa iye) kaamba koti kubwera kwake kunalembedwa mu Uthenga Wabwino wa Yesu (mtendere ukhale pa iye). Kubwera kwa Muhammad (mtendere ukhale pa iye) chimodzimodzinso kwa Yesu (mtendere ukhale pa iye), kunaloseredwa ndi Mose (mtendere ukhale pa iye).
Nthawi ya Muhammad (mtendere ukhale pa iye), anthu once omwe sankakhulupilira mwa iye ankachita zosemphana ndi chiphunzitso chenicheni cha Yesu (mtendere ukhale pa iye). Izi zinagawanitsa mpingo, ndi kuchititsa kuti pakhale mitundu yosiyanasiyana ya ma Baibulo padziko. Kusiyana kwa mipingo ndi ma Baibulo ndi umboni wokwanira kwa Akhrisitu woti chipembedzo chawo chimachita zotsemphana ndi chiphunzitso chake choyambilira. Ichi ndi chifukwa chake Asilamu amanena kuti uthenga womwe atumiki once ankalalikira umapezeka m’Chisilamu.
Asilamu amati iwo ndi otsatira enieni a Yesu (mtendere ukhale pa iye). N’chifukwa chiyani iwo samatchedwa Akhrisitu?
M’Baibulo, mulibe malo ngakhale amodzi omwe akunena kuti Yesu (mtendere ukhale pa iye) anazitcha yekha kuti iye ndi Mkhrisitu. Malinga ndi Baibulo, liwu loti ‘Mkhrisitu’ linatchulidwa poitanira Akhrisitu mu chaka cha 43 A.D. basi, ndipo panthawiyi n’kuti Yesu (mtendere ukhale pa iye) anali atatengedwa kale ndi Mulungu kupita kumwamba.
Liwu limeneli linayamba kugwiritsidwa ntchito ndi Ayuda osakhulupilira ku Antiyokeya mu chaka cha 43 A.D. Bukhu la Machitidwe m’Baibulo likuchitirapo umboni pa nkhaniyi motere:
“…ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhrisitu ku Antiokeya.” [Machitidwe 11:26]
Dzinali latchulidwa kachiwiri pa Machitidwe 26:28, ndipo latchulidwa kachitatu pa I Petro 4:16. Tikaphatikizira, dzinali latchulidwa katatu kokha mu Chipangano Chatsopano. Ngakhale izi zili chomwechi, dzinali silinatchulidwepo m’moyo wonse wa Yesu (mtendere ukhale pa iye) pa dziko lapansi.
Kodi pali ubale wanji pakati pa Yesu, Mose ndi Muhammad (mtendere ukhale pa iwo)
Yesu ( mtendere ukhale pa iye) ankalalikira uthenga womwe Mose (mtendere ukhale pa iye) ankalalikira. Chipangano Chakale chinalosera za kubwera kwake, ndipo otsatira a Mose (mtendere ukhale pa iye) amayenera kumutsatira iye. Yesu (mtendere ukhale pa iye) nayenso analosera za kubwera kwa mtumiki wina wotchedwa Muhammad (mtendere ukhale pa iye) yemwe adzabwere pambuyo pake. Otsatira mtumiki aliyense amayenera kutsatira atumiki omwe analonjezedwa m’mabuku awo opatulika chifukwa choti mtumiki wina aliyense amanena kuti anabwera kudzakwaniritsa, osati kudzathetsa, malamulo a mtumiki yemwe analipo iye asanabwere (Mateyu 5:17-18]
Kodi Asilamu amakhulupilira Uthenga Wabwino wa Yesu?
Inde. Asilamu once amakhulupilira uthenga omwe unavumbulutsidwa kwa Yesu (mtendere ukhale pa iye), ndipo ngati iwo satero, ndiye kuti sakhala Asilamu. Uthenga Wabwino wa Mateyu, Marko, Luka ndi Yohane ndi Injeel, Uthenga Wabwino weniweniwa Yesu (mtendere ukhale pa iye). Ngakhale izi zili chonchi, Asilamu amakhulupilira mawu okhawo omwe Qur’an imavomelezana nawo. Asilamu amakhulupiliranso Torah (Bukhu lenileni la Chipangano Chakale lomwe linavumbulutsidwa kwa Mose (mtendere ukhale pa iye).
Kodi Chisilamu chimatanthauza chiyani?
Chisilamu chimatanthauza ‘kugonjera’ mwa Mulungu mmodzi basi, yemwe ali Mlengi wa zonse. ‘Chisilamu’ ndi liwu la chiyankhulo cha chiArabu (Chiluya) ndipo limatanthauza ‘mtendere. Mwachidule Msilamu ndi munthu yemwe amakhazikitsa mtendere pogonjera kuchifuniro cha Mulungu mmodzi.
Kodi Asilamu amapembedza Muhammad (mtendere ukhale pa iye?
Ayi. Asilamu amapembedza Mulungu mmodzi yekha, yemwe ali Mlengi wa zonse. Kwa iwo, Muhammad (mtendere ukhale pa iye) ndi mtumiki wa Mulungu yemwe ankalalikira uthenga woti Mulungu ndi mmodzi yekha. Iyenso mwini wake ankapembedza Mulungu Mmodzi yemweyu.
Kodi Muhammad (mtendere ukhale pa iye) anabwera ndi chipembedzo chatsopano?
Muhammad (mtendere ukhale pa iye), chimodzimodzinso Yesu (mtendere ukhale pa iye), sanabwere kudzafalitsa chipembedzo chatsopano. Iye anabwera kudzaongola ndi kudzakwaniritsa uthenga wa Yesu (mtendere ukhale pa iye) womwe panthawiyi unali utasokonezedwa ndi anthu omwe analipo Yesu (mtendere ukhale pa iye) atachoka. Ichi ndi chifukwa chomwe kuli koyenera kuti anthu azitsatira uthenga wa Chisilamu womwe Muhammad (mtendere ukhale pa iye) ankalalikira chifukwa sungawatengere iwo kuchionongeko. Iwo ayenera kutero ngati akufunadi kukhala okondeka pamaso pa Mulungu komanso Yesu.
Kodi ‘Allah’ ndindani?
Allah ndi dzina la Mulungu mmodzi yekha.
Kodi Chikhulupiliro chomwe chamanga maziko a Chisilamu ndi chiti? Maziko a Chisilamu agona pa kukhulupilira kuti Mulungu ndi mmodzi yekhayo yemwe ali woyenera kupembedzedwa.
Kodi Qur’an ndi Chiyani?
Qur’an ndi mawu enieni a Mulungu omwe anavumbulutsidwa kwa Muhammad (mtendere ukhale pa iye). Ili ndi Buku lokhalo la Mulungu lomwe, kwa zaka zopitilira 1400 tsopano, silinasinthidwepo poonjezera kapena pochotsa liwu ngakhale limodzi lokha. Bukuli likadali m’chiyankhulo chomwe linavumbulutsidwira, cha chiArabu.
Malinga ndi Chisilamu, kuti munthu akapulumutsidwe ayenera kuchita chiyani?
Choyamba, iye afunika kukhulupilira kuti palibe mulungu wina woyenera kupembedzedwa, koma Mulungu Mmodzi yekha, ndiponso afunika kukhulupilira kuti Muhammad (mtendere ukhale pa iye) ndi Mtumiki womaliza wa Mulungu.
Kenako, iye afunika kugwira ntchito zabwino modzipereka kwa Mulungu ndi cholinga chomusangalatsa Iye. Ntchito zabwino zomwe munthu angagwire ndi monga kupereka chaulere kwa osowa, kusala, kupemphera, kusamala amasiye, ndi ntchito zina zotero. Ngati tichimwa m’moyo mwathu n’kulephera kugwira ntchito zotamandika pamasopa Mulungu, tiyenera kulapa kwa Mulungu kuti atikhululukire machimo athu. Munthu ayenera kuvomereza kulakwa kwake asanalape, ndipo kulapa kwakeko kuyenera kukhala kochokeradi pansi pa mtima wake.
***
44
Mukamaliza kuwerenga bukuli, muona kuti ndi Chisilamu chokha chomwe chimalemekeza machitidwe a Yesu (mtendere ukhale pa iye). Mukhalanso mutadziwa kuti Chisilamu si chipembedzo chatsopano. Ichi ndi chipembedzo chomwe chimaika chikhulupiliro mwa Mulungu Mmodzi yekha. Ichinso ndi chipembedzo cha Yesu (mtendere ukhale pa iye) kuphatikizapo atumiki ena omwe analipo iye asanabwere.
Kukhala Msilamu sikutanthauza kuchita chisankho pakati pa Muhammad (mtendere ukhale pa iye) kapena Yesu (mtendere ukhale pa iye). Kukhala Msilamu kumatanthauza kutsatira Yesu (mtendere ukhale pa iye) pochita zomwe ankaphunzitsa Muhammad (mtendere ukhale pa iye), yemwe anabwera kudzakwaniritsa uthenga wa Yesu (mtendere ukhale pa iye).
Ndikupempha Mulungu kuti awakhululukire awerengi athu machismo awo, komanso akachititse bukuli kukhala njira yomwe ingawatengere anthu kuchipulumutso powaunikira chilungamo. Ndikupempha munthu wina aliyense kuti aziwerenga buku lolemekezeka la Qur’an Chifukwa:
• Ndi mawu enieni a Mulungu omwe Iye ankawavumbulutsa pang’onopang’ono kwa zaka 23.
• silidzitsutsa
• limapereka mayankho kumavuto omwe anthu amakumana nawo pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Limalongosolanso za moyo womwe uli mkudza
• ndi buku lokhalo lomwe linayamba kutetezedwa ndi kusungidwa pa mtima ndi anthu miyandamiyanda dziko lonse lapansi kuchokera pamene linavumbulutsidwa kufikira lero lino.
• lili mu chiyankhulo chomwe linavumbulutsidwa, cha chiArabu.
• Matanthauzo ake alibe zolakwika, zoonjezera, kapena zochotsera zina zilizonse.
• Silimatsutsana ndi mfundo zolondola za Sayansi.
• silinasinthidwepo, ndipo limatetezedwa ndi kusungidwa bwino mu chiyankhulo chake chomwe linavumbulutsidwa.
• Limaitanira wina aliyense kuchipembedzo chimodzi chomwe chimapezeka mibado yonse ya anthu.
***