المملكة العربية السعودية

وزارة التعليم العالي

الجامعة الإسلامية بالمدينة المنورة

عمادة خدمة المجتمع

قسم توعية الجاليات

تعريف موجز بالإسلام

(بلغة شيشيوى)

TANTHAWUZO

LACHISILAMU

M’CHICHEWA
بسم الله الرحمن الرحيم

 MUDZINA LAMULUNGU WACHIFUNDO WACHISONI

 CHISILAMU

TANTHAWUZO LACHISILAMU

Choyamba ndikuthokoza Mulungu bwana Wazolengedwa zonse. Mtendere ndi madalistso a Mulungu akhale kwa Mtsogoleri wa Aneneri onse, Mtumiki Wathu Muhammadi pamodzi ndi akubanja kwake, Ophunzira ake ndi omutsatira Onse. Ndikuyikira Umboni kuti palibe Mulungu Wina Koma Mulungu Mmodzi Yekha, Komanso Muhammadi (Mtendere ndi Madalitso a Mulungu a Khale Kwaiye) Ndi Mthenga Wake, Zonsezi Potsimikidza ndi Mtima, Kulankhula ndi lilime Komanso Kugwiritsa ntchito thupi potsatira Malamulo ache.

Zonsezi zimatheka pogwiritsa ntchito nsanamira za lmani (chi khu lupiliro) zomwe zilipo zisanu ndi chimodzi komanso, Nsanamira zisanu zachisilamu ndi Ihsani (kumpembedza Mulungu ngati mkumuwona, ngakale kuti simukumuona koma Iyeyo amakuonani).

 CHISILAMU

Chisilamu ndi uthenga Omaliza mu uthenga Onse wa Mulungu, Umene adawutumiza kwa mneneri wake Omaliza mwa aneneri ndi atumiki ake onse. Ameneyu ndi Muhammadi (mtendere ndi madatitso a Mulungu akhale kwa iye). mwana wa ABDUL-LAHI.

Chimenechi ndi Chipembedzo chowonadi, muchifukwa cha chipembedzochi Mulungu sakalola Chipembedzo china chake kuchokera kwa Munthu wina aliyense posakhala chisilamu. Zowonadi, anachipanga Mulungu kukhala chipembedzo chopepuka ndi chosavuta. Malamulo onse amene ali chipembedzomu ndi wokhawo amene anayikidwa ndi Mulungu kukhala ofewa kwa munthu amene angalowe ndi mtima wake onse. Ndipo Mulungu sanawa lamulile anthu zinthu zothi sangazithe. Chizindikiro chake ndi kulankhula zowona kumene kulipo m’malamulo ake, dziwani kuti malamulo ake onse siaphuzo. Chisilamuchi chayezamila muchilungamo kusonyeza kuti chipembedzochi ndi cholugama chomwe chikufunika m’moyo wa munthu watsikundi tsiku.Chifundo ndiye chikhalidwa cha chisilamu. Chimenechi ndi chipembedzo cholemekezeka chimene chikuwawuza ndi kuwasonyeza anthu kuchita chinthu chaphindu padziko lino lapansi ndi lakumwanba, ndiponso Chikuwachenjeza anthu kuchita chilichonse chosowetsa mtendere wa munthu padziko lapansi lino ndi lakumwanba. Indedi chimenechi ndi chipembedzo chimene Mulungu anachipanga kuti chikonze makhalidwe a anthu ndi kutinso chikhale chikhulupiriro cha anthu onse ndikusiya zikhulupiriro zina. Chimenechi ndi chipembedzo chimene Mulungu anachipanga kuti chigwiritsanitse mitima ndi maganizo a anthu amene adaali osiyana siyana. Mitimayi idapulumutsidwa kuzinthu zoipa ndikuyisonyeza kuzinthu zabwino ndikuyiwongolera kunjira Yowongoka. Chisilamuchi ndi chipembedzo chabwino sichinanene koma zokhazo zimene zili zabwino zokhazokha. Cholinga cha uthenga wa chisilamu ndi kuphunzitsa anthu Zinthu izi:

CHOYAMBA:

Kuwadziwitsa anthu za Mulungu wawo ndi mbiri zake zapamwamba.

CHACHIWIRI:

Kuwayitanira anthu kuti azimpembedza Mulungu m’modzi yeka ndi kutinso asamaphatikize ndi china chake pomupembedza ndi potsatira malamulo a ake muzinthu zimene adalamulira anthu padziko lino lapansi.

CHACHITATU:

Kuwakumbutsa anthu zimene ati akaziwone ndi mathero awo akadzamwalira komanso ndizimene ati akakumane nazo m’manda ndi nthawi yowukitsidwa m’manda ndi nthawi yoti azikawagamula patsiku la chiweruzo ndi malo amene ati akakhale kapena ku mtendere (PARADISO) kapena ku moto (JAHENA).

Titha kunena mwachidule pazimene chisilamu chikuyitanira motere:

(A) NSANAMIRA ZA IMANI (CHIKHULUPIRIRO)

Uku ndiko kukhulupirira nsanamila zisano ndi chimodzi za imani.

NSANAMIRA YOYAMBA: CHIKHULUPIRIRO MWA MULUNGU

Chikhuhipiriro ichi sichingapezeke mpakana pakhalepo zinthu izi kapena kuti pokhapokha munthu akhuhipirire zinthu izi:

CHOYAMBA: ARRUBUBIYA.

ARRUBUBIYA ndi ku khulupirira kuti Mulungu ndi amene amasunga, kusamalira ndi kuyanganira zolengedwa zake kulenga, kupereka chakudya, kupereka m’vula ndizina zambiri zofunika kwa zolengedwa zake.

CHACHIWIRI: AL- ULUHIYYA

AL- ULUHIYYA ndi mbalinso imodzi ya chikhulupiriro kuti Mulungu ndi m’modzi amene ali oyenera kumugwadira ndipo zonse zimene zimapembedzedwa posakhala Mulungu m’modziyo ndizopanda pache.

 CHACHITATU: AL-ASMAA WASSIFAT

AL- ASMAA WASSIFAT ndi mbalinso imodzi ya chikhulipiriro m’mayina onse oyera a Mulungu monga:

MULUNGU NAMALENGA ndi mayinena otero. Ndikukhulupiriranso m’mbiri zonse za Mulungu monga m’mene Anatiwuzira, mwini wache Mulungu ndi mwamene anatiwuzira mtumiki wathu Muhammadi mtendere wa Mulungu ukhale kwa iye.

 NSANAMIRA YACHIWIRI: CHIKHULUPIRIRO MWA ANGERO

Angero ndi akapolo a Mulungu olemekezeka analengedwa ndi Mulungu ndipo amagwadira, kumvera ndi kutsatira malamulo ake ndipo amalamulidwa kugwira ntchito zosiyana siyana. Mwa Angerowa pali GABRIELI amene ntchito yake ndi kutenga mawu a Mulungu ndikupereka kwa atumiki ake.

MIKAEL ndi mngeronso wa Mulungu ntchito yake ndi kutsitsa ndi kugawa mvura.

ISRAFIIL ndi m’ngeronso wa Mulungu amene akuyembekezera kuti azayimbe lipenga lowukira anthu m’manda tsiku lomaliza(QIYAMA).

MALAKAL- MAWUTI ndi m’ngeronso wa Mulungu amene amachotsa miyoyo ya zolongedwa nthawi ya kufa.

 NSANAMIRA YACHITATU: CHIKHULUPIRIRO M‘MABUKHU A MULUNGU:

Mulungu adatsitsa mabukhu kwa atumiki ake m’mabukumu muli chiwongoko ndi mtendere umene ukufunika pa umoyo wa munthu padziko lino lapansi ndi lakumwamba. Mabukhu amene akudziwika ndi awa:

(1) TURA: (OLD TESTAMENT)

Ili ndi bukhu limene adalitumiza Mulungu kwa mtumiki wake Musa(MOSES).Limeneli ndi bukku lalikulu la ana a ISRAELI.

(2) INJEILI: (NEW TESTAMENT)

Ili ndi bukhu limene adalitumiza Mulungu kwa mtumiki wake ISSA (yesu)

(3) ZABUR: (BOOK OF PSALMS)

Ili ndi bukhu limene adalitumiza Mulungu kwa mtumiki wake DAUDI(DAVIDI)

(4) SUHUFU: (SCRIPTURE OF ABRAHAM)

Ili ndi bukhu limene adalitumiza Mulungu kwa mtumiki wake IBRAHIM (ABRAHAM)

(5) QUR-AN:

Ili ndi bukhu lomaliza limene adalitumiza kwa mtumiki wake omaliza MUHAMMAD ndipo Mulungu walisunga kuchisokonezo ndi kusintha kwina kuli konse ndiponso ndi umboni wa anthu onse mpaka tsiku la chiweluzo.

NSANAMIRA YACHINAYI: CHIKHULUPIRIRO MWA ATUMIKI A MULUNGU

Daziwani kuti Mulungu anatumiza kwa anthu onse atumiki, ndipo mtumiki oyamba anali NOWA (NUHU) omaliza ndi mtumiki MUHAMMAD. Atumiki onsewa anali anthu olengedwa analibe chilichonse chosonyeza Umulungu. Iwowa anali akapolo mwa akapolo a Mulungu anawalemekeza powapasta Uthenga wake.Uthenga omaliza ndi wa Muhammadi, iyeyu adamutumiza kwa anthu onse palibenso mtumiki wina pambuyo pake, Mtendere ndi madalitsa a Mulungu akhale kwa atumiki ndi Aneneli ake onse.

NSANAMIRA YACHISANO: CHIKHULUPIRIRO PATSIKU LACHIWERUZO (TSIKU LOMALIZA)

Ili nditsiku palibenso tsiku pambuyo patsikuli.Ili nditsiku limene adzawukisidwa anthu m’manda ali amoyo kuti adzakhale mpaka kalekale kumtendere(PARADISO)kapena ku moto (JEHENA) Tsono chikhulupiriro patsiku lomalizali ndi chikhulupiriro pazonse zimene zimawoneka ndi kukhala pambuyopa infa monga mavuto a mmanda ndi mtendere wake, kuwukisidwa m’manda ndi kuwerengedwa pazintchito zimene wakhala munthu akuchita padziko lino lapansi

NSANAMIRA YA CHISANO NDI CHIMODZI: CHIKHULUPIRIRO PA QADARI ( FATE)

Qadari ndi kukhulupirira kuti Mulungu anadziwa ndipo anaalemba zimene anafuna mu Ufumu wake. chili chonse chopezeka adachipanga ndi kuchilenga Iye mwini Mulungu. Palibe chimene chimachitika kapena kuwoneka pokhapo kuti Mulungu anachidziwa ndi kuchilemba.

(B) NSANAMIRA ZACHISILAMU

Chisilamu chinamangidwa ndi nsanamira zisano, Munthu sangakhale nsilamu mpakana atakhulupirira ndi kugwiritsira ntchito nsanamila zonse zachisilamu:

 NSANAMIRA YOYAMBA: SHAHADA

Uku ndi kuyira umboni kuti palibe Mulungu wina wachowonadi koma Mulungu m’modzi yekha ndipo Muhammadi ndimthenga wa Mulungu. Mawo amenewa amatchedwa kuti ndi SHAHADA amanenedwa ndi munthu amene akulowa mchipembedzochi. Amenewa ndi makiyi a chisilamu ndipo ndi chiyambi chimene chisilamuchi chinamagwidwa. Mawu onena kuti palibe Mulungu wina koma Mulungu m’modzi, akuthandawuza kuti palibe woyenera kumugwadira muchowonadi koma Mulungu m’modzi yeka.Iyeyu ndi Mulungu wowonadi ndipo zonse zimene amazitcha kuti ndi Mulungu posakhala Mulungu amene tikumutchulayu, ndizopanda pache, tikamati Mulungu timathandawuza kuti Umugwadirayo mucho wonadi.

Ndipo tikamati ndikuyikira Umboni kuti Muhammadi ndi mthenga wa Mulungu, ndikuvomereza kuti zonse zimene ananena ndi zowunadi, mukatero muyenera kutsatira malamulo ake ndi kuzitalikira zinthu zonse zimene adaletsa.

NSANAMARA YACHIWIRI: MAPEMPHERO: (SAWALA)

Mapemphero ndi nsanamila yachiwiri yachisilamu. Uku ndikupemphera kasano patsiku.Awa ndi mapemphero amene adalamulira mwini wake Mulungu kuti akhale njira yimodzi yoyandikira munthu kwa Mulungu wake ndi kumamupempha zinthu zachinsisi zomwe munthu safuna kuti wina azidziwe komanso ndi zinthu zina zambiri. Dziwani kuti mapempherowa amamuletsa munthu kuchita zoyipu ndi zonyansa mu mphamwu ya Mulungu. Mapempherowa asanja zonse zabwino mchipembedzo chachisiamu monga chiwongoko cha chikhulupililo chenicheni ndiponso amapeza munthu chifukwa cha mapompherowa mtendere wa mumtima ndi muthupi. Amampangitsa kukhala wa Msangala padziko Lino ndi Tsiku la chimalizo.

 NSANAMIRA YA CHITATU ZAKKA

Ichi ndichopereka chimene amapereka munthu amene ali ndi chuma chomwe chakwana muyeso woperekera kutha kwa chaka chili chonse ndiye chimaperekedwa kwa anthu oyenera, anthu osawuka ndi ena amene amaloledwa kupasidwa chumachi. Munthu amene ali ndi chuma chosakwanira muyeso sakuloledwa kupereka. Choperekachi chikukakamizidwa kwa okhawo anthu amene ali olemera pofuna kukwaniritsa chipemphezo chawo ndikuwonetsa kuzipereka kwawo pa malamulo a Mulungu komanso pofuna kuyeretsa chikhalidwe chawo, kuteteza chuma chawo ndikuzitalikitsa kuzoipa. Choperekachi chimamuyeretsa opereka, kuzoipa powathandiza anthu ovutika ndi osowa. Muyeso wa chuma umene umaperekedwa ndiyochepa kwambiri pofananiza ndi chuma chimene operekayu wapasidwa ndi Mulungu.

 NSANAMIRA YA CHINAYI: KUSALA KUDYA

Kusala Kudya kumachitika mwezi umodzi pa chaka chili chonse. Uwu ndi mwezi wa RAMADHANI mwezi wa chisanu ndi chinayi(9) powerengera chisimukire mutumiki wathu Muhammadi kuchokera ku Makka kupita ku Madinah. Asilamu onse amasiya zilakolako zawo monga kudya ndi kumwa ndi kugona ndi azikazi awo usana kuyambira ku mbanda kucha mpakana kulowa kwa dzuwa. Akatero Mulungu amawapatsa anthu osalawa zinthu zabwino zimene adalonjeza padziko lapansi lino ndila kumwamba. Ndiponso anthuwa akatero amakwanilitsa chipemphezo chawo ndi chikhuhipiriro chawo.

 NSANAMIRA YA CHISANO: HAJJI

Uwu ndi ulendo wa munthu opita ku Nyumba ya Mulungu yoyera. Mulungu anayika lamulo kwa anthu amene angathe kupita ku Makka kamodzi pa moyo wawo. Kumeneko amasonkhana asilamu kuchokera madera onse adziko lapansi lino kupita kumalo amene alioyera ndi abwino padziko lonse lapansi kukapembedza Mulungu mmodzi. Anthu onse amakhala atavala zofanana, palibe kusiyana pakati pa mfumu ndi anthu ake kapena olemera ndi osawuka, wakuda ndi oyera.

Asilamu onse amapanga mapemphero awo limodzi. Mapempherowa amene mkati mwake muli kukayima pamalo otchedwa ARAFAT, kuzungulira nyumba ya Mulungu KABA, kasano ndi kawiri. KABA ndi nyumba ya Mulungu, asilamu onse padziko lino lapansi kuli konse kumene ali nthawi ya mapemphero awo omwe amapempheredwa kasanu patsiku amayangana kunyumbayi, dziwaninso kuti mmapemphero a Hajjiwa muli kupita kukayenda ndawala pakati pa phiri lotchedwa SWAFA ndi phiri lotchedwa MARWA.

(C) Dziwani kuti chisilamu chakonza Umoyo wa munthu aliyenese payekha payekha komanso pagulu ndipo, chimathandiza anthu kuzinthu zimene zingawathandize padziku lino ndi lakumwamba, ndiye chawalola anthu ndi kuwayitanira kuti azikwatira ndi kuwaletsa kuchita chiwelewele ndi kukwatilana amuna okha okha ndi zonse zoipa Ndiponso chikulamulira anthu kulumikiza ubale ndi kuchitirana chifundo, chisoni ndi kusunga anthu asawuka ndi osowa, monga: mmene chikulamulira ndi kuyitanira kuchita chili chonse chinene chili chabwino, chawatetezanso ndikuwaletsa kuchita chinthu choyipa. Chisilamu chikuloleza anthu kupeza zofunikira zamoyo wawo pogwira ntchito kapena malonda amene ali abwino ndi zina zotero. Chikuwaletsanso anthu kuchita katangale ndi malonda onse amene ali oyipa oletsedwa ndi chili chonse chachinyengo. Mulungu amadziwa ndi kuzindikila kusiyana kwa anthu potsatira malamulo ake ndiye anayika chilango kwa anthu kapena munthu aliyense amene angasowetse mtendere wa munthu mzake monga kusokoneza zinthu, kupha, kuba, bodza, kapena kumenya anthu ndi kuwachitira zoipa. Zimenezi ndi zilango za Mulungu zomwe adaziyika molingana ndi tchimo la munthu popamda kuwonjezera kapena kupungula. Chisilamu Chalinganiza zinthu zofunika pakati pa olamula ndi olamulidwa. Chawalamulira olamulidwa kuti ayenera kutsatira malamulo a anthu amene ali olamula posakhala malamulo onyoza Mulungu. Awachenjezanso anthu olamulidwa ndi kuwaletsa kuwagalukira amene akuwalamulira chifukwa kuteroko kumazetsa chisokonezo ndi kusowa mtendere wa anthu m’dziko.

Pomaliza tingathe kunena kuti chisilamu chinabwera kuzakonza zabwino zapakati pa anthu ndi Mulungu wawo ndiponso pakati pa munthu ndi anthu palibe makhalidwe abwino koma kuti chisilamu chalongosola ndikuwa yitanira anthu kuchita ndiponso palibe makhalidwe amene ali oyipa koma kuti chisilamu chachenjeza ndikuletsa. Pomaliza ndikuyamika ndikuthokoza Mulungu bwana wazolengedwa zonse.

 Translated From Arabic to chichewa by

 Bilali Ayami Bwanausi

 From Zambia

 Revised by

 Abdul Rahman Molosi Daudi

 From Malawi

 KINGDOM OF SAUDI ARABIA

 ISLAMIC UNIVERSITY

 OF MADINAH