(1) M’dzina la Allah Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha.
(2) Kutamandidwa konse ndi kwa Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.
(3) Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha.
(4) Mwini tsiku la chiweruziro.
(5) Inu Nokha tikukupembedzani, ndiponso Inu Nokha tikukupemphani chithandizo.
(6) Tiongolereni kunjira yoongoka.
(7) Njira ya omwe mudawapatsa chisomo; osati ya amene adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera.