(1) Nena (iwe Mtumiki (s.a.w), kwa amene akukufunsa mwachipongwe, mbiri za Mulungu wako): “Iye ndi Allah Mmodzi, (alibe mnzake).
(2) Allah ndi Wokhala ndi zonse Wodaliridwa ndi zolengedwa Zake.
(3) Sadabale (mwana) ndiponso sadaberekedwe.
(4) Ndiponso palibe aliyense wofanana ndi Iye.”