95 - At-Tin ()

|

(1) Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona (pansi pa mitengo imeneyi Ibrahim ndi Nuh (Nowa) adapeza uneneri),

(2) Ndi phiri la Sinai (pamene Allah adamulankhulira Mûsa),

(3) Ndiponso mzinda uwu (wolemekezeka) wamtendere; (Makka, womwe adapatsiridwa uneneri Muhammad) (s.a.w).

(4) Palibe chikaiko, tamulenga munthu mkalengedwe kabwino, kolingana (ndipo ali ndi mbiri zabwino).[457]
[457] M’gulu la nyama palibe yopambana kuposa munthu mkalengedwe ndi pa nzeru.

(5) Pambuyo pake tamubwezera pansi kumposa wa pansi.[458]
[458] Munthu ali ndi makhalidwe awiri: Ngati agwiritsa ntchito nzeru zake amaongoka ndipo amaiposa nyama ili yonse. Koma ngati sagwiritsa ntchito nzeru zake amasokera ndi kukhala wapansi kuposa nyama zonse.

(6) Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, adzakhala nawo iwo malipiro osatha.

(7) Tsono nchiyani chakuchititsa kuti ukanire kuuka ndi malipiro pambuyo (poona mphamvu zathu pa chilichonse)?[459]
[459] (Ndime 7-8) Allah akuuza munthu kuti: Pambuyo podziwa kuti Allah ndi Yemwe adapanga zimenezo, ndi chiyani nanga chikumukaikitsa za tsiku la chiweruziro?

(8) Kodi Allah si Muweruzi wa nzeru kuposa aweruzi onse?