77 - Al-Mursalaat ()

|

(1) Ndikulumbilira mphepo yomwe ikuomba motsatizana.

(2) Ndi mphepo yamkuntho ikamakuntha.

(3) Ndi mphepo yobalalitsa mitambo ndi mvula.

(4) Ndi ma Ayah osiyanitsa pakati pachoona ndi chonama;

(5) Ndi angelo opereka chivumbulutso kwa aneneri.

(6) Kuti chichotse madandaulo kapena chikhale chenjezo;

(7) Ndithu zimene mukulonjezedwa (kuti chimaliziro chidzakhalapo) zidzachitikadi (popanda chipeneko),

(8) Pamene nyenyezi zidzafafanizidwa (kuwala kwake ndi kuchotsedwa m’malo mwake).

(9) Ndiponso pamene thambo lidzang‘ambidwa.

(10) Ndi pamenenso mapiri adzachotsedwa m’malo mwake ndi kuperedwa (kukhala fumbi).

(11) Ndi pamene atumiki adzasonkhanitsidwa pa nthawi yake, (kuti apereke umboni ku mibadwo yawo).

(12) Kodi nditsiku lanji azichedwetsera (zinthu zikuluzikulu kuti zidzachitike)?

(13) Nditsiku loweruza (pakati pa zolengedwa).

(14) Nchiyani chingakudziwitse za tsiku la chiweruzirolo?

(15) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).

(16) Kodi sitidawaononge (anthu) akale (chifukwa cha machimo awo, monga anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu)?

(17) Kenako titsatiza ena (okana Allah m’kuonongekako monga tidawachitira oyamba),

(18) Chomwecho tiwachitiranso ochimwa.

(19) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).

(20) Kodi sitidakulengeni kuchokera ku madzi onyozeka, (madzi ambewu ya munthu)?

(21) Kenako tidawaika pamalo okhazikika (kuti chilengedwe chake chikwanire pamenepo),

(22) Mpaka nyengo yodziwika (imene tidaipima kuti mwana abadwe).

(23) Tidaipima nyengoyo; taonani kupima bwino Ife opima!

(24) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).

(25) Kodi sitidaichite nthaka kukhala yofungatira,

(26) Amoyo ndi akufa?

(27) Ndipo tidaika m’menemo mapiri ataliatali (olimbitsa nthaka), ndipo takumwetsani madzi okoma.

(28) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa).

(29) (Kudzanenedwa kwa okana tsiku la chimaliziro:) Pitani kuzimene mudali kuzitsutsa zija.

(30) Pitani kumthunzi (wautsi wa ku Moto) wa nthambi zitatu,

(31) Simthunzi (wamtendere) ndiponso siwotchinjiriza ku malawi a Moto.”

(32) Ndithu motowo umaponya mphalikira (mbaliwali) zazikulu ngati nyumba,

(33) Zonga ngati ngamira zachikasu.

(34) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (zimenezi).

(35) Ili ndi tsiku lomwe sadzayankhula.

(36) Ndipo sadzapatsidwa chilolezo (choyankhulira) kuti apereke madandaulo awo.

(37) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (za tsiku limenelo).

(38) (Adzauzidwa kuti): Ili ndi tsiku loweruza (pakati pa abwino ndi oipa takusonkhanitsani inu (otsutsa Muhammad {s.a.w}), ndi akale (otsutsa aneneri akale).

(39) Ngati muli ndi ndale (yodzipulumutsira ku chilango Changa) ndichiteni ndaleyo!

(40) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo la Allah).

(41) Ndithu oopa (Allah tsiku limenelo) adzakhala mu mthunzi ndi mitsinje,

(42) Ndipo adzakhala ndi zipatso zomwe azidzazifuna.

(43) (Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani, imwani mokondwa chifukwa cha zabwino zomwe mudali kuchita (mu moyo wa dziko lapansi).

(44) Ndithu umo ndi mmene Ife timawalipirira ochita zabwino.

(45) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah)

(46) Idyani, sangalalani pang’ono m’kanthawi kochepa; ndithu inu ndinu ochimwa (chifukwa chakumphatikiza Allah ndi zolengedwa).

(47) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah).

(48) Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Weramani, (pembedzani Allah).” sawerengera.

(49) Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (malamulo a Allah).

(50) Kodi ndi nkhani iti imene adzaikhulupirira pambuyo pa Iyi (Qur’an)?