(1) Hâ-Mîm.
(2) Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka.
(3) Ndithu tidaivumbulutsa (Qur’an) mu usiku wodala. Ife ndithu Ndiachenjezi.
(4) Mu (usiku) umenewu chinthu chilichonse chanzeru chimaweruzidwa ndi kulongosoledwa.
(5) Mwa chilamulo chochokera kwa Ife. Ndithu Ife ndife otumiza atumiki (kuti achenjeze anthu).
(6) (Chifukwa cha) chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Wodziwa kwabasi.
(7) Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli otsimikiza.
(8) Palibe wopembedzedwa moona koma Iye basi. Amapereka moyo ndikupereka imfa, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu oyamba.
(9) Koma iwo (okanira) ali mchikaiko akungosewera, (potsatira zilakolako zawo zoipa).
(10) Basi, yembekezera tsiku limene thambo lidzadze ndi utsi woonekera (konsekonse).
(11) Udzawaphimba anthu onse (ndipo adzakhala akunena:) “Ichi ndi chilango chowawa.
(12) E Mbuye wathu! Tichotsereni chilangochi, ndithu ife tikhulupirira.”
(13) (Kodi lero) kukumbukira kuwapindulira chiyani iwo? Chikhalirecho mtumiki wolongosola chilichonse adawadzera.
(14) Koma sadamlabadire uku akumnena kuti: “Waphunzitsidwa (ndi anthu), ndiponso wopenga.”
(15) Ndithu Ife tichotsa chilangocho pang’ono (koma) inu mubwerezanso (machimo anu).
(16) (Kumbuka, iwe Mtumiki), tsiku limene tidzawalanga chilango chachikulu; ndithu Ife ndife olanga.
(17) Ndipo ndithu iwo asadadze, tidawayesa anthu a Farawo. Ndiponso adawadzera mtumiki wolemekezeka,
(18) Kuti: “Ndipatseni akapolo a Allah. Ndithu ine kwa inu ndi Mtumiki wokhulupirika.”
(19) “Ndipo musadzikweze kwa Allah. Ndithu ine ndikubweretserani chisonyezo choonekera.”
(20) “Ndipo Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye Wanga ndiponso Mbuye wanu (ku chiwembu chofuna kundipha) pondigenda (ndi miyala).”
(21) “Ndipo ngati simundikhulupirira, ndipatukeni (musandivutitse).”
(22) “(Koma adamchitira mtopola). Ndipo iye adaitana Mbuye wake kuti: “Awa ndithu ndi anthu oipa.”
(23) (Allah adamuuza kuti): “Pita ndi akapolo Anga usiku; ndithu inu mulondoledwa.”
(24) “Ndipo isiye nyanja ili momwemo, zii. ndithu iwo ndikhamu (lankhondo) limene limizidwa.”
(25) Kodi ndi minda ingati ndi akasupe zomwe adazisiya atamizidwa!
(26) Ndiponso mmera ndi malo abwino!
(27) Ndi mtendere (waukulu) umene adali kusangalala nawo mmenemo.
(28) Umo ndi mmene zidalili. Ndipo tidawapatsa anthu ena zimenezo.
(29) Thambo ndi nthaka sizidawalilire ndipo sadapatsidwe mpata (wobwereranso pa dziko).
(30) Ndipo ndithu tidapulumutsa ana a Israyeli ku chilango choyalutsa.
(31) Chochokera kwa Farawo; ndithu iye adali wodzikweza ndiponso mmodzi wa opyola malire.
(32) Ndipo ndithu tidawasankha (Ayuda nthawi imeneyo) pa mitundu ina m’kudziwa Kwathu,
(33) Ndipo tidawapatsa zisonyezo (kupyolera m’dzanja la Mûsa) momwe mudali mayeso oonekera poyera kwa iwo.
(34) Ndithu awa (Aquraish) akunena (kuti):
(35) “Palibe china choposera pa imfa yathu yoyambayi, ndipo ife sitidzaukitsidwa.”
(36) “Choncho tibweretsereni makolo athu (amene adafa), ngati mukunena zoona (kuti kuli kuuka).”
(37) Kodi iwo ndi abwino (ndi kupambana pa nyonga), kapena anthu a Tubba (mafumu a kudziko la Yemen) ndi amene adalipo kale iwo asadadze? Tidawaononga. Ndithu iwo adali oipa.
(38) Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zimene zili pakati paizo, mwachibwana.
(39) Sitidalenge ziwirizi koma mwachoonadi; koma anthu ambiri sakudziwa.
(40) Ndithu tsiku lachiweruziro ndiyo nthawi yawo onse (imene alonjezedwa).
(41) Tsiku limene m’bale sadzathandiza m’bale wake pa chilichonse (ku chilango cha Allah), ngakhale iwo sadzapulumutsidwa.
(42) Kupatula amene Allah adzawachitira chifundo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwachisoni chosatha.
(43) Ndithu mtengo wa Zakkumi.
(44) Ndi chakudya cha ochimwa.
(45) (Kutentha kwake) ngati mtovu wosungunulidwa, (wotentha kwambiri;) udzakhala ukuwira mmimba.
(46) Monga kuwira kwa madzi otentha kwambiri.
(47) (Kudzanenedwa): “Mgwireni; mkokereni (ndi kumponya) pakatikati pa Jahena!”
(48) “Kenako mthireni pamwamba pamutu wake chilango chamadzi otentha!”
(49) (Adzauzidwa mwachipongwe): “Lawa! Ndithu iwe ndiwe wamphamvu zambiri, wolemekezeka, (monga momwe udali kudzitamira muja).”
(50) “Ndithu izi ndi zimene mudali kuzikaikira zija!”
(51) Ndithu oopa Allah adzakhala pa malo a chitetezo.
(52) Mminda ndi mu akasupe.
(53) Adzavala (nsalu) za silika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atayang’anizana (nkhope).
(54) Umo ndi mmene zidzakhalire; ndipo tidzawakwatitsa ndi akazi okongola amaso aakulu.
(55) Mmenemo adzakhala akuitanitsa mtundu uliwonse wa zipatso, mwamtendere;
(56) Sadzalawa imfa mmenemo, kupatula imfa yoyamba ija; ndipo adzawateteza kuchilango cha Jahena,
(57) Chifundo chochokera kwa Mbuye wako! Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu!
(58) Ndithu taifewetsa (Qur’an) mchiyankhulo chako (cha Chiarabu) kuti akumbukire.
(59) Choncho yembekeza; iwonso akuyembekezera, (kodi ndani chimtsikire chilango pakati panu).