86 - At-Taariq ()

|

(1) Ndikulumbilira ku mwamba ndi Nyenyezi imene imadza usiku,

(2) Chitakudziwitse nchiyani za Nyenyezi yodza usikuyo?

(3) Imeneyo ndi nyenyezi yowala kwambiri (mu mdima).

(4) Ndithudi palibe mzimu uliwonse koma uli ndi msungi wake (amene akuuyang’anira ndikulemba zonse zochita zake).

(5) Aganizire munthu, kodi adalengedwa kuchokera kuchiyani?

(6) Adalengedwa kuchokera ku madzi ofwamphuka.

(7) Amatuluka kuchokera pakati pa mafupa a msana (wa mwamuna) ndi chifuwa (cha mkazi).

(8) Ndithu Iye ndiwakutha, kumbwezeranso (ku moyo pa mbuyo pa imfa).

(9) Tsiku limene zobisika zonse zidzaonekera poyera.

(10) Munthu sadzakhala ndi mphamvu (tsiku limenelo zodzitetezera iye mwini) ndiponso sadzakhala ndi mtetezi.

(11) Ndikulumbiliranso mitambo yobweretsabweretsa mvula.

(12) Ndi nthaka imene imang’ambika (potulutsa m’mera),

(13) Ndithudi iyi (Qur’an) ndi mawu olekanitsa (Haqq ndi Bâtwil - choona ndi chonama).

(14) Imeneyi sinkhambakamwa.

(15) Ndithudi iwo akukonza chiwembu.[416]
[416] (Ndime15-16) Tanthauzo lake ndikuti akafiri (osakhulupilira) akuchita ndale kuti azimitse dangalira la Qur’an ndikuyesetsa kuti awabweze amene adakhulupilira ndiponso ndikufuna kumupha Mneneri (s.a.w). Naye Allah akuwachitira ndale powaonongera ziwembu zawo zomwe amazikonza.

(16) Nanenso ndikuwakonzera chiwembu (champhamvu kwambiri chimene sangathe kuchipewa).

(17) Basi, apatse nthawi osakhulupirira apatse nthawi pang’ono, (aona posachedwa).