100 - Al-Aadiyaat ()

|

(1) Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma,

(2) Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m’miyala),

(3) Ndi othira nkhondo adani mmawa (dzuwa lisadatuluke),

(4) Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo,

(5) Ndikulowelera mkatikati mwa adani.

(6) Ndithu munthu ali wokanira Mbuye wake, (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo).[472]
[472] Tanthauzo la “kukanira Mbuye wake” ndi kuukanira mtendere Wake. Ndipo kukanira mtendere ndiko kusagwiritsira ntchito mtenderewo mnjira zabwino, monga m’mapemphero ndi zina zotero.

(7) Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake).

(8) Ndipo ndithu iye ndiwokonda chuma kwambiri (ndiponso ngwamsulizo).[473]
[473] Kapena kuti ali wofunitsitsa chuma kwambiri; kumeneko ndikumangoti mtima dyokodyoko pachuma. Ukachipeza ndikumachichitira umbombo ndipo ndikumaganiza kuti chumacho nchopambana china chilichonse.

(9) Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za m’manda,

(10) Ndikudzasonkhanitsidwa ndi kuonekera poyera zomwe zidali m’mitima?

(11) Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).[474]
[474] “Kuwadziwa kwambiri,” kukutanthauza kuti Iye ngodziwa zazikuluzikulu ndi zazing’onozing’ono zoonekera poyera ndi zobisika. Tsiku limenelo adzawalipira chilichonse chimene adachita.