(1) Pamene thambo lidzasweke,[397]
[397] Kuyambira pa Ayah 1 mpaka 4, Allah akutisonyeza zododometsa zina za tsiku lachimaliziro.
(2) Ndi pamene nyenyezi zidzayoyoke (ndi kumwazikana),
(3) Pamenenso nyanja zikuluzikulu zidzaphwasulidwe.
(4) Ndiponso pamene manda adzafukulidwe (ndikutuluka akufa omwe adali mmenemo),
(5) (Panthawiyo) mzimu uliwonse udzadziwa zimene udatsogoza (zabwino ndi zoipa) ndi zimene udasiya m’mbuyo.[398]
[398] Munthu aliyense pa tsiku limenelo adzadziwa zimene adachita, zabwino ndi zoipa.
(6) E iwe munthu! Nchiani chakunyenga kumsiya Mbuye wako wa ufulu (kufikira pomnyoza)?
(7) Amene adalenga iwe nakulinganiza (ziwalo zako) ndi kukulongosola (moyenera);
(8) Ndipo maonekedwe amtundu uliwonse omwe adawafuna adakuveka (popanda chifuniro chako).
(9) Ayi, sichoncho! Koma inu mukutsutsa za (tsiku) lamalipiro.
(10) Ndithu pa inu alipo okuyang’ anirani,[399]
[399] Munthu aliyense ali nawo angelo awiri, Rakibu ndi Atidu. Ntchito zawo ndi kulemba ntchito za munthu, zabwino ndi zoipa zomwe.
(11) Olemekezeka, olemba (zochita zanu.)
(12) Akudziwa (zonse) zimene mukuchita (zabwino ndi zoipa).
(13) Ndithudi ochita zabwino adzakhala mu mtendere.
(14) Ndipo ndithu amene ali olakwira malamulo a Allah adzakhala ku Moto wopsereza.
(15) Adzaulowa tsiku la malipiro.
(16) Ndipo iwo kumeneko sadzachokako.
(17) Kodi nchiyani chingakudziwitse za tsiku la malipiro?
(18) Ndipo nchiyani chingakudziwitse za tsiku lamalipiro?
(19) Limeneli ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzakhala ndi mphamvu (yodzetsa mtendere kapena yochotsa chovuta) pa mzimu wina. Ndipo lamulo pa tsiku limeneli ndi la Allah yekha.[400]
[400] Tanthauzo lake ndikuti tsiku limenelo sipadzakhala munthu wotha kumthandiza mnzake pa chilichonse ndiponso palibe adzakhale ndi mphamvu zolamula kupatula Allah yekha.