56 - Al-Waaqia ()

|

(1) Chikadzachitika chochitikacho (Qiyâma).

(2) Palibe wotsutsa za kuchitika kwake.

(3) Chidzatsitsa (oipa) ndi kutukula (abwino).

(4) Nthaka ikadzagwedezeka kwamphamvu.

(5) Ndipo mapiri akadzaperedwaperedwa.

(6) Nkukhala fumbi longouluka.

(7) Choncho, inu mudzakhala m’magulu atatu (kulingana ndi zochita zanu).

(8) Anthu akumanja (abwino;) taonani kukula kwa ulemelero wa anthu akumanja!

(9) Ndi anthu akumanzere (oipa;) taonani kuipa khalidwe la anthu akumanzere!

(10) Ndipo otsogola (pochita zabwino pa dziko) adzakhalanso otsogola (polandira ulemu tsiku lachimaliziro).

(11) Iwowo ndioyandikitsidwa (kwa Allah).

(12) M’minda yamtendere.

(13) (Iwowo oyandikitsidwawo), gulu lalikulu lochokera kumibadwo yakale.

(14) Ndipo ochepa ochokera ku mbadwo wotsirizira.

(15) Uku ali m’makama (m’mabedi) olukidwa ndi zingwe zagolide,

(16) Atatsamira m’makamawo uku akuyang’anizana (mwachikondi).

(17) Anyamata osasintha adzakhala akuwazungulira iwo (ndi kuwatumikira).

(18) Uku atatenga matambula ndi maketulo (odzaza ndi zakumwa za ku Jannah), ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa zochokera mu akasupe oyenda;

(19) (Zakumwa zake) zosapweteketsa mutu ndiponso zosaledzeretsa;

(20) Ndi zipatso (zamitundumitundu) zimene azikazisankha;

(21) Ndi nyama yambalame imene mitima yawo izikafuna;

(22) Ndi akazi ophanuka maso mokongola,

(23) (Kukongola kwawo) ndiye ngati ngale zosungidwa bwino mzigoba zake.

(24) Kukhala mphoto chifukwa cha zimene amachita (zabwino padziko lapansi).

(25) M’menemo sakamva mawu achabe ngakhale (mawu a) machimo,

(26) Koma mawu oti: “Mtendere! Mtendere!”

(27) Anthu akudzanja lamanja. Taonani kukula malipiro a anthu akudzanja lamanja!

(28) (Adzakhala m’mithunzi ya) mitengo ya masawu yopanda minga.

(29) Ndi mitengo ya nthochi yobereka kwambiri.

(30) Ndi m’mithunzi yotambasuka kwambiri, yosachoka,

(31) Ndi madzi oyenda mosalekeza,

(32) Ndi zipatso zambiri,

(33) Zopezeka mnyengo zonse, ndiponso zosaletsedwa (kwa amene akuzifuna).

(34) Ndi zoyala zapamwamba (zawofuwofu).

(35) Ndithu tidzawalenga (akazi okhulupirira) m’kalengedwe kapamwamba.

(36) Tidzawapanga kukhala anamwali.

(37) Okondedwa ndi amuna awo; ofanana misinkhu,

(38) A anthu akudzanja la manja.

(39) Gulu lalikulu lochokera ku m’badwo woyamba.

(40) Ndiponso gulu lalikulu lochokera ku mibadwo yotsiriza.

(41) Anthu akudzanja lakumanzere. Taonani chilango choopsa kwa anthu akudzanja lakumanzere!

(42) Adzakhala mu mvuchi wamoto ndi m’madzi owira.

(43) Ndi mumthunzi wa utsi wakuda.

(44) Siwoziziritsa ndiponso siwosangalatsa.

(45) Ndithu iwo amakhala kalelo mosangalala (samalabadira kumvera Allah),

(46) Ndipo amapitiriza kuchita machimo aakulu (polinga kuti palibe kuuka ku imfa).

(47) Ndipo amanena (motsutsa); “Kodi tikadzafa nkusanduka fumbi ndi mafupa ofumbwa, tidzaukitsidwanso?”

(48) “Kodi ndi makolo athu akale (adzaukitsidwanso!)

(49) Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo). Ndithudi, amibadwo yoyamba ndi mibadwo yomaliza (omwe inu muli m’gulu lawo),

(50) Adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya tsiku lomwe lakhazikitsidwa.

(51) Kenako inu osokera (njira yachilungamo), otsutsa (za kuuka,)

(52) Mudzadya (ku Jahannam) mtengo wa Zakkum, (mtengo wowawa wopezeka mu Jahannam).

(53) Mudzakhutitsa mimba zanu ndi umenewu (chifukwa cha njala yadzaoneni).

(54) (Mkhuto wa mtengowo) adzamwera madzi owira;

(55) Adzamwa monga mmene imamwera ngamira yodwala matenda aludzu!

(56) Ili ndi phwando lawo tsiku lamalipiro.

(57) Ife tidakulengani kodi nchifukwa ninji simukukhulupirira?

(58) Tandiuzani za madzi (ambewu ya munthu) amene mumawathira m’chiberekero,

(59) Kodi inu ndiamene mumawalenga (madziwo ndi kumayang’anira mkusinthasintha kwake kuti akhale cholengedwa) kapena Ife ndiamene timawalenga?

(60) Ife tidalamula imfa pakati panu ndipo Ife sitili wolephera,

(61) Kubweretsa ena m’malo mwanu ndi kukulengani mwamaonekedwe ena omwe simumawadziwa.

(62) Ndipo ndithu mukdziwa kalengedwe koyamba; nanga bwanji simukukumbukira.

(63) Tandiuzani za zimene mukubzala?

(64) Kodi ndinu amene mukuzimeretsa kapena ndife Amene tikuzimeretsa?

(65) Tikadafuna tikadazitembenuza (mbewu zimenezo kukhala zouma isanakwane nthawi yake yozithyola) choncho mukadakhala mukudandaula.

(66) (Uku mukunena:) “Ndithu ife tangotaya chuma chathu (padera);”

(67) “Koma ife tamanidwa (phindu la khama lathu).”

(68) Kodi mukuwaona madzi amene mukumwa!

(69) Kodi ndinu amene mudawatsitsa ku mitambo kapena ndife Amene timawatsitsa?

(70) Tikadafuna tikadawapanga kukhala amchere; nanga nchifukwa ninji simuthokoza?

(71) Kodi mukuwuona moto umene mumaukoleza?

(72) Kodi ndinu amene mudameretsa mitengo yake kapena Ndife tidaipanga?

(73) Ife taupanga kuti ukhale chikumbutso (cha Moto watsiku lachimaliziro akauona), ndikuti ukhale chothandiza kwa anthu apaulendo (amene akuyenda m’chipululu).

(74) Choncho, pitiriza kulemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu.

(75) Ndikulumbilira motsimikiza, mmene mumatsikira nyenyezi (pomwe zikulowa).

(76) Ndithu kulumbira uku, mukadakhala olingalira, nkwakukulu kwabasi (pazimene kukusonya).

(77) Ndithu iyi ndi Qur’an yolemekezeka (ndipo mkati mwake muli zithandizo zambiri).

(78) Idachokera mu buku lotetezedwa.

(79) Salikhudza kupatula okhawo oyeretsedwa (angelo).

(80) Chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.

(81) Kodi nkhani iyi (ya Qur’an) ndiyomwe inu mukuinyozera?

(82) Kodi mwakuchita kukanira kukhala kuthokoza kwanu pa zimene wakupatsani?

(83) Mmaona bwanji (mzimu wa mmodzi wa inu) ukafika kummero (panthawi ya imfa).

(84) Uku inu panthawi imeneyo mukuona zimenezo.

(85) Pomwe Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu, koma inu simuona,

(86) Mukadakhala kuti simuzalipidwa (pa zomwe mukuchita),

(87) Bwenzi mukuubweza (mzimuwo) ngati mukunena zoona.

(88) Ngati (amene yamfikira imfayo) adali mmodzi wa woyandikitsidwa (kwa Allah;)

(89) Kobwerera kwake ndi kumpumulo ndi mtendere ndi kupatsidwa zonunkhira ndiponso Munda wamtendere.

(90) Ndipo ngati adali mmodzi wa anthu akudzanja lamanja,

(91) (Kudzanenedwa kwa iye:) “Mtendere ukhale pa iwe, amene udali m’gulu la anthu akudzanja lakumanja (anthu abwino).”

(92) Koma ngati adali mmodzi wa anthu otsutsa, osokera,

(93) Phwando lamadzi owira (ndilake).

(94) Ndi kupsa m’moto wa Jahena.

(95) Ndithu izi ndizoona, zotsimikizika.

(96) Choncho lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu.