83 - Al-Mutaffifin ()

|

(1) Kuonongeka koopsa kukawapeza opunguza miyeso ya malonda.

(2) Amene amati akamadziyezera zinthu kwa anthu amafuna kulandira miyeso yodzadza.

(3) Koma pamene iwo akamawayesera pa muyeso wa mbale kapena wa sikelo amapungula (choyenera kulandira ogulawo).

(4) Kodi amenewa (akupungula miyeso pamalondawo) sakuganiza kuti adzaukitsidwa;

(5) Pa tsiku lalikulu (ndiponso loopsa)?

(6) Tsiku limene adzaimilira anthu pamaso pa Mbuye wa zolengedwa.

(7) Ayi! Ndithu (siyani chinyengo pamalonda ndi kusalabadira kuuka mmanda); zolembedwa za ntchito ya oipa zili mu Sijjin.

(8) Nanga nchiyani chitakudziwitse za Sijjin?

(9) Ameneyu ndi kaundula wamkulu yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu oipa).

(10) Chilango chaukali tsiku limenelo chili pa otsutsa,[401]
[401] Kutsutsa kulipo kwa mitundu itatu: (a) Kutsutsa kwa mawu ndi zochita; (b) Kutsutsa kwa zochita zokha, monga ukauzidwa kuti chinthu ichi nchoipa, munthu nkudziwa kuti zoona nchoipadi koma nkudzachichita chimenecho mosalabadira; (c) Kutsutsa ndi zolankhula zokha. Kumeneko ndiko monga munthu akudziwa kuti chakutichakuti ncholetsedwa (haramu) koma m’malo mwake iye nkumati chimenecho nchovomerezeka (halali)

(11) Amene akutsutsa za tsiku la malipiro.

(12) Ndipo palibe angalitsutse koma yekhayo wopyola malire (pochita zoipa), wa machimo ambiri;

(13) Pamene ma Ayah Athu akuwerengedwa kwa iye (onena za tsiku la malipiro ndikuuka mmanda) amanena kuti: “Izi ndi nthano za anthu akale.”

(14) Iyayi, sichoncho! Koma yaphimbidwa mitima yawo ndi dzimbiri (la machimo) omwe akhala akukolola.[402]
[402] Munthu akachita choipa koyamba ndipo osalapa, limalowa dontho lakuda mu mtima mwake; nthawi iliyonse pamene akuonjezera machimo, dontho lija limakulirakulira mpaka kuuphimba mtima wonse. Dontho limeneli ndilo likutchedwa “Ran.” Tsono mtima ngati utaphimbidwa chotere sulabadira kuchita zoipa, ngakhale kuti auongole sungaongoke.

(15) Ayi ndithu iwo (okanira) tsiku limenelo) adzatchingidwa kwa Mbuye wawo; (sadzamuona).

(16) Pambuyo pake adzalowa ku Moto; (oyaka)

(17) Kenaka adzauzidwa (powaliritsa) “Ichi nchilango chomwe mudali kuchitsutsa (pa dziko lapansi).”

(18) Zoona, ndithu kaundula wa anthu abwino (ochita ntchito zabwino) ali mu Illiyyun.

(19) Nanga nchiyani chitakudziwitse za Illiyyun?

(20) Ameneyu ndi kaundula (wamkulu) yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu abwino);

(21) Amamuyikira umboni (angelo) amene ayandikitsidwa (kwa Allah).

(22) Ndithu ochita zabwino adzakhala mu mtendere,

(23) Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (zimene Allah wawapatsa monga mtendere ndi ulemelero).

(24) Udzaona kuwala kwa mtendere pa nkhope zawo;

(25) Adzamwetsedwa vinyo (woyeretsedwa) wotsekeredwa ndi zitsekerero zolimba;

(26) Komalizira kwake (kwa vinyoyo) kuzikatuluka fungo la misk; kuti akapeze zimenezi, apikisane opikisana.[403]
[403] Apa, akutilamula kupikisana pakuchita zabwino kuti tipeze madalitso amene awakonzera anthu abwino. Kumeneko ndikuti munthu aliyense alimbikire kuchita mapemphero ndi zina zabwino.

(27) Ndipo chosakanizira cha vinyoyo ndi madzi a Tasnim.

(28) (Tasnim ameneyo) ndi kasupe amene azikamwa amene ayandikitsidwa (kwa Allah.)

(29) Ndithu amene adachita machimo adali kuwaseka (mwachipongwe) okhulupirira (pa dziko lapansi);

(30) (Okhulupirira) akadutsa pafupi ndi iwo ankakodolerana maso (mwachipongwe);

(31) Ndipo akabwerera kwa anzawo amabwerera akusangalala (ndi kunyozedwa kwa okhulupirira);

(32) Ndipo (nthawi zonse) akawaona Asilamu amanena: “Ndithu awa ndi osokera (chifukwa chomkhulupirira Mtumiki).” (s.a.w)

(33) Sanatumizidwe (Akafiri) kukhala ayang’aniri kwa okhulupirira (ndikuwaweruza zakulungama ndi kusokera).

(34) Basi lero okhulupirira awaseka osakhulupirira (powabwezera chipongwe chawo chimene ankachita pa dziko lapansi),[404]
[404] (Ndime 34-36) Tanthauzo lake ndikuti okhulupilira, tsiku lachimaliziro adzakhala m’mipando ya ulemu uku akuwayang’ana ndi kuwaseka anthu osakhulupilira ali m’mavuto monga momwe iwo adali kuseka okhulupilira pa dziko lapansi.

(35) Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (mtendere umene Allah wawapatsa).

(36) Kodi alipidwa osakhulupirira pa zomwe ankachita zija (pa dziko lapansi)?