101 - Al-Qaari'a ()

|

(1) Kugunda kwa phokoso (la Qiyâma)!

(2) Kodi kugunda kwa phokosolo ndi chiyani?

(3) Ndichiyani chingakudziwitse za kugunda kwa phokoso (la Qiyâma komwe kudzawakomole anthu)?

(4) Limenelo ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika.[475]
[475] Apa, pakutanthauza kuti anthu adzakhala ali balalabalala ngati agulugufe ndipo azidzangodziponya uku ndi uku, osadziwa kopita. Imeneyo ndi nthawi yotuluka m’manda.

(5) Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya womwazidwa (wongouluka uku ndi uku mumlengalenga).

(6) Tsono amene muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzalemere (ndikupepuka zoipa).[476]
[476] Tsiku limenelo ntchito zonse zabwino ndi zoipa zidzayesedwa ndi muyeso wa Allah, koma sitidadziwitsidwe kuti muyeso umenewo udzakhala wotani udzayesa zonse zazikulu ndi zazing’ono zomwe mpaka za mumtima.

(7) Ndiye kuti iye adzakhala mu umoyo wosangalatsa (patsiku la chiweruziro).

(8) Ndipo yemwe muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzapepuka (ndi kulemera zoipa),

(9) Ndiye kuti mbuto yake ndi ku Hawiya.

(10) Kodi ndi chiyani chingakudziwitse za Hawiya?

(11) Umenewo ndi Moto woyaka mwa ukali!