(1) Kwakutangwanitsani kusonkhanitsa (chuma chambiri ndi ana).[477]
[477] (Ndime 1-2) Ndi chizolowezi cha anthu kupikisana pa chuma ndi pa ana. Choncho, mma Ayah awa: 1-2 Allah akuwauza: Kupikisana kwawo kochuluka, kukonda za m’dziko kwambiri, kwaiwalitsa kutumikira Allah mpaka imfa kuwapeza.
(2) Mpakana mwapita kumanda (mwamwalira ndikukalowa m’manda).
(3) Sichoncho! Mudziwa posachedwapa.[478]
[478] Tanthauzo lake ndilakuti, pamene idzakufikirani imfa mudzadziwa kuti mudali kutaya nthawi ndi zinthu zopanda pake.
(4) Ndiponso sichoncho! Mudziwa posachedwapa.
(5) Sichoncho! mukadakhala mukudziwa, kudziwa kwachitsimikizo (sibwenzi mukutangwanika ndi za mdziko).
(6) Ndithudi mudzauona Moto.
(7) Kenako mudzauona ndithu ndi diso lachitsimikizo.
(8) Tsono patsikulo ndithudi mudzafunsidwa za mtendere (omwe munapatsidwa).[479]
[479] Munthu aliyense ndi chilichonse chimene ali nacho ndi mphatso yochokera kwa Allah. Choncho, pa tsiku lachimaliziro adzafunsidwa za momwe adagwiritsira ntchito mphatso zimenezi, kaya m’njira yoipa kapena yabwino.