108 - Al-Kawthar ()

|

(1) “Ndithu takupatsa zabwino zambiri (zina mwa izo ndi mtsinje wotchedwa Kauthar).
Surayi ndi yotsatirayi, zidavumbulutsidwa nthawi imodzi. Koma pali kutsutsana; ena akuti zidavumbulutsidwa ku Makka pomwe ena akuti zidavumbulutsidwa ku Madina. Sura ziwirizi zikutiphunzitsa m’mene tingadziikire mchitetezo cha Allah, ndiponso tikuphunzitsidwa kuti Iye (Allah) ndi mwini mphamvu zonse. Atha kumuteteza munthu kuchinthu chilichonse chifukwa chakuti Iye (Allah) ndi Mlengi wa chinthu chilichonse. Choncho, yemwe asiya chitetezo Chake ndikumafuna chitetezo cha ufiti, azimu, manda, ndi zina zotero ndiye kuti akuziika iye mwini kumachitidwe a “SHIRIK” (kupembedza mafano).

(2) “(Pakuti ndakupatsa zimenezo), pitiriza kupembedza Mbuye wako (moyera mtima) ndipo ipha nsembe yako (chifukwa chakuthokoza Allah pa zimene wakupatsa, monga ulemelero ndikukusankhira zabwino zambiri).
“Zomwe adalenga” zikutanthauza chilichonse cholengedwa, chamoyo ndi chopanda moyo; chooneka ndi chosaoneka.

(3) “Ndithu mdani wako ndiye ali wopanda mwawi.
Palibe chikaiko, usiku wa mdima uli ndi zoopsa zambiri zomwe sizipezeka masana ndi usiku wowala. Mu usiku wa mdima, mumayenda zinthu zoopsa zambiri, monga zirombo zolusa, akuba, achiwembu ndi zina zambiri. Kukacha zonsezi zimabisala koma kukada zimatuluka.