45 - Al-Jaathiya ()

|

(1) “Hâ-Mîm.

(2) “Chivumbulutso cha buku (ili) chochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.

(3) “Ndithu kuthambo ndi m’nthaka muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa okhulupirira.

(4) “Ndiponso mkalengedwe kanu ndi zimene wazifalitsa mmenemo, mu zamoyo ndizisonyezo kwa anthu amene akutsimikiza.

(5) “Ndi kusinthana kwa usana ndi usiku, ndi mvula imene Allah akutsitsa kuchokera kumwamba, akuukitsa nthaka ndi mvulayo, itafa (itauma), ndi kuyendetsa mphepo mosinthasintha; (zonsezi) ndi zisonyezo kwa anthu anzeru.

(6) “Izi ndi Ayah (ndime) za Allah; tikukuwerengera iwe mwachoonadi. Kodi ndi nkhani yanji adzaikhulupirire atapanda kulabadira nkhani ya Allah ndi Ayah Zake?

(7) “Kuonongeka kuli pa aliyense wopeka zinthu, wamachimo ambiri.

(8) “Amene akumva Ayah za Allah zikuwerengedwa kwa iye kenako nkumapitiriza (zochita zake zosalungama) uku akudzikweza ngati kuti sadazimve ayazo; muuze nkhani ya chilango chowawa.

(9) “Ndipo akadziwa chinthu chochepa chochokera mma Ayah athu, amachichitira chipongwe; amenewa ndi amene adzakhala ndi chilango chosambula.

(10) “Jahannam ili (kuwayembekezera) kuseri kwawo; ndipo zimene adachita sizidzawathandiza chilichonse, ngakhale atetezi amene adadzipangira kusiya Allah (sadzawathandiza); ndipo adzapeza chilango chachikulu.

(11) “Ichi ndi chiongoko; ndipo amene adakanira Ayah za Mbuye wawo, adzakhala ndi chilango chachikulu chochokera mchilango chowawa.

(12) “Allah ndi Amene wakugonjetserani nyanja kuti zombo ziziyenda mmenemo mwa lamulo Lake; ndikuti munke mufunafuna chifundo Chake kuti muthokoze.

(13) “Ndipo wakugonjetserani za kumwamba ndi zam’nthaka, zonse zikuchokera kwa Iye. Ndithu mzimenezo muli zisonyezo kwa anthu amene amalingalira.

(14) “Nena kwa amene akhulupirira kuti awakhululukire amene sakuopa masiku a Allah (a chilango; mmasiku amenewo) kuti awalipire anthu pa zomwe amachita (zoipa).

(15) “Amene akuchita chabwino akudzichitira yekha ndipo amene akuchita zoipa, zidzakhala paiye mwini. Kenako m’dzabwezedwa kwa Mbuye wanu.

(16) “Ndithu tidawapatsa ana a Israyeli buku, ulamuliro ndi uneneri; ndiponso tidawapatsa zina mwa zinthu zabwino ndikuwalemekeza pamwamba pa mitundu ina (ya nthawiyo).

(17) “Ndipo tidawapatsa zisonyezo zoonekera pazinthu zachipembedzo chawo; sadapatukane mpaka pomwe kudawadzera kudziwa, chifukwa chadumbo pakati pawo. Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsemphana.

(18) “Kenako tidakuika iwe pa malamulo a zinthu za chipembedzo (Chathu). Choncho tsatira malamulo (Athu), ndipo usatsate zilakolako za amene sadziwa (njira yoona).

(19) “Ndithu iwo (amene akutsata njira zonama) sangakuthandize chilichonse kwa Allah; ndithu achinyengo ena a iwo amatetezana wina ndi nzake; koma Allah ndi Mtetezi wa oopa (Iye potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa).

(20) “Iyi (Qur’an imene yavumbulutsidwa kwa iwe), ndizisonyezo kwa anthu chiongoko ndi chifundo kwa anthu omwe akutsimikiza (kuti lilipo tsiku la chiweruziro).

(21) “Kodi amene adadzichitira zoipa akuganiza kuti tingawachite monga omwe adakhulupirira ndi kuchita zabwino kuti afanane pa moyo wawo ndi pa imfa yawo? Ndi kuweruza koipa kumene iwo akuweruza.

(22) “Ndipo Allah adalenga thambo ndi nthaka moona ndi kuti mzimu uliwonse ulipidwe zimene udadzichitira, (zoipa kapena zabwino) ndipo iwo sadzaponderezedwa.

(23) “Kodi wamuona amene wachichita chilakolako chake kukhala mulungu wake wompembedza? Ndipo Allah wamlekelera kuti asokere, kupyolera mkudziwa Kwake; ndipo wamdinda (chidindo) mmakutu mwake ndi mu mtima mwake ndi kumuika chivindikiro mmaso mwake. Choncho ndani angamuongole pambuyo pa Allah? Kodi simukumbukira?

(24) “Ndipo (okanira kuuka ku imfa) adanena: “Kulibe (moyo wina) koma moyo wathu womwewu wa padziko lapansi; timafa ndi kukhala ndi moyo; palibe chikutiononga koma nthawi basi.” Koma iwo alibe kudziwa pa zimene akunenazo; akungoganizira chabe.

(25) “Ndipo Ayah Zathu zikawerengcdwa kwa iwo zolongosola chilichonse momveka, alibe mtsutso wina koma kunena kuti: “Tibweretsereni makolo Athu (aukitseni akhale ndi moyo) ngati inu muli owona!”

(26) “Nena (kwa iwo iwe Mtumiki): “Allah amakupatsani moyo. Kenako amakupatsani imfa. Kenako adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko.” Koma anthu ambiri sakudziwa.

(27) “Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah, ndipo tsiku limene Qiyâma idzachitika, (anthu) ogwirizana ndi zonama adzaonongeka patsikulo.

(28) “Ndipo udzaliona gulu lililonse litagwada (uku nkhope zili zyoli); gulu lililonse lidzaitanidwa ku kaundula wake (kukamuwerenga): “Lero mulipidwa zimene mudali kuchita!”

(29) ““Uyu kaundula Wathu akunena zoona za inu; ndithu Ife tidali kulemba zimene mudali kuchita.”

(30) “Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, Mbuye wawo adzawalowetsa ku chifundo Chake; kumeneko ndiko kupambana koonekera.

(31) “Ndipo amene adakanira, (adzauzidwa kuti): “Kodi Ayah Zanga sizidali kuwerengedwa kwa inu? Koma inu mudadzikweza; ndipo mudali anthu oipa.”

(32) “Ndipo kukanenedwa kuti lonjezo la Allah ndiloona, ndikuti Qiyâma ilibe chikaiko, mudali kunena: “Sitikudziwa Qiyâma kuti nchiyani; tikungoganizira chabe, ndipo tilibe chitsimikizo (cha Kiyamayo).”

(33) “Choncho, kuipa kwa zimene adachita kudzawaonekera, ndipo zidzawazinga zimene ankazichitira chipongwe.

(34) “Kudzanenedwanso kwa iwowa: “Lero tikuiwalani (pokusiyani mchilango) monga momwe inu mudaiwalira kukumana ndi tsiku lanu ili. Ndipo malo anu ndi ku Moto, ndipo mulibe wokupulumutsani.”

(35) ““Zimenezi nchifukwa chakuti inu mudazichitira chipongwe Ayah za Allah, ndipo moyo wa pa dziko udakunyengani.” Choncho lero satulutsidwa mmenemo ndipo madandaulo awo savomerezedwa.

(36) “Tero kutamandidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wakumwamba ndi Mbuye wa pa dziko lapansi; Mbuye wazolengedwa.

(37) “Ndipo ukulu ndi Wake, kumwamba ndi pansi; ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya!