58 - Al-Mujaadila ()

|

(1) “۞ Ndithu Allah wamva mawu a (mkazi) amene akubwezeranabwezerana nawe (mawu) pa za mwamuna wake (amene adamsala); ndipo akusuma kwa Allah. Ndipo Allah akumva kukambirana kwanu; ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya (chilichonse).
Apa akutiuza kuti titsanzire zimene adachita tate wa Shariya amene ndi Ibrahima pamodzi ndi omtsatira ake pamene adadzipatula kwa makolo awo ndi abale awo omwe adali m’chipembedzo chonama. Msilamu amkonde Allah kuposa tate wake, ana ake, mkazi wake, chuma chake ndi thupi lake limene. Atsogoze zofuna za Allah asanachite china chilichonse. Akatero akhala kuti wakhulupilira Allah mwachoonadi.

(2) “Amene akufanizira mwa inu (Asilamu) akazi awo (ndi amayi awo) iwo siamayi awo; amayi awo ndiamene adawabereka. Ndithu iwo akunena mawu oipa ndi onama. Koma ndithu Allah ali Wofafaniza (machimo) ndi Wokhululuka (kwa amene walapa).

(3) “Ndipo amene akuwafanizira akazi awo (ndi amayi awo) kenako nkubweza zimene adanena, apereke ufulu kwa kapolo asanakhale malo amodzi (ndi mkaziyo). Amenewa ndi malamulo a Allah kwa inu (amene) mukuchenjezedwa nawo. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita (zoonekera poyera ndi zosaonekera choncho sungani malamulo amene Allah wakhazikitsa pa inu).

(4) “Ndipo amene sadapeze (kapolo) asale miyezi iwiri yondondozana asadakhalirane pamodzi (ndi mkaziyo), koma amene sadathe kusala adyetse masikini makumi asanu ndi limodzi (60). Izi (zalamulidwa) kuti mukhulupirire mwa Allah ndi Mthenga Wake. Amenewo ndiwo malire a Allah; (malamulo okhazikitsidwa ndi Allah choncho musawalumphe). Ndipo chilango chopweteka chili pa osakhulupirira.

(5) “Ndithu amene akutsutsana ndi Allah kudzanso Mthenga Wake, ayalutsidwa monga momwe adayalutsidwira amene adalipo patsogolo pawo; ndithu tavumbulutsa Ayah zolongosola, momveka (pa zololedwa ndi zoletsedwa). Ndipo chilango choyalutsa chili pa osakhulupirira.

(6) “(Kumbuka) tsiku limene Allah adzaukitsa akufa onse ndi kuwafotokozera zimene adachita (pa moyo wa dziko lapansi: zoipa ndi zabwino); Allah adazisunga mozilemba koma iwo adaziiwala. Ndipo Allah ndi mboni wa zonse (palibe chingabisike kwa Iye).

(7) “Kodi sukudziwa (iwe, womvera wanzeru) kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zam’dziko lapansi? Sipakhala manong’onong’o a (anthu) atatu koma Iye Ngwachinayi wawo (ndi kudziwa kwake kosabisika chilichonse cha kumwamba ndi m’dziko), ngakhale a (anthu) asanu koma Iye Ngwachisanu ndi chimodzi wawo (mkudziwa Kwake), ngakhale ali ochepera kuposera pamenepa kapena ochulukira koma Iye ali nawo paliponse pomwe ati akhale (Allah ali nawo pamodzi mukudziwa Kwake kosabisika chilichonse), kenako adzawafotokozera pa tsiku la chiweruziro zimene adachita; ndithu Allah Ngodziwa chilichonse (mokwanira).
Allah sakutiletsa kuwachitira zabwino anthu amene sali Asilamu, mmalo mwake akutilamula kuti tiwachitire zabwino ngati alibe upandu uliwonse ndi Asilamu.

(8) “Kodi siudaone! Kwa amene aletsedwa kunong’onezana zoipa pakati pawo, kenako akubwereza zimene adaletsedwa? Akunong’onezana za machimo, mtopola ndi kunyoza Mtumiki. Akakudzera akukulonjera (ndi malonje achinyengo) amene Allah sadakulonjerepo nawo ndipo akunena m’mitima mwawo: “Kodi nchifukwa chiyani Allah sakutilanga ndi mawu tikunenawa (ngati iyeyu ndi Mtumikidi wa Allah?” Jahannam ikuwakwanira: adzailowa. Ndipo taonani kuipa malo (awo) wobwerera!

(9) “E inu amene mwakhulupirira! Ngati mukunong’onezana, musamanong’onezane za machimo ndi mtopola ndi kunyoza Mtumiki; koma nong’onezanani za kulungama ndi kuopa Allah ndipo muopeni Allah, kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwe (ndi kuweruzidwa).
(Ndime 2-3) Khalidwe la munthu limene limakwiyitsa Allah kwambiri ndiko kunena zokoma chikhalirecho zochita zili zoipa. Amawanyenga anthu ndi mawu otsekemera koma zochita zake ndizachinyengo zokhazokha. Munthu wa makhalidwe otere, malipiro ake ndi kulowa ku nthukutira ya Moto. Choncho zochita zanu zifanane ndi zimene mukuyankhula. Apeweni makhalidwe achiphamaso.

(10) “Ndithu manong’onong’o oipa amachokera kwa satana kuti adandaulitse amene akhulupirira; koma sangawapweteke nawo chilichonse kupatula Allah atafuna ndipo okhulupirira atsamire kwa Allah Yekha, (asalabadire zonong’onezana zawo).

(11) “E inu amene mwakhulupirira! Kukapemphedwa kwa inu kuti perekani malo pabwalo (pokhala), perekani malowo (kuti anzanu apeze pokhala; mukatero) Allah akuphanulirani (chifundo Chake pano pa dziko ndi kumwamba). Ndipo kukanenedwa kuti imilirani, muimilire (musanyozere, apatseni ena malo); Allah awakwezera (ulemelero) mwa inu amene akhulupirira ndi amene apatsidwa nzeru. Ndipo Allah akudziwa bwino zimene mukuchita.
Allah akufuna kuti Asilamu akhale dzanja limodzi pofalitsa Chisilamu, agwire ntchito yokomera gulu lonse mothangatana.

(12) 12 . E inu amene mwakhulupirira! Mukafuna kuyankhula ndi Mtumiki (s.a.w) tsogozani pa zoyankhula zanuzo, sadaka: kutero ndibwino kwa inu ndiponso ndichoyeretsa (mitima yanu). Koma ngati simudapeze (sadakayo) ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni.

(13) “Kodi mwaopa kutsogoza sadaka pakunena naye (Mtumiki)? Ngati simudachite zimenezi basi Allah wakukhululukirani; choncho pempherani Swala moyenera ndipo perekani Zakaat ndiponso mverani Allah pamodzi ndi Mtumiki Wake. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.

(14) “Kodi sukuwaona amene apalana ubwenzi ndi anthu amene Allah wawakwiira; iwo sali mwa inu ndiponso sali mwa iwo. Ndipo akulumbira zabodza uku akudziwa (kuti limeneli ndibodza).

(15) “Allah wawakonzera chilango chaukali, ndithudi nzoipa zimene amachita.

(16) “Kulumbira kwawo adakuchita kukhala chodzitetezera (iwo, ana awo ndi chuma chawo); choncho adatsekereza (anthu) ku njira ya Allah; choncho chilango choyalutsa chili pa iwo.
(Ndime 8-9) Allah akulonjeza kuti Chisilamu chidzapambana zipembedzo zonse ngakhale osakhulupilira akuchithira nkhondo.

(17) “Chuma chawo, ngakhale ana awo, sizidzawathandiza konse ku chilango cha Allah. Iwowo ndi anthu a ku Moto m’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali.

(18) “(Alikumbukire) tsiku limene Allah adzawaukitsa (ku imfa) onse, adzayamba kulumbira kwa Iye (zabodza) monga akulumbira (zabodza) kwa inu. Ndipo akuganiza kuti apezapo kanthu (pakulumbira kwawo). Dziwani, ndithudi, iwo ndi abodza.

(19) “Satana wawapambana ndipo wawaiwalitsa kukumbukira Allah. Iwowa ndiachipani cha satana. Dziwani kuti chipani cha satana nchotayika, (choonongeka).

(20) “Ndithudi amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, iwowo adzakhala m’gulu la onyozeka.

(21) “Allah adalamula (kuti): “Ndithu ndipambana Ine ndi atumiki Anga.” Ndithu Allah ndiwanyonga zokwana, Wopambana (sapambanidwa ndi aliyense).

(22) “Supeza anthu okhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro akukonda amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, ngakhale atakhala atate awo, ana awo abale awo ndi akumtundu wawo; kwa iwo (Allah) wazika chikhulupiliro (champhamvu) m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi mphamvu zochokera kwa Iye. Ndipo adzawalowetsa m’minda yomwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Allah adzakondwera nawo ndipo (iwonso) adzakondwera Naye. Iwowa ndi chipani cha Allah. Dziwani kuti chipani cha Allah ndichopambana.
Arabu amatchedwa “Ummiyyuna” chifukwa chakuti samadziwa kulemba ndi kuwerenga. Kusadziwa kulemba ndi kuwerenga kudafala pakati pawo ndipo ngakhale Mtumiki amene samadziwa kulemba ndi kuwerenga chilichonse. M’ndime imeneyi, Allah akutiphunzitsa kuti adampereka Muhammad (s.a.w) kuti awaongolere anthu ku njira yoongoka. Iyeyu adaperekedwa panyengo imene anthu adali ndi khumbo la Mneneri wa Allah kuti awatsogolere ku njira yolungama pakuti pa nthawiyo zipembedzo zonse za Allah zidali zitaonongeka. Pachiyambi Arabu amatsatira chipembedzo cha Ibrahim. Kenako adasintha nkuyamba kupembedza mafano. Adayambitsa zinthu zambiri zosalolezedwa ndi Allah. Ndipo nawonso anthu amabuku, Ayuda ndi Akhrisitu, adasintha zophunzitsa za mabuku awo. Choncho Allah adapereka Muhammad (s.a.w) ndi malamulo aakulu okwanira bwino. Mkati mwake mudali chilichonse chofunika m’moyo wa anthu pa nyengo zosiyanasiyana pa moyo wa pa dziko ndi wa pa tsiku lachimaliziro. Allah adampatsa zabwino zomwe sadampatseponso wina aliyense, woyamba ndi womaliza.