(1) Ndikulumbilira tsiku lachimaliziro.
(2) Ndikulumbiliranso mzimu wodzidzudzula (pa cholakwa chimene wachita. Ndithu mudzaukitsidwa; mafupa anu omwazikana atasonkhanitsidwa.)
(3) Kodi munthu akuganiza kuti Ife (Amene tidamlenga kuchokera popanda chilichonse) sitidzatha kusonkhanitsa mafupa ake (ofumbwa)?
(4) Iyayi, Ife tikhoza (kutisonkhanitsa) ndi kutilongosola bwino timizere takunsonga kwa zala zake. (Mafupa ake ndiye osanena)!
(5) Koma munthu akufuna kuti apitirize kuchimwa (mmasiku akudza) mtsogolo mwake.
(6) Akufunsa (mwa chipongwe): “Kodi lidzakhala liti tsiku la chimaliziro?”
(7) Pamene maso adzangoti tong’oo (ndi mantha),
(8) Ndi kuchoka kuwala kwa mwezi,
(9) Ndipo dzuwa ndi mwezi ndikusonkhanitsidwa.
(10) Munthu adzanena tsiku limenelo: “Nkuti kothawira (chilangochi?)”
(11) (Adzauzidwa): “Iyayi, (iwe munthu) palibe pothawira (pako)!”
(12) Tsiku limenelo kobwerera (anthu) ndi kwa Mbuye wako basi.
(13) Tsiku limenelo munthu adzauzidwa zochita zake zimene adazitsogoza ndi zimene adazichedwetsa.
(14) Koma munthu adzadzichitira umboni yekha pa mzimu wake.
(15) Ngakhale atapereka madandaulo ake (otani kuti apulumuke nawo sadzapulumuka).
(16) Usaigwedezere (Qur’an) lirime lako (pamene ikuvumbulutsidwa) kuti uifulumilire (kuiwerenga ndi kuisunga mu mtima).
(17) Ndithu ndiudindo wathu kuisonkhanitsa (mu mtima mwako) ndi kukhazikitsa kawerengedwe kake (palirime lako).
(18) Choncho pamene tikukuwerengera iwe tsatira kuwerenga kwakeko (uku uli chete).
(19) Kenako, ndithu ndiudindo Wathu kulongosola (zimene siukumvetsa),
(20) Iyayi koma mukukonda moyo wa pa dziko.
(21) Ndipo mukusiya moyo wa tsiku lachimaliziro.
(22) Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zowala,
(23) Zili kumuyang’ana Mbuye wawo.
(24) Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zoziya (zokhwinyata).
(25) Zikuyembekezeka kuti zilandira tsoka lodula msana.
(26) Sichoncho! Pamene mzimu udzafika pa nthitimtima, (pomwe pakumana mafupa am’mapewa).
(27) Ndipo ndikunenedwa ndani angamchiritse!
(28) Ndipo (iye mwini wake), nkutsimikiza kuti ndithu uku ndikusiyana (ndi dziko lapansi),
(29) Ndipo miyendo idzasanjikizana; (iyi ndi nthawi yochoka mzimu).
(30) Tsiku limenelo koperekedwa (anthu onse) nkwa Mbuye wako.
(31) Ndipo sadakhulupirire komanso sadapemphere Swala (zisanu),
(32) Koma (m’malo mwake) adatsutsa ndi kunyoza.
(33) Kenaka adapita kubanja lake (uku akuyenda) monyada.
(34) Kuonongeka nkwako (iwe wotsutsa)! Kuonongeka zedi!
(35) Ndiponso kuonongeka nkwako! kuonongeka zedi!
(36) Kodi munthu akuganiza kuti angosiidwa chabe? (Sadzaweruzidwa)?
(37) Kodi sadali dontho la umuna umene udafwamphukira (m’chiberekero)?
(38) Kenako adakhala nthinthi (ntchintchi) ya magazi, ndipo adamlenga ndi kumlinganiza (monga munthu).
(39) Ndipo adalenga kuchokera mmenemo mitundu iwiri: mwamuna ndi mkazi.
(40) Kodi (Iye amene adayambitsa chilengedwe choyambachi) sangathe kuwapatsa moyo akufa?