78 - An-Naba ()

|

(1) “۞ Kodi akufunsana zachiyani?

(2) “Za nkhani yayikulu ija.

(3) “Imene iwo akusiyana (maganizo).
Tanthauzo lake ndikuti: “Kodi chilengedwe chanu nchovuta kwambiri kuposa chilengedwe cha thambo pamene inu mukuganiza kuti Allah sangathe kukudzutsani pambuyo pa imfa?”

(4) “Aleke (zimenezo) adzadziwa posachedwapa.
Mu Ayah iyi Allah akusonyeza kuti Iye ndi Mwini mphamvu zonse zochitira chinthu chilichonse chachikulu kuposa kuwaukitsa akufa; ndiponso akukumbutsa ufulu Wake waukulu womwe adatichitira potipatsa zinthu zonsezo kuti tithandizike nazo.

(5) “Ayi, ndithu aleke (zimenezo); posachedwapa adzadziwa zoona zake (pamene chilango chidzawatsikira).
Apa tanthauzo lake ndikuti adzaona masiku onse amene adakhala m’dziko ngati lidali ola limodzi.

(6) “Kodi sitidachite nthaka kukhala ngati choyala?
Tsiku lina Mneneri (s.a.w) atakhala ndi akuluakulu a Aquraishi. Adali kuwalalikira za chipembedzo mwachidwi, ndipo adali kuyembekezera kuti akavomereza Chisilamu iwo, ndiye kuti anthu owatsatira naonso avomereza. Chifukwa anthu ambiri sadalowe Chisilamu poopa atsogoleri awo. Pa nthawi imeneyi adatulukira wakhungu wina yemwe ankatchedwa Ibn Ummu Maktum. Sadadziwe kuti Mneneri (s.a.w) ali wotanganidwa. Adamukuwira: “E Iwe Mneneri wa Allah! Ndiphunzitse inenso zimene wakuphunzitsa Allah.” Ndipo ankangomubwerezera-bwerezera mawu amenewa. Mneneri (s.a.w) pakuti adali ndi chidwi ndi kulalikira akuluakulu aja, adamchitira tsinya wakhungu uja chifukwa chomuonongera ntchito yake; sadamumvere. Basi pamenepa Allah akumdzudzula Mneneri Wake pa zomwe adachita posiya kumumvera amene adamubwerera kudzafuna chiongoko.

(7) “Ndi mapiri ngati zichiri (zolimbitsa nthaka)?

(8) “Ndipo takulengani mitundu iwiri (amuna ndi akazi).

(9) “Ndipo tidachita tulo tanu kukhala mpumulo (ku mavuto a ntchito).

(10) “Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake).

(11) “Ndipo tapanga masana kukhala nthawi yopezera zofunika pa moyo;

(12) “Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba;

(13) “Ndipo tidapanga nyali yowala ndi yotentha kwambiri (dzuwa);

(14) “Ndipo tawatsitsa madzi otsika mwamphamvu kuchokera ku mitambo, ya mvula;

(15) “Kuti titulutse ndi madziwo mbewu ndi m’mera, (chomwe ndi chakudya cha anthu ndi nyama).

(16) “Ndi minda yothothana nthambi za mitengo.

(17) “Ndithu tsiku la chiweruziro ndinthawi imene idakhazikitsidwa kale.

(18) “Tsiku limene lipenga (lakuuka) lidzaimbidwa ndipo inu mudzabwera (kubwalo losonkhanirana) muli magulumagulu.

(19) “Ndipo thambo lidzatsegulidwa (mbali zonse): choncho lidzakhala makomomakomo.

(20) “Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake, adzakhala ngati zideruderu.
(Ndime 11-16) Apa Allah akumuletsa Mtumiki Wake kuti asachitenso zonga adachitazo ndi kumuuza kuti Qur’an ndi ulaliki chabe, amene afuna kulingalira za ulalikiwo, umuthandiza, ndipo amene safuna, kutaika ndi kwake. Ndiponso adamufotokozera kuti Qur’an idachokera m’mabuku olemekezeka; idachokera ku “Lauhil-Mahfudh” mabuku omwe ali m’manja mwa Angelo olemba, olemekezeka, ochita zabwino omwe ndi abwino kuposa Aquraishi.

(21) “Ndithu moto wa Jahannam ukuwadikilira (oipa).

(22) “Mbuto ya opyola malire.
Ngati munthu sakumbuka chilengedwe chake, ayang’ane chakudya chimene akudya momwe chimapezekera. Azindikira mphamvu za Allah.

(23) “Adzakhala m’menemo muyaya.

(24) “Sadzalawa m’menemo kuzizira (kowachotsera kutentha), kapena chakumwa (chowachotsera ludzu lawo);

(25) “Kupatula madzi otentha kwambiri ndi mafinya (otuluka mmatupi a anthu a ku Moto);

(26) “Kukhala malipiro olingana ndi ntchito zawo.

(27) “Ndithu iwo sadali kuyembekezera chiwerengero (cha Allah);

(28) “Adatsutsa zizindikiro Zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi mtsutso waukulu.

(29) “Ndipo chinthu chilichonse tachisunga mochilemba.

(30) “Basi, lawani (lero chilango Changa); sitikuonjezerani chinthu china koma chilango pamwamba pa chilango.

(31) “Ndithu anthu oopa Allah adzakhala ndi malo wopambana.

(32) “Minda ndi zipatso za mphesa.

(33) “Ndi mabuthu (anamwali) ofanana misinkhu.

(34) “Ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa.

(35) “Sakamva m’menemo mawu opanda pake kapena bodza.

(36) “Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye wako zopereka zokwanira.
(Ndime 38-39) Tsiku limenelo anthu adzakhala kakhalidwe ka mitundu iwiri: amene adakhulupilira ndi kuchita ntchito zabwino nkhope zawo zidzawala ndi chimwemwe, ndipo amene adakanira ndikumachita zoipa, nkhope zawo zidzakhala zafumbi ndi zakuda monga momwe anenera ma Ayah 40 ndi 42.

(37) “Mbuye wa kumwamba ndi pansi ndi zimene zili pakati pake; Wachifundo chambiri. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu yolankhulana naye (pa tsiku limenero);

(38) “Tsiku limene adzaima Jibril ndi angelo pa mzere (ali odzichepetsa); sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi (Allah) Wachifundo chambiri (kuyankhula) ndipo adzanena zolondola.

(39) “Limenelo ndi tsiku loona, (lopanda chikaiko); choncho amene akufuna adzipezere malo (njira yonkera) kwa Mbuye wake. (Pomugonjera Iye pa moyo uno wadziko lapansi).

(40) “Ndithu tikukuchenjezani zachilango chomwe chili pafupi kudza; tsiku limene munthu adzayang’ana zimene adatsogoza manja ake, ndipo wosakhulupirira adzanena: Kalanga ine! Ndikadakhala dothi, (kuti ndisalangidwe chilango chikundiyembekezachi).