79 - An-Naazi'aat ()

|

(1) “Ndikulumbilira (angelo) amene amazula mwamphamvu (mizimu ya osakhulupirira).
Surah zambiri zimene zidavumbulutsidwa ku Makka zimanena zododometsa za tsiku lachimaliziro.

(2) “Ndikulumbiliranso (angelo) amene amachotsa moleza (mizimu ya okhulupirira).

(3) “Ndi omwe amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (ponka nayo ku malo ake oyembekezera).

(4) “Ndi iwo amene akupikisana pokwaniritsa malamulo a Allah.

(5) “Ndi iwo (angelo) amene akulongosola malamulo (Ake). (Ndithudi inu anthu mudzauka kwa akufa).

(6) “Patsiku lomwe (lipenga loyamba lidzaimbidwa), dziko lapansi ndi mapiri ake zidzagwedezeka (ndipo aliyense adzafa).

(7) “Ndipo kudzatsatira kuyimba kwa lipenga lachiwiri (kumene kudzaukitsa akufa onse).

(8) “Tsiku limenelo mitima idzanjenjemera ndi kuopa.

(9) “Maso a eni mitimayo adzakhala ozyolika (chifukwa chamadandaulo);

(10) (Osakhulupirira) akunena: “Kodi nzoona tidzabwezedwa pambuyo pa imfa monga tidalili kale?”

(11) ““Pomwe ife titakhala mafupa ofumbwa (tingabwezedwe ndi kuukitsidwa mwa tsopano)?”

(12) “Adanena (mokanira ndi mwachipongwe): “Choncho kubwerera kumeneko ngati kudzakhalepodi kudzakhala kotaika (ndi kopanda phindu kwa ife. Pomwe ife sindife oyenera kutaika).”

(13) “(Musaganize kubwererako nchinthu chovuta). Ndithundithu Kiyamayo ndi nkuwo umodzi.

(14) “Mwadzidzidzi (zolengedwa zonse) zidzangoona zili pa dziko latsopano (zili zamoyo).

(15) “Kodi yakufika (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Mûsa?
Tsiku limenelo mapiri adzakhala osalimba ngati thonje limene likungouluka ndi mphepo.

(16) “Pamene Mbuye wake adamuitana pa chigwa choyera (chotchedwa) Tuwaa.

(17) “(Adamuuza kuti) pita kwa Farawo ndithu iye wapyola malire, (mkudzitukumula kwake ndikupondereza anthu).

(18) “Choncho ukamuuze kuti: “Kodi ukufuna kudziyeretsa?”

(19) ““Ndikuti ndikuongolere kwa Mbuye wako kuti uzimuopa?”

(20) “(Basi Mûsa) adamuonetsa (Farawo) chozizwitsa chachikulu.

(21) “Koma (Farawo) adatsutsa (Mûsa pazimene adadza nazo zija) ndi kunyoza.

(22) “Kenaka adabwerera uku akulimbika kutsutsana naye (Allah),

(23) “Adawasonkhanitsa (afiti) uku akuitana anthu;

(24) “Nanena: “Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba!”

(25) “Pamenepo Allah adamulanga chifukwa cha mawu ake omaliza ndi oyamba.

(26) “Ndithu pa zimenezi pali phunziro (lalikulu) kwa yemwe akuopa Allah.

(27) “Kodi kulengedwa kwanu, (inu osakhulupirira kuti muuke) nkovuta kapena thambo limene adalimanga (posonkhanitsa mbali zake zosiyanasiyana ndikukhala chinthu chimodzi)?
Ngamira za bere ndi chuma cha mtengo wapatali kwa Aarabu. Akuuzidwa apa kuti tsiku limenelo adzazisiya osazilabadira konse.

(28) “Adatukula nsinkhu wake ndikulikonza bwino (popanda pena pong’ambika kapena posiyana ndi pena).

(29) “Ndipo amauvindikira usiku wake ndi mdima ndipo amatulutsa kuwala wake.

(30) “Ndipo pambuyo pazimenezo, nthaka adaiyala (kuti ikhale yoyenera kuikhala).

(31) “Adatulutsa m’menemo madzi ake (potulutsa akasupe) ndikumeretsa msipu wake;

(32) “Ndipo mapiri adawakhazikitsa (ndikuwalimbika);

(33) “(Adachita zonsezi) chifukwa chokusangalatsani inu ndi ziweto zanu.
Mwa zina zododometsa pa tsiku limenelo ndi nyama za mtchire kusonkhanitsidwa pamodzi popanda kumenyana kapena kudyana.

(34) “Choncho likadzafika tsoka lalikulu (tsiku la Qiyâma).

(35) “Tsiku limenelo munthu adzakumbukira zimene adachita, (zabwino ndi zoipa).

(36) “Ndipo Moto waukali udzawonetsedwa kwa yense openya.

(37) “Tsono amene adapyola malire (pochita machimo),

(38) “Ndikudzisankhira (yekha) moyo wa pa dziko lapansi,

(39) “Ndithu Jahannam ndiwo malo ake.

(40) “Tsono amene akuopa kuti adzaimilira pamaso pa Mbuye wake, nauletsa mtima wake ku zilakolako zoipa,

(41) “Ndithu Munda wamtendere ndiwo adzakhale malo ake.

(42) “Akukufunsa (iwe Mtumiki) (s.a.w) za nthawi (ya tsiku lachimaliziro kuti): “Idzakhala liti?”

(43) “Uli ndi mphamvu yanji iwe yofotokozera za tsikulo? (Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo kotero kuti ungaitchule kwa iwo).

(44) “Kwa Mbuye wako ndiko kuli mathero ake.

(45) “Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuiopa; (osati kulengeza zanthawi yake).

(46) “Tsiku limene adzaiona adzakhala ngati sadakhale (pa dziko nthawi yayitali), koma ngati madzulo amodzi kapena masana ake (nthawi ya m’mawa).
(Ndime 8-9) Ma Ayah awiriwa akufotokoza momwe Aarabu adalili Usilamu usadabwere. Munthu ankati akapatsidwa mphatso ya mwana wa mkazi adali kukhumudwa ndi kudandaula kwambiri. Ankanena kuti asungwana ngopanda phindu ndipo kuti kudali kuononga zinthu pakumulera, kumudyetsa, ndi kumuveka. Ndipo akadzakhala wachiwerewere adzakhala manyazi aakulu kwa makolo ake. Pamene chidadza chisilamu chidathetsa mkhalidwewu. Ndipo apa Allah akutisonyeza kuti patsiku limenelo, la chiweruziro, mwana uja adaikidwa wa moyo, adzafunsidwa kuti adaphedwa ndi tchimo lanji. Iye adzayankha kuti sadachite tchimo lililonse koma adaphedwa mopanda chilungamo.