88 - Al-Ghaashiya ()

|

(1) “Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)?

(2) “Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka,
Apa ndikuti Allah akuwaona anthu Ake nthawi ili yonse. Palibe chimene iwo achita popanda Iye kuchiona ndi kuchilemba.

(3) “Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri.

(4) “Zikalowa ku Moto wotentha kwambiri.

(5) “Zikamwetsedwa mu kasupe wotentha kwabasi.

(6) “Sadzakhala ndichakudya koma minga.

(7) “Yosanenepetsa (thupi) ndiponso yosathetsa njala.

(8) “Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala.

(9) “Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi).
Arabu asadalowe m’Chisilamu akazi sadali kugawiridwa chuma cha masiye kudzanso ana aang’onoang’ono a masiye sadali kuchiona chumacho.

(10) “M’minda ya pamwamba (Jannah).

(11) “Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula).

(12) “Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola).
(Ndime 25-26) Tanthauzo lake ndikuti palibe chofanizira chilango cha Allah chomwe chidzaperekedwe kwa akafiri ndiponso ndi kunjata komwe akafiri adzanjatidwe.

(13) “Mmenemo muli makama a pamwamba,

(14) “Ndi zikho zoikidwa bwino (pamaso pawo),

(15) “Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere

(16) “Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse.

(17) “Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani?
“Mzimu wokhazikika” ndi mzimu wa munthu wokhulupilira amene akuchita zomwe walamulidwa ndi kusiya zimene waletsedwa. Umenewo ndiwo mzimu umene udzakhale wodekha pa tsiku lachimaliziro chifukwa chakuti pa tsikulo sudzakhala ndi mantha kapena kudandaula.

(18) “Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)?

(19) “Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)?

(20) “Ndi nthaka momwe idayalidwira.

(21) “Basi, kumbutsa (anthu) ndithu iwe, ndiwe mkumbutsi.

(22) “Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire).
Tanthauzo lake nkuti mzimu wokhazikika udzakondwera ndi zimene udzalandira kwa Allah tsiku limenelo ndipo naye Allah adzakondwera nawo.

(23) “Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako),

(24) “Allah amulanga chilango chachikulu zedi.

(25) “Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi.

(26) “Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife.